Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 7/1 tsamba 3-4
  • Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwamtundu Uliwonse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwamtundu Uliwonse?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulambira Kokayikitsa m’Nthaŵi Zakale
  • Kulambira Koyera Kuipitsidwa
  • Kulambira Baala Nkhondo Yosatha M’mitima mwa Aisrayeli
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Sanasunthike Pakulambira Koona
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Ino Ndi Nthawi Yofunika Kuchitapo Kanthu Mwachangu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Sanasunthike pa Kulambira Koona
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 7/1 tsamba 3-4

Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwamtundu Uliwonse?

MULUNGU analenga munthu ndi chikhumbo chauzimu​—chikhumbo cha kulambira. Sichinakhaleko mwa chisinthiko. Chinali mbali ya munthu kuyambira pachiyambi.

Komabe, nzachisoni kuti anthu apanga njira zolambirira zambiri ndi zosiyanasiyana, ndipo kaŵirikaŵiri, zimenezi sizinachititse banja laumunthu kukhala logwirizana ndi lachimwemwe. M’malo mwake, nkhondo zokhetsa mwazi zikumenyedwabe m’dzina la chipembedzo. Zimenezi zikubutsa funso lofunikali: Kodi njira imene munthu amalambiriramo Mulungu ili ndi ntchito?

Kulambira Kokayikitsa m’Nthaŵi Zakale

Mitundu yakale imene inali kukhala ku Middle East imatipatsa chitsanzo cha m’mbiri chimene chimatithandiza kuyankha funsolo. Ambiri anali kulambira mulungu wotchedwa Baala. Anali kulambiranso anzake a Baala achikazi, monga Asherah. Kulambira Asherah kunaphatikizapo kugwiritsira ntchito mlongoti wopatulika umene amati unali chizindikiro cha kugonana. Akatswiri ofukula mabwinja ogwira ntchito kuderalo afukula mafano ambiri a akazi amaliseche. Mafano ameneŵa, imatero The Encyclopedia of Religion, “amasonyeza mulungu wachikazi amene ali ndi mpheto yaikulu kwambiri, atagwiririra maŵere ake,” ndipo “mwinamwake amaimira . . . Asherah.” Koma chinthu chimodzi nchotsimikizirika, nthaŵi zambiri kulambira Baala kunali kwachisembwere kwambiri.

Chifukwa chake, nzosadabwitsa kuti kulambira Baala kunaphatikizapo madzoma akugonana. (Numeri 25:1-3) Sekemu, Mkanani, anagwirira chigololo namwali wachichepereyo Dina. Mosasamala kanthu za zimenezo, anaonedwabe kukhala wolemekezeka koposa m’banja lawo. (Genesis 34:1, 2, 19) Kugonana ndi wachibale, mathanyula, ndi kugona nyama kunali kofala. (Levitiko 18:6, 22-24, 27) Liwu lachingelezilo “sodomy,” zimene amathanyula amachita, linatengedwa ku dzina la mzinda umene unaliko kale kudera limenelo la dziko. (Genesis 19:4, 5, 28) Kulambira Baala kunaphatikizaponso kukhetsa mwazi. Inde, olambira Baala anali kuponya ana awo amoyo m’moto wolilima monga nsembe kwa milungu yawo! (Yeremiya 19:5) Machitachita onsewa anali mbali ya ziphunzitso zachipembedzo. Motani?

“Nkhalwe, chilakolako cha kugonana ndi kusadziletsa za m’nthanthi za Akanani,” akutero Dr. Merrill Unger m’buku lake lakuti Archaeology and the Old Testament, “nzoipitsitsa kwambiri kuposa kwina kulikonse panthaŵiyo ku Near East. Ndipo mkhalidwe wapadera wa milungu ya Akanani, wakuti inalibiretu makhalidwe, uyenera kuti unachititsa olambira ake kukhala ndi mikhalidwe yoipitsitsa ndi kusonkhezera machitachita onyansitsa ambiri apanthaŵiyo, monga uhule wopatulika, [ndi] kupereka ana nsembe.”

Kodi Mulungu anavomereza kulambira kwa Akanani? Sanatero ayi. Iye anaphunzitsa Aisrayeli njira yoyera yomlambiriramo. Ponena za machitachita otchulidwawo, iye anachenjeza kuti: “Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; pakuti amitundu amene ndiwapitikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi; dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala mmwemo.”​—Levitiko 18:24, 25.

Kulambira Koyera Kuipitsidwa

Aisrayeli ambiri sanavomereze lingaliro la Mulungu la kulambira koyera. M’malo mwake, analola kulambira Baala kupitiriza m’dziko lawo. Posapita nthaŵi, Aisrayeli anakopeka nayesa kusanganiza kulambira kwa Yehova ndi kuja kwa Baala. Kodi Mulungu anavomereza kulambira kosanganizikana kumeneko? Talingalirani zimene zinachitika mu ulamuliro wa Mfumu Manase. Iye anamangira Baala maguwa a nsembe, anatentha mwana wake monga nsembe, ndipo anachita matsenga. “Ndipo anaika chifanizo chosema [cha mlongoti wopatulika, NW] [ʼashe·rahʹ m’Chihebri] chimene adachipanga m’nyumba ija Yehova adainenera . . . kuti, M’nyumba muno . . . ndidzaikamo dzina langa kosatha.”​—2 Mafumu 21:3-7.

Anthu a Manase anatsatira chitsanzo cha mfumu yawo. Kwenikweni, iye “[a]nawachititsa choipa, kuposa amitundu amene Yehova adawawononga pamaso pa ana a Israyeli.” (2 Mafumu 21:9) M’malo molabadira machenjezo obwerezabwereza operekedwa ndi aneneri a Mulungu, Manase anachita mbanda kwakuti anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa. Ngakhale kuti Manase analapa pambuyo pake, mwana wake ndi womloŵa m’malo, Mfumu Amoni, anayambitsanso kulambira Baala.​—2 Mafumu 21:16, 19, 20.

M’kupita kwa nthaŵi, mahule achimuna anayamba kuchitira uchisi wawo m’kachisi. Kodi Mulungu anauona motani mchitidwe umenewu wa kulambira Baala? Kupyolera mwa Mose, anali atachenjeza kuti: “Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu [mwachionekere wogona anyamata] kuloŵa nazo m’nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha choŵinda chilichonse; pakuti onse aŵiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nawo.”​—Deuteronomo 23:17, 18.

Mdzukulu wa Manase, Mfumu Yosiya, anayeretsa kachisi kuchotsamo kulambira Baala kwachisembwereko. (2 Mafumu 23:6, 7) Koma zinthu zinali zitafika poipitsitsa. Posapita nthaŵi kuchokera pa imfa ya mfumu Yosiya, kulambira mafano kunayambanso kuchitika m’kachisi wa Yehova. (Ezekieli 8:3, 5-17) Chotero Yehova anachititsa mfumu ya Babulo kuwononga Yerusalemu ndi kachisi wake. Chochitika chomvetsa chisoni cha m’mbiri chimenechi ndicho umboni wakuti mitundu ina ya kulambira siili yovomerezeka kwa Mulungu. Bwanji nanga za m’tsiku lathu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena