Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 8/15 tsamba 31
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Wosindikiza Amene Anasiya Chizindikiro Chake
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Nkufuniranji Choonadi?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Akristu Amalambira Mumzimu ndi M’choonadi
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Choonadi cha Chipembedzo Chingapezeke?
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 8/15 tsamba 31

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwakondwa kuŵerenga makope a Nsanja ya Olonda a posachedwapa? Ngati mwatero, mudzasangalala kukumbukira zotsatirazi:

▫ Kodi choonadi cha chipembedzo chingapezeke?

Yesu Kristu ananena kuti: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Yesu sanangosonyeza kuti choonadi chikhoza kupezeka komanso kuti kuchipeza nkofunika ngati tifuna kuti kulambira kwathu Mulungu akulandire. Anauza mkazi Wachisamariya kuti: “Olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:23)​—4/15, tsamba 5.

▫ Kodi Robert Estienne anali yani, ndipo anasiya motani chizindikiro chake?

Robert Estienne anali wosindikiza wokhalako m’zaka za zana la 16. Anapereka moyo wake pa kufalitsa Malemba Oyera ndipo anayesetsa kuika mawu a m’Baibulo monga momwe analembedwera poyamba. Njira yake yogaŵira malemba a Baibulo m’mavesi ndiyo imene ikugwiritsiridwa ntchito kwambiri lerolino.​—4/15, masamba 10, 14.

▫ Kodi timapindula motani ndi kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku?

Malemba nthaŵi zonse amakhala ndi tanthauzo latsopano kwa ife, ndipo maulosi a masiku otsiriza amakhomerezeka kwambiri m’maganizo mwathu chifukwa cha zimene taona, kumva, ndi zimene zatichitikira. Pamene chidziŵitso chathu m’moyo chikula ndipo pamene tilimbana ndi mavuto, timayamikira kwambiri uphungu wa Baibulo. (Miyambo 4:18)​—5/1, tsamba 15.

▫ Kodi mungakumbukire motani malemba a Baibulo?

Pamene mukuŵerenga Baibulo, chongani malemba osankhidwa amene mufuna kuwakumbukira, kapena akopeni pamakadi ndi kuika makadiwo pamene mukhoza kumawaona tsiku ndi tsiku. Poyesa kuloŵeza mavesiwo pamtima, asinkhesinkheni ndi kuwagwiritsira ntchito. Musayese kuloŵeza ochulukitsa nthaŵi imodzi, mwinamwake limodzi kapena aŵiri mlungu uliwonse.​—5/1, masamba 16, 17.

▫ Kodi ndi chidziŵitso chotani chimene Uthenga Wabwino wa Luka uli nacho kuwonjezera pa chimene alembi ena a Mauthenga Abwino anapereka?

Pamene kuli kwakuti mbali yaikulu yolembedwa ndi Luka ili yofanana ndi nkhani ya Mateyu, 59 peresenti njosiyana. Luka analemba za zozizwitsa zisanu ndi chimodzi zopezeka m’buku lake lokha ndipo anasimba mafanizo a Yesu osasimbidwa ndi alembi ena a Mauthenga Abwino kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengerocho.​—5/15, tsamba 12.

▫ Kodi kuŵala kwapadera kwa kuunika kwa choonadi kumene kunavumbuluka mu 1935 kunali kotani?

Chaka chimenecho anthu a Yehova anamvetsa kuti khamu lalikulu lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9, 14 silinali kunena za gulu lachiŵiri lakumwamba koma aja amene ali ndi ziyembekezo za pa dziko lapansi. (Yohane 10:16)​—5/15, tsamba 20.

▫ Kodi ndi njira zothandiza zotani zimene tingatonthoze nazo ofedwa?

Mvetserani. Perekani chitsimikiziro. Khalani wopezeka. Yambani ndinu kuchitapo kanthu pamene kuli koyenera. Lembani kalata kapena tumizani khadi lotonthoza. Pempherani nawo. (Yakobo 5:16) Pitirizani kuwathandiza.​—6/1, masamba 13, 14.

▫ Kodi abale ndi alongo auzimu angachitenji kuthandiza aja okhala m’mabanja a zipembedzo zosiyana kuti apirire?

Nthaŵi zonse lankhulani nawo ndi mawu olimbikitsa, abwino, ndi otonthoza. (1 Atesalonika 5:14) Zimenezi zimakhala zotsitsimula maganizo ndi matupi awo. Ngati kutheka ndipo nkoyenera, aphatikizeni m’zochita zanu zateokrase ndi m’macheza. Atchuleni m’mapemphero anu. (Aroma 1:9; Aefeso 1:16)​—6/1, tsamba 29.

▫ Kodi kuleza mtima pamene tili mu utumiki wakumunda kuli ndi mfupo zotani?

Kuleza mtima kumathandiza wofalitsa Ufumu kupirira mphwayi kapena chitsutso chilichonse. M’malo mwa kutsutsana ndi eni nyumba okwiya, atumiki oleza mtima adzakhoza kuyankha mofatsa kapena kuchoka mwakachetechete, motero akumasunga mtendere ndi chimwemwe. (Mateyu 10:12, 13) Ndiponso, onga nkhosa adzakopeka ndi uthenga wa Ufumu.​—6/15, tsamba 12.

▫ Kodi nchifukwa ninji kudziŵa choonadi cha Baibulo kuli kofunika koposa?

Kudziŵa choonadi kumatimasula ku mabodza, zinyengo, ndi miyambo. Pamene titsatira choonadi, chimatilimbikitsa kupirira zovuta ndipo chimatipatsa chiyembekezo chimene chimatikhozetsa kulimbika pa chiyeso.​—7/1, tsamba 8.

▫ Kodi ndi thayo lalikulu liti limene mpingo wa Akristu odzozedwa unalanda Israyeli wakuthupi?

Mwaŵi wa kuchitira umboni ukulu wa Yehova pakati pa mitundu. (Yesaya 43:21; 1 Petro 2:9)​—7/1, tsamba 19.

▫ Kodi mawu a mtumwi Petro akuti mwamuna ayenera ‘kuchitira ulemu’ mkazi wake amatanthauzanji? (1 Petro 3:7)

Mwamuna amene amachitira ulemu mkazi wake samamchititsa manyazi kapena kumtsitsa. M’malo mwake, amasonyeza mwa mawu ndi zochita zake​—kuseri ndi poyera​—kuti amamuŵerengera kwambiri. (Miyambo 31:10-31)​—7/15, tsamba 19.

▫ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kupitikitsa wochimwa wosalapa mumpingo Wachikristu ndi kusonyeza chikondi?

Kuchotsa ndiko chisonyezero cha kukonda Yehova ndi njira zake. (Salmo 97:10) Kumasonyeza kukonda awo amene amalondola njira yolungama chifukwa chakuti kumachotsa munthu amene angapereke chisonkhezero choipa pakati pawo; kumatetezeranso chiyero cha mpingo. (1 Akorinto 5:1-13)​—7/15, tsamba 25.

▫ Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” wotchulidwa ndi Yesu pa Mateyu 24:45-47, angadziŵidwe motani lerolino?

Makamaka amadziŵika mwa ntchito imene amachita pogaŵira zofalitsa zozikidwa pa Baibulo, pophunzitsa ndi kulalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu,’ ndi kumamatira kwawo zolimba ku Mawu a Mulungu, Baibulo. (Mateyu 24:14; 28:19, 20)​—8/1, tsamba 16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena