Chifukwa Chake Kulambira Koona Kumakhala ndi Dalitso la Mulungu
“Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama.”—CHIVUMBULUTSO 19:1, 2.
1. Kodi Babulo Wamkulu adzafika motani pamapeto ake?
“BABULO WAMKULU” wagwa m’maso mwa Mulungu ndipo tsopano ali pafupi kuleka kukhalako. Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti mkazi wachigololo wachipembedzo ameneyu wapadziko lonse posachedwapa adzawonongedwa ndi onyengana nawo ake andale; mapeto ake adzakhala odzidzimutsa ndi amwamsanga. Vumbulutso la Yesu kwa Yohane linali ndi mawu aulosi awa: “Mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.”—Chivumbulutso 18:2, 21.
2. Kodi atumiki a Yehova adzachita motani pa chiwonongeko cha Babulo?
2 Chiwonongeko cha Babulo Wamkulu adzalira nacho magulu ena a dziko la Satana koma atumiki a Mulungu sadzatero ayi, kumwamba kapena padziko lapansi. Mfuu yawo yachisangalalo kwa Mulungu idzakhala yakuti: “Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.”—Chivumbulutso 18:9, 10; 19:1, 2.
Kodi Chipembedzo Choona Chiyenera Kupatsa Zipatso Zotani?
3. Kodi ndi mafunso ati amene afunika mayankho?
3 Popeza dziko lapansi lidzayeretsedwa kuchotsapo chipembedzo chonyenga, kodi ndi kulambira kotani kumene kudzatsala? Kodi ife lero tingadziŵe motani gulu lachipembedzo limene lidzapulumuka chiwonongeko cha ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga wa Satana? Kodi zipatso zolungama zimene gululi liyenera kupatsa nzotani? Pali njira zosachepera khumi zodziŵira kulambira koona kwa Yehova.—Malaki 3:18; Mateyu 13:43.
4. Kodi chofunika choyamba cha kulambira koona nchotani, ndipo Yesu anapereka motani chitsanzo pankhaniyi?
4 Yoyamba ndi yofunika koposa, Akristu oona ayenera kuchirikiza uchifumu umene Yesu anafera—uchifumu wa Atate wake. Yesu sanapereke moyo wake kaamba ka chifuno cha ndale, mtundu, fuko, kapena kakhalidwe ka anthu. Iye anaika Ufumu wa Atate wake patsogolo pa zolinga za Ayuda zandale kapena zofuna kusintha zinthu. Pamene Satana anamsonyeza maulamuliro a dziko iye anayankha ndi mawu awa: “Choka Satana, pakuti kwalembedwa, [Yehova, NW] Mulungu wako udzamgwadira, ndipo iye yekhayekha udzamlambira.” Iye anadziŵa kuchokera m’Malemba Achihebri kuti Yehova ndiye Mfumu yoona padziko lonse lapansi. Kodi ndi gulu liti lachipembedzo limene motsimikiza limachirikiza ulamuliro wa Yehova m’malo mwa magulu a ndale a dzikoli?—Mateyu 4:10; Salmo 83:18.
5. (a) Kodi olambira oona ayenera kuliona motani dzina la Mulungu? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Mboni za Yehova zimalemekeza dzinalo?
5 Chofunika chachiŵiri nchakuti kulambira koona kuyenera kulemekeza ndi kuyeretsa dzina la Mulungu. Wamphamvuyonseyo anasonyeza dzina lake Yehova (lolembedwa kuti Yahweh m’Mabaibulo ena), kwa anthu ake Israyeli, ndipo lagwiritsiridwa ntchito nthaŵi zikwi zambiri m’Malemba Achihebri. Iye asanachite ndi zimenezo, Adamu, Hava, ndi ena analidziŵa dzinalo, ngakhale kuti sanalilemekeze nthaŵi zonse. (Genesis 4:1; 9:26; 22:14; Eksodo 6:2) Pamene otembenuza a Dziko Lachikristu ndi a Ayuda nthaŵi zambiri achotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo, Mboni za Yehova zaika dzinalo m’malo ake oyenera ndi kulilemekeza mu New World Translation of the Holy Scriptures. Zimalemekeza dzinalo, monga momwedi anachitira Akristu oyambirira. Yakobo anatsimikiza kuti: ‘Sumeoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake. Ndipo mawu a aneneri avomereza pamenepo; . . . kuti anthu otsalira afunefune [Yehova], ndi amitundu onse amene dzina langa linatchulidwa pa iwo, ati [Yehova], amene azidziŵitsa zinthu zonsezo.’—Machitidwe 15:14-17; Amosi 9:11, 12.
6. (a) Kodi chofunika chachitatu cha kulambira koona nchotani? (b) Kodi Yesu ndi Danieli anaugogomezera motani ulamuliro wa Ufumu? (Luka 17:20, 21)
6 Chofunika chachitatu cha kulambira koona nchakuti kuyenera kukweza Ufumu wa Mulungu monga mankhwala okha oyenera ndi ogwira ntchito othetsera mavuto a anthu okhudza ulamuliro. Yesu anawaphunzitsa bwino otsatira ake kupemphera kuti Ufumuwo udze, kuti ulamuliro wa Mulungu uyambe kuyendetsa zinthu padziko lapansi. Danieli anauziridwa kulosera za masiku otsiriza kuti: “Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse. . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [adziko, andale]. Nudzakhala chikhalire.” Kodi ndani m’zaka za zana lino la 20 amene mwa zochita zawo asonyeza kuti amachirikiza kotheratu Ufumuwo?—zipembedzo za Babulo Wamkulu kapena Mboni za Yehova?—Danieli 2:44; Mateyu 6:10; 24:14.
7. Kodi olambira oona amaliona motani Baibulo?
7 Chofunika chachinayi kuti pakhale chivomerezo cha Mulungu nchakuti atumiki oona a Mulungu ayenera kuchirikiza Baibulo monga Mawu ouziridwa a Mulungu. Chifukwa chake iwo sangatengeke ndi maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo, amene amayesa kululuza Baibulo kukhala buku wamba la anthu lokhala ndi zonse zimene zingakhale zolakwa zawo. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Baibulo lili Mawu ouziridwa a Mulungu, mongadi momwe Paulo analembera Timoteo kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”a Chifukwa chake, Mboni za Yehova zimaona Baibulo kukhala chitsogozo chawo, buku lawo la malangizo a moyo watsiku ndi tsiku, ndi kasupe wawo wa chiyembekezo cha mtsogolo.—2 Timoteo 3:16, 17.
Chipembedzo cha Chikondi, Osati cha Udani
8. Kodi chofunika chachisanu cha kulambira koona nchotani?
8 Kodi Yesu anawasiyanitsa motani otsatira ake oona? Yankho lake likutifikitsa pa chizindikiro chachisanu chofunika kwambiri chodziŵira kulambira koona. Yesu anati: ‘Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:34, 35) Kodi Yesu anasonyeza motani chikondi chake? Mwa kupereka moyo wake monga nsembe ya dipo. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Kodi nchifukwa ninji chikondi chenicheni chili mkhalidwe wofunika kwambiri kwa Akristu oona? Yohane anafotokoza kuti: “Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu . . . Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:7, 8.
9. Kodi ndani amene asonyeza chikondi choona, ndipo motani?
9 Kodi ndani m’nthaŵi yathu amene asonyeza chikondi choterechi, ngakhale pamene pali chidani chifukwa cha kusiyana khungu, mtundu, kapena fuko? Kodi ndani amene apambana chiyeso choposa, kufika ndi ku imfa, kuti chikondi chawo chisefukire? Kodi tinganene kuti ndi ansembe achikatolika ndi avirigo amene kunena zoona alinso ndi thayo la kupululutsa mafuko komwe kunachitika ku Rwanda mu 1994? Kodi ndi a Orthodox a ku Serbia kapena Akatolika a ku Croatia amene achita “kuyeretsa fuko” ndi machitachita ena osakhala achikristu m’nkhondo yachiŵeniŵeniyo ya kumaiko a Balkan? Kapena kodi ndi atsogoleri achipembedzo achikatolika kapena achiprotesitanti amene asonkhezera tsankho ndi chidani ku Northern Ireland pazaka makumi oŵerengeka zapitazo? Inde Mboni za Yehova sizingaimbidwe mlandu wa kutengamo mbali m’kulimbana kulikonse kotero. Zazunzika m’ndende ndi m’misasa yachibalo, mpaka imfa ndithu, m’malo mwakuti zitaye chikondi chawo chachikristu.—Yohane 15:17.
10. Kodi nchifukwa ninji Akristu oona amasunga uchete?
10 Chofunika chachisanu ndi chimodzi cha kulambira kovomerezeka kwa Mulungu ndicho uchete kulinga ku nkhani zandale za dzikoli. Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhala auchete pa zandale? Paulo, Yakobo, ndi Yohane akutipatsa chifukwa champhamvu cha kaimidwe kameneka. Mtumwi Paulo analemba kuti Satana ndiye “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” amene akuchititsa khungu maganizo a osakhulupirira mwa njira iliyonse yotheka, kuphatikizapo ndi ndale zogaŵanitsa. Wophunzira Yakobo anati “ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu,” ndipo mtumwi Yohane anati “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Chifukwa chake, Mkristu woona sangayese kutaya kudzipereka kwake kwa Mulungu mwa kuloŵa m’ndale ndi ulamuliro wa dziko la Satana loipali.—2 Akorinto 4:4; Yakobo 4:4; 1 Yohane 5:19.
11. (a) Kodi Akristu amaiona motani nkhondo? (b) Kodi chifukwa cha Malemba cha kaimidwe kameneka nchotani? (2 Akorinto 10:3-5)
11 Chifukwa cha zofunika ziŵiri zapitazo, chachisanu ndi chiŵiri nchachionekere, chimene chili chakuti olambira oona achikristu sayenera kutengamo mbali m’nkhondo. Popeza chipembedzo choona ndicho ubale wa dziko lonse wozikidwa pa chikondi, ndiye kuti palibe chimene chingagaŵanitse kapena kuwononga “gulu lonse la abale . . . m’dziko.” Yesu anaphunzitsa chikondi, osati udani; mtendere, osati nkhondo. (1 Petro 5:9, NW; Mateyu 26:51, 52) “Woipa” mmodzimodziyo, Satana, amene anasonkhezera Kaini kupha Abele akupitiriza kufesa udani pakati pa anthu ndi kusonkhezera nkhondo ndi kukhetsa mwazi pamaziko a kugaŵanikana pa zandale, chipembedzo, ndi mafuko. Akristu oona ‘saphunziranso nkhondo,’ mosasamala kanthu za zimene zingatulukepo. Mophiphiritsira, iwo ‘asula kale malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape.’ Amabala zipatso zamtendere za mzimu wa Mulungu.—1 Yohane 3:10-12; Yesaya 2:2-4; Agalatiya 5:22, 23.
Mulungu Amadalitsa Chiyero cha Makhalidwe ndi cha Ziphunzitso
12. (a) Kodi chofunika chachisanu ndi chitatu nchotani, koma kodi ndi magaŵano otani azipembedzo amene mungatchule? (b) Kodi Paulo anasonyeza motani chofunika chimenechi chachisanu ndi chitatu?
12 Umodzi wachikristu ndiwo chofunika chachisanu ndi chitatu cha kulambira koona. Komabe, zipembedzo zogaŵanitsa za Dziko Lachikristu zalephera kuudzetsa uwo. Ambiri otchedwa matchalitchi ofala agaŵanika kukhala mipatuko yamitundumitundu, ndipo pakhala msokonezo. Mwachitsanzo, tatengani chipembedzo cha Baptist ku United States, chimene chili chogaŵanika pakati pa a Northern Baptists (Matchalitchi a Abaptist Achimereka ku U.S.A.) ndi a Southern Baptists (Mgwirizano wa Abaptist Wakummwera), ndiponso magulu ena ambiri a Abaptist amene akhalapo chifukwa cha magaŵanowo. (World Christian Encyclopedia, tsamba 714) Magaŵano ambiri akhalapo chifukwa cha kusiyana kwa ziphunzitso kapena utsogoleri wa tchalitchi (mwachitsanzo, Presbyterian, Episcopalian, Congregational). Magaŵano a Dziko Lachikristu ali olingana ndi aja a zipembedzo za kunja kwa Dziko Lachikristu—kaya Chibudha, Chisilamu, kapena Chihindu. Kodi mtumwi Paulo anawalangiza chiyani Akristu oyambirira? “Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mumtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.”—1 Akorinto 1:10; 2 Akorinto 13:11.
13, 14. (a) Kodi ‘kukhala oyera mtima’ kumatanthauzanji? (b) Kodi ndi motani mmene kulambira koona kumasungidwira koyera?
13 Kodi chofunika chachisanu ndi chinayi nchiyani pa chipembedzo chovomerezedwa ndi Mulungu? Pulinsipulo la Baibulo lasonyezedwa pa Levitiko 11:45: “Mukhale oyera, popeza ine ndine woyera.” Mtumwi Petro anabwereza chofunika chimenechi pamene analemba kuti: ‘Monga mwa iye wakuitana inu ali Woyera Mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse.’—1 Petro 1:15.
14 Kodi chofunika chimenechi cha kukhala oyera chikutanthauzanji? Kuti olambira a Yehova ayenera kukhala oyera mwauzimu ndi m’makhalidwe. (2 Petro 3:14) Palibe malo a ochimwa dala osalapa, amene mwa makhalidwe awo amachitira mwano nsembe ya dipo ya Kristu. (Ahebri 6:4-6) Yehova amafuna kuti mpingo wachikristu ukhale wokonzeka ndi woyera. Kodi zimenezo zimachitika motani? Njira ina ndiyo ya kuchotsa kochitidwa mwa kuweruza aja amene angaipitse mpingo.—1 Akorinto 5:9-13.
15, 16. Kodi ndi masinthidwe otani amene Akristu ambiri apanga m’moyo wawo?
15 Asanadziŵe choonadi chachikristu, ambiri anali ndi moyo wosadziletsa, wokonda zokondweretsa, ndi wodzikonda. Koma mawu onena za Kristu anawasintha, ndipo apeza chikhululukiro cha machimo awo. Paulo anasonyeza zimenezo mwamphamvu pamene analemba kuti: ‘Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa.’—1 Akorinto 6:9-11.
16 Nzachionekere kuti Yehova amayanja aja amene alapa nasiya makhalidwe awo otsutsana ndi malemba, kutembenuka, ndi kukhala otsatira oona a Kristu ndi ziphunzitso zake. Iwo amakondadi anansi awo monga adzikonda okha ndipo amasonyeza zimenezo m’njira zambiri, monga mwa kulimbikira mu utumiki umene umapereka uthenga wa moyo kwa onse omwe angamve.—2 Timoteo 4:5.
“Choonadi Chidzakumasulani”
17. Kodi chofunika chachikhumi cha kulambira koona nchotani? Perekani zitsanzo.
17 Palinso chachikhumi chimene Yehova amafuna kwa aja omlambira mumzimu ndi m’choonadi—chiphunzitso choyera. (Yohane 4:23, 24) Yesu anati kwa otsatira ake: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Choonadi cha Baibulo chimatimasula ku ziphunzitso zosalemekeza Mulungu, monga sou yosafa, moto wa helo, ndi purigatoriyo. (Mlaliki 9:5, 6, 10; Ezekieli 18:4, 20, NW) Chimatimasula ku chinsinsi chachibabulo cha “Utatu Wopatulikitsa” wa Dziko Lachikristu. (Deuteronomo 4:35; 6:4; 1 Akorinto 15:27, 28) Kumvera choonadi cha Baibulo kumachititsa anthu kukhala achikondi, odera nkhaŵa ena, okoma mtima, ndi achifundo. Chikristu choona sichinachirikizepo oweruza osalolera ndi okonda kulipsira a bwalo la inquisition, monga Tomás de Torquemada, kapena osonkhezera nkhondo audani, monga apapa ochirikiza Nkhondo za Mtanda. Komabe, Babulo Wamkulu wapatsa zipatso zotero m’mbiri yonse, kwenikweni kuyambira nthaŵi ya Nimrode mpaka lero.—Genesis 10:8, 9.
Dzina Lapadera
18. (a) Kodi ndani amene amakwaniritsa zofunikazo khumi za kulambira koona ndipo motani? (b) Kodi ife payekhapayekha tiyenera kuchitanji kuti tikalandire dalitso limene lili mtsogolo?
18 Kodi ndani lerolino amene amakwaniritsa zofunika khumi zimenezi za kulambira koona? Kodi ndani amene ena amawadziŵa ndi kuwazindikira chifukwa cha mbiri yawo ya umphumphu ndi mtendere? Padziko lonse Mboni za Yehova zimadziŵika chifukwa cha ‘kusakhala kwawo a dziko lapansi.’ (Yohane 15:19; 17:14, 16; 18:36) Anthu a Yehova ali ndi mwaŵi wakunyamula dzina lake ndi kukhala Mboni zake, mongadi momwe Yesu Kristu analili mboni yokhulupirika kwa Atate wake. Timanyamula dzina loyeralo, tikumazindikira thayo lathu lakukwaniritsa zimene limaimira. Ndipo, pokhala Mboni zake, tilidi ndi chiyembekezo chaulemerero cha mtsogolo! Ndicho kukhala mbali ya banja laumunthu logwirizana ndi lomvera, lolambira Mfumu ya Chilengedwe Chonse m’paradaiso wobwezeretsedwa pano padziko lapansi. Kuti tikalandire dalitso limenelo, tiyeni tipitirize kusonyeza bwino lomwe kuti tili kumbali ya kulambira koona ndi kunyamula dzinalo Mboni za Yehova monyadira “pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama”!—Chivumbulutso 19:2; Yesaya 43:10-12; Ezekieli 3:11.
[Mawu a M’munsi]
a Matembenuzidwe a Baibulo okha sali ouziridwa ndi Mulungu. Matembenuzidwewo, malinga ndi mmene alili, angasonyeze kusiyanasiyana kwa kamvedwe ka zinenero zoyamba zimene Baibulo linalembedwamo.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi atumiki a Yehova akuchiona motani chiwonongeko cha Babulo Wamkulu?
◻ Kodi zofunika zazikulu za kulambira koona nzotani?
◻ Kodi choonadi chimakumasulani motani?
◻ Kodi ndi mwaŵi wapadera wotani umene tili nawo monga Mboni za Yehova?
[Zithunzi patsamba 17]
Mboni za Yehova zikulalikira ndi kuphunzitsa za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu
[Chithunzi patsamba 18]
Akristu oona asunga uchete nthaŵi zonse pa ndale zadziko ndi nkhondo
[Mawu a Chithunzi]
Ndege: Chilolezo cha Ministry of Defense, London