Zakudya za m’Bokosi Zichita Umboni
M’MASIKU a pambuyo pa chivomezi ku Kobe, Japan, January wathayu, anthu a kumalo okanthidwawo anali kuvutika kupeza chakudya. Komabe, Mboni za Yehova sizinasoŵe chakudya, chifukwa cha thandizo lachikondi la mabwenzi awo. Kwa masiku aŵiri kapena atatu pambuyo pa chivomezi, mipingo yapafupi inapereka mpunga. Posapita nthaŵi, mabwenzi achifundo anayamba kupereka zakudya za m’mabokosi. Ku mabokosi a zakudyawo, ambiri anamamatizako timapepala tolembapo mawu osonyeza chikondi chawo kwa osoŵawo. Awo amene analandira chakudyacho ananena kuti chakudya chilichonse “chinamveka mchere” chifukwa cha misozi yogwerako imene sanakwanitse kuiletsa pamene anaŵerenga timapepalato.
Mboni za Yehova zinagaŵana zakudyazo ndi osoŵa ena. Mboni ina inali kudya chakudya chake cha masana pamene inali kuyenda pagalimoto ndi mnzake wogwira naye ntchito m’kampani imodzi wosakhala Mboni. Motero anagaŵana naye chakudya cha m’limodzi la mabokosi amene anali atalandira kuchokera ku zoperekedwa za chithandizo.
“Kodi chakudya chamasana cha m’bokosi chimenechi mwachigula kuti?” mnzakeyo anafunsa. Mbaleyo anafotokoza ntchito yachithandizo ya Mboni. “Kwa masiku angapo sindinadye ndiwo za masamba. Ndidzasunga zina ndi kupita nazo kunyumba kwa banja langa,” mwamunayo ananena moyamikira.
Nthaŵi yachitatu pamene izi zinachitika, mwamunayo anapereka ma yen 3,000 (pafupifupi $35, U.S.) kwa Mboniyo ndi kunena kuti: “Ndikudziŵa zochita zanu, motero chonde ndiloleni ndipatse chopereka ku ntchito yanu. Ndiyamikira kwambiri kugaŵana kwanu zakudya ndi ine. Mabwenzi anu onse ndi anthu abwinodi.”