Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 12/1 tsamba 4-7
  • Kupereka Thangato Pakati pa Zowonongeka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupereka Thangato Pakati pa Zowonongeka
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Accra​—“Tsiku la Nowa Laling’ono”
  • San Angelo​—“Zinamveka Ngati Kuti Dziko Linali Kutha”
  • Kobe​—“Mulu wa Zowonongeka za Matabwa, Pulasitala ndi Mitembo ya Anthu”
  • Mpumulo Wachikhalire Posachedwa!
  • Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Zinthu Zimene Mkuntho wa Hurricane Andrew Sunakhoze Kuwononga
    Galamukani!—1993
  • Chimene Mkuntho Sunathe Kukokolola
    Galamukani!—2003
  • Pamene Kugwa Masoka Achilengedwe
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 12/1 tsamba 4-7

Kupereka Thangato Pakati pa Zowonongeka

KHAMA la munthu popereka thangato kutagwa tsoka liyeneradi kutamandidwa. Mabungwe ambiri a thangato athandizira kumanganso nyumba, kugwirizanitsanso mabanja, ndipo, koposa zonse, kupulumutsa moyo.

Kutagwa tsoka, Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito​—ndipo zimathokoza kaamba ka​—makonzedwe alionse opangidwa ndi mabungwe a thangato a boma. Nthaŵi imodzimodziyo, zili ndi thayo la m’Malemba la ‘kuchitira . . . chokoma, . . . makamaka iwo a pabanja [lawo] la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Inde, Mboni zimaona ngati kuti zili paubale; zimaonana monga “banja.” Nchifukwa chake zimatchana “mbale” ndi “mlongo.”​—Yerekezerani ndi Marko 3:31-35; Filemoni 1, 2.

Chotero pamene tsoka ligwera malo ena ake, akulu pakati pa Mboni za Yehova amayesayesa mwakhama kuti adziŵe kumene chiŵalo chilichonse cha mpingo chili ndi zimene chikufunikira ndi kupanga makonzedwe operekera thandizo lofunikalo. Taonani mmene zimenezi zinachitikira ku Accra, Ghana; San Angelo, U.S.A.; ndi Kobe, Japan.

Accra​—“Tsiku la Nowa Laling’ono”

Mvula inayamba kugwa cha ku ma 11 koloko usiku, ndipo inagwa mosalekeza kwa maola ambiri. “Inali kugwa zolimba kwakuti banja langa lonse linali maso,” akutero John Twumasi, mmodzi wa Mboni za Yehova ku Accra. Daily Graphic inaitcha “Tsiku la Nowa laling’ono.” “Tinayesa kusamutsira m’chipinda chapamwamba katundu wina wamtengo wapatali,” John akupitiriza, “koma potsegula chitseko cha makwerero, madzi a chigumulawo analoŵa.”

Aboma anapereka chenjezo lakuti anthu onse achoke, koma ambiri anazengereza, powopera kuti nyumba yopanda anthu​—ngakhale yodzaza madzi​—ikanapatsa mwaŵi ofunkha. Ena sanachoke ngakhale kuti anali kufuna. “Ineyo ndi amayi sitinathe kutsegula chitseko,” akutero mtsikana wina wotchedwa Paulina. “Madzi anapitiriza kukwera, chotero tinaimirira pa mikunda ya matabwa ndi kugwirira kumtanda wa tsindwi. Potsirizira pake, cha ku ma 5 koloko mmaŵa, anansi athu anatipulumutsa.”

Mpata utapezeka, Mboni za Yehova zinayamba nthaŵi yomweyo kugwira ntchito. Mlongo wina wachikristu wotchedwa Beatrice akuti: “Akulu mumpingo anali kutifunafuna, ndipo anatipeza kunyumba kwa Mboni inzathu, kumene tinathaŵira. Masiku atatu okha chigumula chitatha, akulu ndi achichepere mumpingo anabwera kwa ife napala matope mkati ndi kunja kwa nyumba yathu. Watch Tower Society inapereka zoyeretsera, mankhwala oletsa tizilombo, penti, mamatiresi, mabulanjeti, nsalu, ndi zovala za ana. Abale anatitumizira chakudya cha masiku angapo. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri!”

John Twumasi, wogwidwa mawu poyambayo, akuti: “Ndinauza ochita lendi ena kuti Sosaite yathu inatitumizira zoyeretsera ndi mankhwala oletsa tizilombo​—zokwanira kuyeretsera nyumba yonse. Ochita lendi pafupifupi 40 anathandiza kuyeretsa. Ndinapatsako anansi anga zoyeretsera zina, kuphatikizapo mwamuna wina amene anali wansembe patchalitchi chakwathu. Anzanga a kuntchito mosadziŵa anaganiza kuti Mboni za Yehova zimangosonyeza chikondi kwa anthu awo.”

Abale ndi alongo achikristu anayamikira kwambiri thandizo lachikondi limene anapatsidwa. Mbale Twumasi akumaliza mwa kunena kuti: “Ngakhale kuti zimene ndinataya chifukwa cha chigumula zinagulidwa ndi ndalama zochuluka kuposa zinthu za thangato, ineyo ndi banja langa tikhulupirira kuti chifukwa cha zogaŵira zokhudza mtima zimenezi zochokera ku Sosaite, tapeza zambiri kuposa zimene tinataya.”

San Angelo​—“Zinamveka Ngati Kuti Dziko Linali Kutha”

Mikuntho imene inasakaza San Angelo pa May 28, 1995, inazula mitengo, kuthyola milongoti ya magetsi, ndi kuponyera m’misewu mawaya amagetsi. Mphepo zinathamanga kufikira makilomita 160 pa ola limodzi, zikumawononga nyumba za magetsi. Nyumba zoposa 20,000 zinakhala mumdima. Ndiyeno kunadza matalala. National Weather Service inasimba za “matalala aakulu ngati mpira wa gofu,” ndiyeno “matalala aakulu ngati mpira wa softball,” ndipo potsirizira pake “matalala aakulu ngati grapefruit.” Phokoso lake linali logonthetsa m’kutu. Munthu wina anati: “Zinamveka ngati kuti dziko linali kutha.”

Pambuyo pake panatsatira bata lochititsa mantha. Anthu anayamba kutuluka pang’onopang’ono m’nyumba zawo zowonongeka kuti aone mmene zinthu zinawonongekera. Mitengo imene inatsala ili chiimire inali itayoyoka masamba ake. Nyumba zimene zinatsala zili chiimire zinaoneka ngati anazisumbudzula. M’madera ena matalala anaphimba nthaka kufikira mita imodzi kuya kwake. Magalasi zikwi zambiri a mazenera a nyumba ndi galimoto anasweka chifukwa cha mkunthowo, kwakuti tsopano zidutswa za magalasi osweka zinali kunyezimira limodzi ndi matalala amene anaphimba nthaka. “Nditafika kunyumba,” mkazi wina anatero, “ndinangokhala m’galimoto langa m’kamsewu koloŵera ndi kulira. Zimene zinawonongeka zinanyanya, zinangondithetsa nzeru.”

Mwamsanga mabungwe a thangato ndi zipatala anapereka thandizo la ndalama, mirimo, mankhwala, ndi malangizo. Nzoyamikirika kuti anthu ambiri amene nawonso anakhudzidwa ndi mkunthowo anachita zomwe anatha kuti athandize ena.

Nawonso mpingo wa Mboni za Yehova unachitapo kanthu. Aubrey Conner, mkulu ku San Angelo, akuti: “Mkunthowo utangotha, tinali kuimba mafoni kuti tidziŵe za wina ndi mnzake. Tinathandizana ndi kuthandizanso anansi athu osakhala Mboni kuika matabwa pa mazenera, mapulasitiki pa matsindwi, ndi kutchinjiriza nyumba monga momwe kungathekere kuti zisamaloŵe madzi ndi mphepo. Ndiyeno tinapanga faelo ya munthu aliyense mumpingo amene nyumba yake inawonongeka. Pafupifupi nyumba zana limodzi zinafunikira kukonzedwa, ndipo mirimo yoperekedwa ndi mabungwe athangato inali yosakwanira. Chotero tinagula mirimo ina ndi kukonzekera ntchitoyo. Onse pamodzi, Mboni 1,000 zinadzipereka kuti zithandize, pafupifupi 250 pakutha kwa mlungu uliwonse. Zinachokera kutali ngakhale kumtunda wa makilomita 740. Onse anagwira ntchito zolimba, nthaŵi zambiri temperecha ili pa 40 digiri Celsius. Ngakhale mlongo wina wazaka 70 anagwira nafe ntchito pakutha kwa mlungu uliwonse kusiyapo umodzi, pamene nyumba yake inali kukonzedwa. Ndipo pakutha kwa mlungupo iye anali patsindwi la nyumba yakeyo akumathandiza ena kukonza!

“Nthaŵi zambiri tinamva openyerera akunena mawu onga akuti, ‘Kodi sikukanakhala bwino ngati zipembedzo zina zikanachita zimenezi kwa anthu awo?’ Anansi athu anachita chidwi poona antchito odzifunira 10 mpaka 12 (kuphatikizapo alongo) akufika Lachisanu mmamaŵa panyumba ya Mboni inzawo, okonzekera kukonza kapena ngakhale kuikanso tsindwi latsopano pa nyumba yonse kwaulere. Nthaŵi zambiri ntchito inali kutha pamlungu umodzi. Nthaŵi zina, womanga wakunja amakhala ali mkati mwa ntchito yokonza tsindwi pamene gulu lathu la antchito linali kufika panyumba yoyandikana nayo. Tinali kupasula ndi kukonzanso tsindwi lathu ndi kuyeretsa bwalo iwo asanamalize ntchito yawo. Nthaŵi zina iwo anali kuleka kugwira ntchito yawo namangotipenya!”

Mbale Conner akumaliza mwa kunena kuti: “Tonsefe tidzalakalaka nthaŵi imeneyi imene tachitira zinthu pamodzi. Tafika pakudziŵana wina ndi mnzake m’njira zosiyana mwa kusonyeza ndi kusonyezedwa chikondi cha pa abale kuposa ndi kale lonse. Tikhulupirira kuti zimenezi zangokhala chitsanzo cha mmene zinthu zidzakhalira m’dziko latsopano la Mulungu, abale ndi alongo akumathandizana chifukwa chakuti akufunadi kutero.”​—2 Petro 3:13.

Kobe​—“Mulu wa Zowonongeka za Matabwa, Pulasitala ndi Mitembo ya Anthu”

Anthu a ku Kobe anafunikira kukhala okonzekera. Ndithudi, September 1 aliyense iwo amakumbukira Tsiku Loletsa Masoka. Ana a sukulu amayeseza njira zopulumukira chivomezi, asilikali amayeseza ntchito yopulumutsa anthu ndi mahelikopitala, ndipo ozimitsa moto amabweretsa makina awo oyerekezera chivomezi, amene anthu odzipereka amayesezamo maluso awo opulumukira m’bokosi lalikulu ngati chipinda limene limagwedezeka ndi kunjenjemera ngati chivomezi chenicheni. Koma pamene chivomezi chinachitikadi pa January 17, 1995, kukonzekera konse kunaoneka ngati kopanda pake. Matsindwi zikwi makumi ambiri anagwera mkati​—zimene sizinachitikepo m’makina oyesezera. Sitima za pamtunda zinagubuduka; zigawo za misewu yaikulu zinagamuka; mipope ya gasi ndi madzi inabooka; nyumba zinagumuka ngati mabokosi amapepala. Magazini a Time anafotokoza malowo kukhala “mulu wa zowonongeka za matabwa, pulasitala ndi mitembo ya anthu.”

Ndiyeno panabuka moto. Nyumba zinalilima pamene ozimitsa moto othedwa nzeru analephera kuyenda chifukwa cha mzera wautali wa galimoto zondondozana kwambiri. Amene anafika kumene kunali moto anapeza kuti sakanatha kutsegula madzi m’mipope yowonongeka ya mzindawo. “Tsiku loyamba kunali msokonezo wokhawokha,” anatero mkulu wina wa ntchito. “Sindinathedwepo mphamvu chonchi m’moyo wanga, podziŵa kuti munali anthu ambiri okwiriridwa m’nyumba zija zoyaka moto. Ndi podziŵanso kuti palibe zimene ndikanachita.”

Onse pamodzi, anthu ngati 5,000 anafa, ndipo nyumba pafupifupi 50,000 zinawonongeka. Kobe anali chabe ndi limodzi la magawo atatu la chakudya chofunikira. Kuti apeze madzi, ena anayamba kukolokota madzi akuda pansi pa mipope ya madzi yobooka. Ambiri osoŵa nyumba anathaŵira kumisasa, ndipo ku ina ya imeneyi anali kugaŵira phoso, akumapatsa munthu aliyense mpunga pang’ono patsiku. Posapita nthaŵi kusakhutira kunawanda. “Boma silinachitepo kalikonse,” mwamuna wina anadandaula motero. “Tikapitiriza kuwadalira, tifa ndi njala.”

Mipingo ya Mboni za Yehova m’Kobe ndi m’madera apafupi nthaŵi yomweyo inadzikonzekeretsa. Woyendetsa helikopitala amene anayamba kuona ntchito yawo anati: “Ndinapita kudera la tsokalo tsiku limene chivomezi chinachitika ndi kukhala komweko mlungu umodzi. Nditafika pamsasa wina, panali chipolowe chokhachokha. Panalibe ntchito iliyonse ya thangato imene inali kuchitika. Mboni za Yehova ndizo zokha zimene zinathamangira kumalowo, zikumasamalira izi ndi izi.”

Inde, panali ntchito yochuluka yofuna kuchitidwa. Nyumba za Ufumu khumi zinakhala zosayenera kugwiritsira ntchito, ndipo Mboni zoposa 430 zinalibe nyumba. Nyumba zinanso 1,206 zimene anali kukhalamo zinafunikira kukonza. Si zokhazo ayi komanso mabanja a Mboni 15 zimene zinamwalira m’tsokalo anali kufunitsitsa chitonthozo.

Mboni ngati 1,000 zakuderalo zinapatula nthaŵi yawo kuti zithandize pantchito yokonza. “Pamene tinali kugwira ntchito panyumba za ophunzira Baibulo osabatizidwa,” akutero mbale wina, “nthaŵi zonse anali kutifunsa kuti, ‘Kodi tidzalipira zingati pa zonsezi?’ Titawauza kuti ntchitoyo inali kuchirikizidwa ndi mipingo, anatiyamikira kuti, ‘Tsopano taona zimene tinaphunzira!’”

Ambiri anachita chidwi ndi Mboni chifukwa cha kuchitapo kanthu kwawo msanga ndipo mosamalitsa pa tsokalo. “Ndinachitadi chidwi,” woyendetsa helikopitala wogwidwa mawu poyambayo anatero. “Mumatchana ‘mbale’ ndi ‘mlongo.’ Ndaona mmene mumathandizirana; anthu inu ndinudi banja lenileni.”

Mboninso zinatengapo maphunziro opindulitsa pa chivomezicho. Mlongo wina anavomereza kuti: “Nthaŵi zonse ndaganiza kuti pamene gulu likukulirakulira, kumakhalanso kovuta kwambiri kuderana nkhaŵa wina ndi mnzake.” Koma chisamaliro cha chifundo chimene analandira chinasintha maganizo ake. “Tsopano ndadziŵa kuti Yehova akutisamalira osati monga gulu chabe komanso monga munthu aliyense payekha.” Komabe, mpumulo wachikhalire ku masoka uli mtsogolo.

Mpumulo Wachikhalire Posachedwa!

Mboni za Yehova zikuyembekezera nthaŵiyo pamene moyo wa munthu ndi zousamalirira sizidzadukizidwanso ndi masoka. M’dziko latsopano la Mulungu, munthu adzaphunzitsidwa kuchita mogwirizana ndi malo okhala a dziko lapansi. Pamene anthu adzakhala akusiya machitachita adyera, sadzakhala pangozi ya masoka achilengedwe.

Ndiponso, Yehova Mulungu​—Mlengi wa mphamvu zachilengedwe​—adzatsimikizira kuti banja lake laumunthu ndi zolengedwa za padziko lapansi sizilinso pangozi ya mphamvu za chilengedwe. Ndiyeno dziko lapansi lidzakhaladi paradaiso. (Yesaya 65:17, 21, 23; Luka 23:43) Ulosi wa Chivumbulutso 21:4 udzakwaniritsidwa mwaulemerero: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”

[Chithunzi patsamba 5]

Beatrice Jones (kumanzere) akusonyeza mmene iye ndi ena anagwirirana manja kuti adutse pamadzi achigumula

[Chithunzi patsamba 6]

Ntchito ya thangato pambuyo pa mikuntho

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena