Olengeza Ufumu Akusimba
Thandizo kwa ‘Aludzu’ ku Russia
“ODALA ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta,” anatero Yesu. (Mateyu 5:6) Zokumana nazo zotsatira zikusonyeza mmene Mboni za Yehova zikuthandizira kukhutiritsa ludzu lauzimu la ambiri ku Russia, kumene kunalibe ufulu wa chipembedzo kwa zaka zoposa 70.
▪ Mkazi wina wotchedwa Valentina anali ndi mafunso aakulu a Baibulo amene anakhala osayankhidwa kwa zaka zambiri. Mwachitsanzo, ankadzifunsa kuti: ‘Kodi Yesu anapemphera kwa yani?’ Analingalira kuti ayenera kukhala atapemphera kwa wina wake wamkulu kuposa iye ndipo anadzifunsa za dzina la Ameneyu.
Anapita ku Tchalitchi cha Russian Orthodox. Komabe, sanapeze mayankho a mafunso ake m’tchalitchi chimenecho. Posakhutira, anapita kutchalichi china chachiprotesitanti komanso sanapeze mayankho omveka. Posadziŵa kwinanso kopita, Valentina anayamba kuŵerenga Baibulo, akumayesa kudzipezera mayankho—mosaphula kanthu. Anapempherera thandizo.
Nthaŵi ina pambuyo pake Mboni za Yehova zinagogoda pachitseko pake. Zinamsonyeza m’Baibulo kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova. Pomalizira pake anadziŵa kumene Yesu anapempherako! Anayamba kuphunzira Baibulo mokhazikika ndi Mbonizo. Nthaŵi zambiri ankakhala maso usiku wonse akumaŵerenga mabuku ofalitsidwa ndi Watch Tower Society ndi kuŵerenga mavesi a m’Baibulo. Posapita nthaŵi Valentina anadziŵa kuti wapeza choonadi. M’miyezi itatu anayamba kuchita nawo ntchito yolalikira, ndipo patapita miyezi iŵiri, anabatizidwa. Kufunafuna kwake choonadi mwa pemphero kunafupidwa.
▪ Mboni ina inayenda pa basi kukalalikira kudera lakumidzi. Paulendowo inakambitsirana ndi mtsikana wina za malonjezo a Baibulo, koma mtsikanayo analibe chidwi. Patapita miyezi iŵiri Mboniyo inapanga ulendo wachiŵiri kudera limodzimodzilo kukapereka nkhani yapoyera. Pambuyo pa nkhaniyo inafikira mlendo wina ndi kumfunsa kuti: “Kodi pali amene walankhula nanu kale za uthenga wabwino wa m’Baibulo?” Mwamunayo anayankha kuti, “Inde, inuyo mwatero.” Mboniyo inayesa kuti akupanga nthabwala. Koma mwamunayo anafotokoza kuti miyezi iŵiri poyambapo anali atamvetsera kukambitsirana kwa pakati pa Mboniyo ndi mtsikanayo, paulendo wa pa basi. “Ndinafuna kudziŵa zowonjezereka, koma munatsika m’basi, ndipo ndinaganiza kuti sindidzaonanso Mboni za Yehova. Ndiyeno kuntchito kwanga ndinakumana ndi mwamuna wina amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni. Choncho ndine ndili pano!”
Mwamunayo ndi mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo. Patapita nthaŵi yaifupi kwambiri, anaona kuti ntchito yake inali kutsutsana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Pofuna kukhala ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu, iye anasintha ntchito yake. Tsopano akuuza ena za Ufumu wa Mulungu pampata uliwonse. Mkazi wake nayenso akupita patsogolo m’maphunziro ake a Baibulo.
Mboni za Yehova m’gawo lalikululo la Russia zili zokondwera kukhala ndi phande pa kunena kwa anthu onse kuti: “Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”—Chivumbulutso 22:17.