Dziperekeni pa Kuŵerenga
“Kufikira ndidza ine, usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza.”—1 TIMOTEO 4:13.
1. Kodi tingapindule motani ndi kuŵerenga Baibulo?
YEHOVA MULUNGU wapatsa anthu luso lodabwitsa la kuphunzira kuŵerenga ndi kulemba. Waperekanso Mawu ake, Baibulo, kotero kuti tilangizidwe bwino. (Yesaya 30:20, 21) Kwenikweni, masamba ake amatikhozetsa ‘kuyenda’ ndi makolo owopa Mulungu onga Abrahamu, Isake, ndi Yakobo. Tingathe ‘kuona’ akazi owopa Mulungu onga Sara, Rebeka, ndi Rute Mmoabu wokhulupirika. Inde, ndipo tingathe ‘kumva’ Yesu Kristu akupereka Ulaliki wake wa pa Phiri. Zosangalatsa zonsezi ndi malangizo ambiri ochokera m’Malemba Opatulika zingakhale zathu ngati tili oŵerenga abwino.
2. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yesu ndi ophunzira ake ankatha kuŵerenga bwino?
2 Mosakayikira, munthu wangwiroyo Yesu Kristu anali ndi luso labwino kwambiri la kuŵerenga, ndipotu iye anadziŵa bwino kwambiri Malemba Achihebri. Motero, pamene anayesedwa ndi Mdyerekezi, mobwerezabwereza Yesu anawagwira mawu nanena kuti “Kwalembedwa.” (Mateyu 4:4, 7, 10) Panthaŵi ina mu sunagoge ku Nazarete, iye anaŵerenga ndi kusonyeza kukwaniritsidwa kwa mbali ya ulosi wa Yesaya pa iye mwini. (Luka 4:16-21) Bwanji nanga za atumwi a Yesu? M’zolemba zawo, iwo kaŵirikaŵiri anagwira mawu Malemba Achihebri. Ngakhale kuti olamulira achiyuda anaona Petro ndi Yohane ngati anthu wamba osaphunzira chifukwa chakuti sanapite kusukulu zamaphunziro apamwamba zachihebri, makalata awo ouziridwa ndi Mulungu amasonyeza bwino kuti ankatha kuŵerenga ndi kulemba bwino. (Machitidwe 4:13) Koma kodi luso la kuŵerenga nlofunikadi?
“Wachimwemwe Ndi Iye Amene Amaŵerenga Momveka”
3. Kodi nchifukwa ninji kuŵerenga Malemba ndi zofalitsa zachikristu kuli kofunika kwambiri?
3 Kuloŵetsa ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso cholongosoka cha Malemba kungatichititse kupeza moyo wosatha. (Yohane 17:3) Chotero Mboni za Yehova zimazindikira kuti kuli kofunika kwambiri kuŵerenga ndi kuphunzira Malemba Opatulika ndi zofalitsa zachikristu zogaŵiridwa ndi Mulungu kupyolera mwa kagulu kake ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ka Akristu odzozedwa. (Mateyu 24:45-47) Kunena zoona, mwa kugwiritsira ntchito zofalitsa zapadera za Watch Tower, anthu zikwi zambiri aphunzitsidwa kuŵerenga ndipo motero apeza chidziŵitso chopatsa moyo cha Mawu a Mulungu.
4. (a) Kodi nchifukwa ninji chimwemwe chimadza mwa kuŵerenga, kuphunzira, ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu? (b) Ponena za kuŵerenga, kodi nchiyani chimene Paulo anauza Timoteo?
4 Chimwemwe chimadza mwa kuŵerenga, kuphunzira, ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti mwa kutero timakondweretsa ndi kulemekeza Mulungu, kulandira madalitso ake, ndi kupeza chisangalalo. Yehova amafuna kuti atumiki ake akhale achimwemwe. Chifukwa cha chimenecho, iye analamula ansembe kuŵerengera Chilamulo chake mtundu wa Israyeli wakale. (Deuteronomo 31:9-12) Pamene Ezara mlembiyo ndi ena anaŵerengera Chilamulo anthu onse osonkhana mu Yerusalemu, anamveketsa tanthauzo lake, ndipo panachitika “kusekerera kwakukulu.” (Nehemiya 8:6-8, 12) Pambuyo pake mtumwi wachikristu Paulo anauza wantchito mnzake Timoteo kuti: “Kufikira ndidza ine, usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza.” (1 Timoteo 4:13) Matembenuzidwe ena amati: “Dzipereke pa kuŵerenga Malemba poyera.”—New International Version.
5. Kodi ndi motani mmene Chivumbulutso 1:3 chimagwirizanitsira chimwemwe ndi kuŵerenga?
5 Mfundo yakuti chimwemwe chathu chimadalira pa kuŵerenga ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu yasonyezedwa bwino pa Chivumbulutso 1:3, NW. Pamenepo timauzidwa kuti: “Wachimwemwe ndi iye amene amaŵerenga momveka ndi aja amene amamva mawu a ulosiwu, ndi amene amasunga zinthu zolembedwamo; pakuti nthaŵi yoikidwiratu yayandikira.” Inde, tifunikira kuŵerenga momveka ndi kumva mawu a ulosi wa Mulungu m’Chivumbulutso ndi m’Malemba onse. Munthu amene ali wachimwemwedi ndiye amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” Chotulukapo chake? “Zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:1-3) Motero, pa zifukwa zabwino, gulu la Yehova limalimbikitsa aliyense wa ife kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu ake mwaumwini, monga mabanja, ndiponso ndi mabwenzi.
Ganizani Mwamphamvu ndi Kusinkhasinkha
6. Kodi Yoswa analamulidwa kuŵerenga chiyani, ndipo zimenezi zinali zopindulitsa motani?
6 Kodi ndi motani mmene mungapindulire kwambiri pa kuŵerenga kwanu Mawu a Mulungu ndi zofalitsa zachikristu? Mwachionekere kudzakhala kopindulitsa kwa inu kuchita zimene anachita Yoswa, mtsogoleri wowopa Mulungu wa Israyeli wakale. Iye analamulidwa kuti: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiliremo [“uliŵerenge chamunsi,” NW] usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.” (Yoswa 1:8) ‘Kuliŵerenga chamunsi’ kumatanthauza kunena nokha mawu motsitsa. Zimenezi zimathandiza kukumbukira, pakuti zimakhomereza mfundo m’maganizo. Yoswa anafunikira kuŵerenga Chilamulo cha Mulungu “usana ndi usiku,” kapena nthaŵi zonse. Imeneyo inali njira yakuti akometse njira yake ndi kuchita mwanzeru posenza mathayo operekedwa ndi Mulungu. Kuŵerenga Mawu a Mulungu kwanthaŵi zonse kotero kungakuthandizeni mofananamo.
7. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulola lingaliro la kuthamanga kukula pamene tikuŵerenga Mawu a Mulungu?
7 Musalole lingaliro la kuthamanga kukula pamene mukuŵerenga Mawu a Mulungu. Ngati mwalinganiza kuthera nyengo yoikika ya kuŵerenga Baibulo kapena chofalitsa chinachake chachikristu, musathamange. Zimenezi nzofunika kwambiri makamaka pamene mukuphunzira muli ndi cholinga cha kufuna kukumbukira mfundo zina zapadera. Ndipo pamene muŵerenga, ganizani mwamphamvu. Pendani mawu a wolemba Baibulo. Dzifunseni kuti, ‘Kodi akusonyeza mfundo yotani? Kodi ndiyenera kuchitanji ndi chidziŵitso chimenechi?’
8. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kusinkhasinkha poŵerenga Malemba?
8 Patulani nthaŵi ya kusinkhasinkha pamene mukuŵerenga Malemba Opatulika. Zimenezi zidzakuthandizani kukumbukira nkhani za m’Baibulo ndi kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Malemba. Kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu ndipo motero mukumakhomereza mfundo zake m’maganizo kudzakukhozetsaninso kulankhula kuchokera mumtima, mukumapereka mayankho abwino kwa ofunadi kudziŵa m’malo mwa kunena zinthu zina zimene mudzadziimba nazo mlandu pambuyo pake. Mwambi wina wouziridwa ndi Mulungu umati: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.”—Miyambo 15:28.
Gwirizanitsani Mfundo Zatsopano ndi Zakale
9, 10. Kodi kuŵerenga Baibulo kwanu kungachirikizidwe motani mwa kugwirizanitsa mfundo zatsopano za m’Malemba ndi zimene mukudziŵa kale?
9 Akristu ochuluka angavomereze kuti panthaŵi ina sanali kudziŵa zambiri ponena za Mulungu, Mawu ake, ndi zifuno zake. Komabe, lero, atumiki achikristu ameneŵa, angathe kufotokoza za chifuno cha nsembe ya Kristu kuyambira pa kulengedwa kwa munthu mpaka pa kugwera kwake mu uchimo, angathe kufotokoza za chiwonongeko cha dongosolo ili la zinthu loipa, ndipo angathe kusonyeza mmene anthu omvera adzadalitsidwira ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Zimenezi nzotheka makamaka chifukwa chakuti atumiki a Yehova ameneŵa ‘amdziŵadi Mulungu’ mwa kuphunzira Baibulo ndi zofalitsa zachikristu. (Miyambo 2:1-5) Pang’ono ndi pang’ono agwirizanitsa mfundo zatsopano zimene aphunzira ndi zakale zimene akuzidziŵa kale.
10 Kugwirizanitsa mfundo zatsopano za Malemba ndi zimene mukudziŵa kale nkothandiza ndi kopindulitsa. (Yesaya 48:17) Pamene malamulo a Baibulo, mapulinsipulo, kapena ngakhale malingaliro ena ochita ngati ovuta kuwamva afotokozedwa, gwirizanitsani zimenezi ndi zimene mukudziŵa kale. Gwirizanitsani chidziŵitsocho ndi zimene mwadziŵa kale ponena za “chitsanzo cha mawu a moyo.” (2 Timoteo 1:13) Fufuzani chidziŵitso chimene chingakuthandizeni kulimbitsa unansi wanu ndi Mulungu, kuwongolera umunthu wanu wachikristu, kapena kukuthandizani kuuza ena choonadi cha Baibulo.
11. Kodi nchiyani chimene mungachite poŵerenga kanthu kena kamene Baibulo limanena ponena za khalidwe? Chitirani fanizo.
11 Pamene muŵerenga kanthu kena kamene Baibulo limanena ponena za khalidwe, yesani kuona pulinsipulo limene likuloŵetsedwamo. Sinkhasinkhanipo, ndi kusankha zimene mungachite pamene muli mu mkhalidwewo. Mwana wa Yakobo, Yosefe anakana mosalekeza kugonana ndi mkazi wa Potifara, akumafunsa kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:7-9) M’nkhani yosonkhezera mtima imeneyi, mumapeza pulinsipulo lalikulu—chisembwere ndilo tchimo kwa Mulungu. Mungagwirizanitse m’maganizo pulinsipulo limeneli ndi mawu ena a m’Mawu a Mulungu, ndipo mungathe kulikumbukira mopindulitsa ngati mungayesedwe kuchita cholakwa.—1 Akorinto 6:9-11.
Onani m’Maganizo Zochitika za m’Malemba
12. Kodi nchifukwa ninji muyenera kuona m’maganizo zochitika za m’Baibulo pamene mukuŵerenga?
12 Kuti mukhomereze mfundo m’maganizo mwanu pamene mukuŵerenga, onani m’maganizo zimene zikuchita. Onani mwamaganizo malo, nyumba, anthu. Imvani mawu awo. Imvani fungo la mkate umene ukuphikidwa pa uvuni. Yerekezerani zochitikazo m’maganizo mwanu. Pamenepo kuŵerenga kwanu kudzakhala kosonkhezera mtima, pakuti mungaone mzinda wakale, kukwera phiri lalitali, kuzizwa ndi chilengedwe chodabwitsa, kapena kuyanjana ndi amuna ndi akazi achikhulupiriro chachikulu.
13. Kodi mungafotokoze motani zimene zalembedwa pa Oweruza 7:19-22?
13 Tinene kuti mukuŵerenga Oweruza 7:19-22. Onani m’maganizo zimene zikuchitika. Woweruza Gideoni ndi amuna olimba mtima mazana atatu a Israyeli aima m’mbuto mwawo kumalekezero a misasa ya Amidyani. Ndi cha ku ma 10 koloko usiku, “poyambira ulonda wapakati.” Alonda a Amidyani angoikidwa kumene, ndipo mdima ukukuta malo a misasa ya adani omagona a Israyeli. Taonani! Gideoni ndi amuna ake ali ndi malipenga. Ali ndi mbiya zazikulu za madzi zokhala ndi miyuni atazigwira m’dzanja lamanzere. Mwadzidzidzi, magulu atatu a zana lililonse akuomba malipenga, kuswa mbiyazo, kutukulira miyuniyo m’mwamba, ndi kufuula kuti: “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni!” Mukuyang’ana kumisasayo. Taonani, Amidyani akuthaŵa nayamba kufuula! Pamene anthu mazana atatuwo akupitirizabe kuomba malipenga awo, Mulungu achititsa Amidyani kumakanthana okhaokha ndi lupanga. Amidyani athaŵa, ndipo Yehova wapatsa Israyeli chilakiko.
Kupeza Maphunziro Ofunika
14. Kodi ndi motani mmene Oweruza chaputala 9 angagwiritsiridwire ntchito kuphunzitsa mwana za kufunika kwa kukhala wodzichepetsa?
14 Mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu, tingathe kuphunzira zambiri. Mwachitsanzo, mwinamwake mukufuna kuti mukhomereze mwa ana anu kufunika kwa kukhala odzichepetsa. Eya, kungakhale kosavuta kuona m’maganizo ndi kupeza tanthauzo la zimene zinanenedwa mu ulosi wa mwana wa Gideoni, Yotamu. Yambani kuŵerenga Oweruza 9:8. “Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu,” anatero Yotamu. Mtengo wa azitona, mtengo wa mkuyu, ndi mpesa inakana kulamulira. Koma nkandankhuku wachabechabe unali wokondwa kukhala wolamulira. Mutaŵerengera ana anu nkhaniyo momveka, mungafotokoze kuti zomera zofunikazo zinaimira anthu oyenera amene sanafune malo achifumu pa Aisrayeli anzawo. Mtengo wa nkandankhuku, umene unali wothandiza pa nkhuni pokha, unaimira ufumu wa Abimeleki wonyada, munthu wambanda amene anafuna kulamulira ena koma anafa mokwaniritsa ulosi wa Yotamu. (Oweruza, chaputala 9) Kodi ndi mwana wamtundu wanji amene angafune kukula ndi kukhala ngati nkandankhuku?
15. Kodi kufunika kwa kukhulupirika kwasonyezedwa motani m’buku la Rute?
15 Kufunika kwa kukhulupirika kumasonyezedwa bwino m’buku la Baibulo la Rute. Tinene kuti a m’banja lanu akulandizana kuŵerenga momveka nkhani imeneyo ndi kuyesa kuloŵetsa mumtima zimene ikunena. Mukuona Rute Mmoabu ali paulendo kumka ku Betelehemu ndi apongozi ake amasiye, a Naomi, ndipo mukumva Rute akuti: “Anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Rute wokangalikayo akuonedwa akukunkha pambuyo pa otuta m’munda wa Boazi. Mukumumva akumuyamikira, akumati: “Onse apamudzi wa anthu a mtundu wanga adziŵa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.” (Rute 3:11) Posapita nthaŵi, Boazi akukwatira Rute. Mogwirizana ndi makonzedwe a ukwati wapachilamu, mkaziyo ndi Boazi akubalira mwana “kwa Naomi.” Rute akukhala kholo la Davide ndipo potsirizira pake la Yesu Kristu. Motero iye analandira “mphotho yokwanira.” Ndiponso, awo amene amaŵerenga nkhani ya m’Malembayi amapezapo phunziro lofunika: Khalani okhulupirika kwa Yehova, ndipo mudzadalitsidwa kwambiri.—Rute 2:12; 4:17-22; Miyambo 10:22; Mateyu 1:1, 5, 6.
16. Kodi Ahebri atatu anakumana ndi chiyeso chotani, ndipo nkhani imeneyi ingatithandize motani?
16 Nkhani ya Ahebri otchedwa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego ingatithandize kukhala okhulupirika kwa Mulungu m’mikhalidwe yoyesa. Onani m’maganizo chochitikacho pamene mukuŵerenga momveka Danieli chaputala 3. Fano lalikulu lagolidi lili thobo pachigwa cha Dura, kumene akuluakulu aboma a Babulo asonkhana. Pakumveka kwa ziŵiya za nyimbo, akugwada ndi kulambira fano limene Mfumu Nebukadinezara waliimika. Ndiko kuti, onse akuchita motero kusiyapo Sadrake, Mesake ndi Abedinego. Mwaulemu, koma mwamphamvu, iwo akuuza mfumu kuti sadzatumikira milungu yake ndi kulambira fano lagolidilo. Ahebri achichepere ameneŵa akuponyedwa m’ng’anjo yotentha yamoto. Koma kodi nchiyani chimene chikuchitika? Itayang’ana mkatimo, mfumu ikuona amuna anayi, mmodzi wa iwo “akunga mwana wa milungu.” (Danieli 3:25) Ahebri atatuwo akutulutsidwa m’nganjo, ndipo Nebukadinezara akulemekeza Mulungu wawo. Kuona m’maganizo chochitikacho kwakhala kofupa. Ndipo zimenezi zimapereka phunziro lofunika chotani nanga ponena za kukhulupirika kulinga kwa Yehova pansi pa chiyeso!
Pindulani ndi Kuŵerenga Baibulo Monga Banja
17. Tchulani mwachidule zinthu zina zopindulitsa zimene banja lanu lingaphunzire mwa kuŵerengera Baibulo pamodzi.
17 Banja lanu lingathe kupeza mapindu ambiri ngati muthera nthaŵi mukuŵerenga Baibulo pamodzi nthaŵi zonse. Kuyambira ku Genesis, mukhoza kuona chilengedwe ndi kusuzumira m’mudzi woyamba wa munthu wa Paradaiso. Mungathe kukhala ndi phande m’zochitika za makolo okhulupirika ndi mabanja awo ndi kutsatira Aisrayeli pamene akuwoloka pouma pa Nyanja Yofiira. Mungathe kuona mnyamata mbusayo Davide akugonjetsa chimphona cha Afilisticho Goliati. Banja lanu lingathe kuona kumangidwa kwa kachisi wa Yehova mu Yerusalemu, lingathe kuona kupasulidwa kwake ndi magulu a Ababulo, ndipo lingathe kuona kumangidwanso kwake pansi pa Kazembe Zerubabele. Muli limodzi ndi abusa wamba pafupi ndi Betelehemu, mungathe kumva chilengezo cha mngelo cha kubadwa kwa Yesu. Mungathe kupeza tsatanetsatane wa ubatizo wake ndi utumiki wake, mungathe kumuona akupereka moyo wake waumunthu kaamba ka dipo, ndipo nanunso mungathe kukondwa nako kuuka kwake. Kenako, mungathe kuyenda ulendo ndi mtumwi Paulo ndi kuona kukhazikitsidwa kwa mipingo pamene Chikristu chikuwanda. Ndiyeno, m’buku la Chivumbulutso, banja lanu lingaone masomphenya aakulu a Yohane a zinthu zamtsogolo, kuphatikizapo Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi.
18, 19. Kodi ndi malingaliro otani amene akuperekedwa ponena za kuŵerenga Baibulo kwa banja?
18 Ngati mukuŵerenga Baibulo momveka monga banja, liŵerengeni momveka bwino ndiponso motenthedwa maganizo. Poŵerenga zigawo zina za Malemba, wa m’banja wina—mwinamwake atate—angaŵerenge mawu ofotokoza nkhaniyo. Ena a inu mungakhale anthu a m’Baibulo, mukumaŵerenga mbali zanu mwaumoyo woyenera.
19 Pamene muŵerenga ndi ena Baibulo monga banja, luso lanu la kuŵerenga lingawongokere. Mwachionekere, kudziŵa kwanu Mulungu kudzawonjezereka, ndipo zimenezi ziyenera kukuchititsani kuyandikira kwambiri kwa iye. Asafu anaimba kuti: “Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu: ndimuyesa Ambuye Yehova pothaŵirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.” (Salmo 73:28) Zimenezi zidzathandiza banja lanu kukhala ngati Mose, amene “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo,” ndiko kuti, Yehova Mulungu.—Ahebri 11:27.
Kuŵerenga ndi Utumiki Wachikristu
20, 21. Kodi ntchito yathu ya kulalikira njogwirizana motani ndi luso la kuŵerenga?
20 Chikhumbo chathu cha kulambira “Wosaonekayo” chiyenera kutisonkhezera kulimbikira kukhala oŵerenga abwino. Luso la kuŵerenga bwino limatithandiza kuchitira umboni kuchokera m’Mawu a Mulungu. Limatithandizadi kupitirizabe mu ntchito yolalikira Ufumu imene Yesu analamulira otsatira ake kuchita pamene anati: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Kuchitira umboni ndiko ntchito yaikulu ya anthu a Yehova, ndipo luso la kuŵerenga limatithandiza kukwaniritsa zimenezi.
21 Kuyesayesa kuli kofunika kuti munthu akhale woŵerenga wabwino ndi mphunzitsi waluso wa Mawu a Mulungu. (Aefeso 6:17) Chotero, ‘chitani changu kudzionetsera kwa Mulungu ovomerezeka, olunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:15) Wonjezerani chidziŵitso chanu cha choonadi cha Malemba ndi luso lanu monga Mboni ya Yehova mwa kudzipereka pa kuŵerenga.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi chimwemwe chimadalira motani pa kuŵerenga Mawu a Mulungu?
◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kusinkhasinkha zimene mukuŵerenga m’Baibulo?
◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kugwirizanitsa mfundo ndiponso kuona zinthu m’maganizo pamene mukuŵerenga Malemba?
◻ Kodi ndi maphunziro ena otani amene angapezedwe m’kuŵerenga Baibulo?
◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kuŵerenga Baibulo momveka monga banja, ndipo ndi kugwirizana kotani kumene kulipo pakati pa kuŵerenga ndi utumiki wachikristu?
[Zithunzi patsamba 13]
Pamene mukuŵerenga Baibulo monga banja, onani m’maganizo zochitikazo ndi kusinkhasinkha tanthauzo lake