Maloto
Tanthauzo: Maganizo kapena zithunzi zamaganizo za munthu m’nthaŵi ya kugona. Baibulo limatchula maloto wamba, maloto ochokera kwa Mulungu, ndi maloto ophatikizapo kuombeza.—Yobu 20:8; Num. 12:6; Zek. 10:2.
Kodi maloto m’nthaŵi yathu ali ndi tanthauzo lapadera?
Kodi nchiyani chimene ofufuza apeza ponena za maloto?
“Munthu aliyense amalota,” ikutero The World Book Encyclopedia (1984, Vol. 5, p. 279). “Achikulire ambiri amalota pafupifupi mphindi 100 mkati mwa tulo ta maora asanu ndi atatu.” Chotero maloto ali chokumana nacho chozoloŵereka cha anthu.
Dr. Allan Hobson, wa ku Harvard Medical School anati: “Ali chochitika chosatsimikizirika chimene chingatathauziridwe mwanjira iriyonse imene wotanthauzirayo wakhotererako. Koma tanthauzo lawo liri kwa munthu wolotayo—osati m’loto lenilenilo.” Posimba mfundoyi, “Science Times” chigawo cha The New York Times inawonjezera kuti: “M’masukulu amene amaika chigogomezero chachikulu pamaloto, muli njira zambiri zopezera tanthauzo lamaganizo la maloto, iriyonse ikumasonyeza mipangidwe ya nthanthi zosiyanasiyana. Wotsatira njira ya Freud adzapeza tanthauzo la mtundu wakuti m’loto, pamene wotsatira Jungi adzapeza lina ndipo Mgestalt womasulira maloto adzapenso tanthauzo lina. . . . koma lingaliro lakuti maloto ali ndi tanthauzo lirilonse lophatikizapo maganizo latsutsidwa kwambiri ndi asayansi odziŵa mitsempha.”—July 10, 1984, p. C12.
Kodi maloto amene amawonekera kukhala opereka chidziŵitso chapadera angachokere kumagwero ena osakhala kwa Mulungu?
Yer. 29:8, 9: “Pakuti Yehova wamakamu . . . atero: Aneneri anu ndi akuwombedza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa. Pakuti anenera kwa inu zonama m’dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.”
Harper’s Bible Dictionary limatiuza kuti: “Ababulo anali ndi chidaliro chachikulu m’maloto kotero kuti nyengo za kupanga zosankha zofunika anagona mu akachisi, kuyembekezera uphungu. Agiriki okhumba malangizo a zaumoyo anagona m’tiakachisi ta Aesculapius [amene chizindikiro chake chinali njoka], ndipo Aroma mu akachisi a Serapis [panthaŵi zina anagwirizana ndi njoka youmba nkhata]. Aigupto analemba mabukhu ochuluka omasulira maloto.”—(New York, 1961), Madeleine Miller ndi J. Lane Miller, p. 141.
M’nthaŵi zakale, Mulungu anagwiritsira ntchito maloto kupereka machenjezo, malangizo, ndi ulosi, koma kodi iye akutsogoza anthu ake mwanjirayo patsopano lino?
Maumboni osonya kumaloto ochokera kwa Mulungu akupezeka pa Mateyu 2:13, 19, 20; 1 Mafumu 3:5; Genesis 40:1-8.
Aheb. 1:1, 2: “Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri [kuphatikizapo maloto] ndi mosiyanasiyana, koma pakutha pake pa masiku ano analankula ndi ife ndi Mwana [Yesu Kristu, amene ziphunzitso zake zalembedwa m’Baibulo].”
1 Akor. 13:8: “Kapena zonenera [ndipo nthaŵi zina Mulungu anapereka maulosi kwa atumiki ake kupyolera mwa maloto], zidzakhala chabe.”
2 Tim. 3:16, 17: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso . . . kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.”
1 Tim. 4:1, NW: “Komabe, mawu ouziridwa amanenadi kuti masiku otsiriza ena adzagwa m’chikhulupiriro, akumamvera mawu ndi ziphunzitso zouziridwa [nthaŵi zina zoperekedwa m’maloto] zosocheza zaziŵanda.”