Tiyenera kulota
KODI mumalota? Tinganene motsimikiza kuti mumatero, pakuti ife tonse timalota pamene tili m’tulo, ngakhale ngati tinganene kuti sitimatero. Kwayerekezeredwa kuti maloto oposa 95 peresenti samakumbukika. Kodi mumakumbukira ati? Kwenikweni, amene timakumbukira ndi aja amene timalota titangotsala pang’ono kudzuka.
Ofufuza za maloto apeza kuti tulo timachitika pang’onopang’ono, tikumakhala tatikulu koposa m’maola oŵerengeka oyambirira ndiyeno nkumachepa pambuyo pake. Maloto amachitika makamaka mkati mwa nyengo ya rapid eye movement (kuyendayenda kwa maso munthu atagona), yotchedwa tulo ta REM. Imeneyi imasinthana ndi nyengo ya tulo tosakhala ta REM. Nyengo iliyonse ya tulo tosakhala ta REM/tulo ta REM imatenga mphindi 90, ndipo nyengo zimenezi zimabwerezedwa nthaŵi zisanu kapena zisanu ndi imodzi usiku, yotsirizira ikumachitika titangotsala pang’ono kudzuka.
Nkulakwa kuganiza kuti ubongo wanu sumagwira ntchito kwambiri pamene muli m’tulo. Kwapezeka kuti ubongo umagwira ntchito kwambiri polota kuposa nyengo zina pamene munthu ali maso, kusiyapo ma neuron ena m’tsinde la ubongo amene amachita ndi kuganiza ndi kukumbukira. Zikuchita ngati kuti ameneŵa amakhala akupuma mkati mwa tulo ta REM. Koma maselo a minyewa ya mauthenga mu ubongo amapitiriza kugwira ntchito.
Ubongo wathu uli mbali yocholoŵana koposa m’thupi, ndipo uli ndi zinthu mabiliyoni ambiri zimene zimatumiza mauthenga pafupifupi nthaŵi zana limodzi mpaka mazana aŵiri kapena atatu pasekondi imodzi. Ubongo wa munthu uli ndi zinthu zambiri kuposa chiŵerengero cha anthu onse padziko lapansi. Ofufuza ena amayerekezera kuti uli ndi zinthu kuyambira 20 biliyoni mpaka zoposa 50 biliyoni. Kucholoŵana kwake kumatsimikiza zimene wolemba Baibulo wina Davide ananena pa thupi la munthu kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu nzodabwiza.”—Salmo 139:14.
Dziko la Maloto
Pamene tili maso, mphamvu zathu zisanu zakuzindikira zimapereka mauthenga ndi zithunzi ku ubongo nthaŵi zonse, koma pamene tili m’tulo zimenezi sizimachitika. Ubongo umadzipangira zithunzi popanda kulandira mauthenga alionse akunja. Chifukwa chake, zimene timaona ndi zochitika m’maloto nthaŵi zina zimachita ngati kuti ndi zideruderu. Zimenezi zimatitheketsa kuchita zinthu zowombana ndi malamulo achibadwa, monga kuuluka ngati Peter Pan kapena kugwa pa therezi popanda kuvulala. Nthaŵi ingasokonezeke kwakuti kale lingaoneke ngati lero. Kapena ngati tikuyesa kuthaŵa, timachita ngati tikulephera kulamulira thupi kuyenda—miyendo yathu ikumakana kuyenda. Ndithudi, zinthu zochititsa nthumanzi kwambiri ndi zochitika zimene tingakumane nazo pamene tili maso zimabwera m’maloto athu. Ambiri amene anaonapo nkhanza yowopsa ya nkhondo satha kuiŵala msanga, ndipo ena sangaiŵale mantha a kuukiridwa ndi mpandu. Zochitika zosautsa zimenezo pamene tili maso zingabwere m’maloto athu, zikumabweretsa maloto oipa. Zinthu wamba zimene timakhala tikuganiza popita kukagona zingatulukire m’maloto athu.
Nthaŵi zina pamene tikuyesa kuthetsa vuto, yankho lake limadza pamene tili m’tulo. Zimenezi zikusonyeza kuti si tulo tonse timene timakhala maloto. Mbali yake ina imakhala ya kuganiza.
Buku lina lonena za maloto ndi ubongo wathu likuti: “Mtundu wofala koposa wa ntchito ya maganizo kutulo si kulota ayi koma kuganiza. Kuganiza kutulo sikumakhala koona zideruderu ndipo sikochititsa nthumanzi. Kumachitikachitika, nthaŵi zambiri kumakhudza zochitika zenizeni m’moyo za dzulo kapena maŵa, ndipo kaŵirikaŵiri kumakhala kosasangalatsa, kopanda luso la kuganiza, ndi kobwerezabwereza.”
Anthu ena amaganiza kuti zimene amalota zili ndi mauthenga awo apadera. Kuti apeze tanthauzo la maloto, iwo amasunga kabuku ka manotsi pambali pa kama wawo kuti aziwalemba atadzuka. Ponena za phindu la mabuku amene amayesa kutanthauzira zizindikiro za maloto, The Dream Game, lolembedwa ndi Ann Faraday, likuti: “Mabuku a maloto amene mumayang’anamo tanthauzo la zochitika m’maloto ndi zizindikiro zake alinso opanda pake, kaya akhale amwambo kapena ozikidwa pa chiphunzitso china chamakono cha zamaganizo.”
Popeza zikuoneka kuti maloto kwenikweni amayambira mu ubongo, sikuli kwanzeru kuganiza kuti amakhala ndi mauthenga apadera kwa ife. Tiyenera kuwaona monga njira yachibadwa imene ubongo umagwirira ntchito, imenenso imauthandiza kukhala mumkhalidwe wabwino.
Koma bwanji ponena za aja amene amati analota za imfa ya wachibale kapena bwenzi lawo napeza kuti tsiku lotsatira munthuyo wamwalira? Kodi zimenezo sizimasonyeza kuti maloto angalosere mtsogolo? M’nkhani yotsatira, tidzapenda mphamvu yochirikiza maloto aulosi.