‘Cherezani Alendo’
‘Patsani zosoŵa oyera mtima; cherezani alendo.’—AROMA 12:13.
1. Kodi chachikulu chimene anthu amafuna nchiyani, ndipo kodi chimaonekera motani?
KUYENDA m’khwalala lopanda anthu usiku kumalo achilendo kungakhale kochititsa mantha masiku ano. Koma kungakhalenso kovutitsa maganizo mofananamo kukhala pakati pa gulu ndi kusadziŵapo aliyense kapena inuyo kusadziŵidwa. Zoonadi, mbali yofunika ya umunthu ndiyo kufuna kusamaliridwa, kufunidwa, ndi kukondedwa. Palibe amene amafuna kuchitiridwa monga mlendo kapena wakwina.
2. Kodi Yehova wasamalira motani kufuna kwathu ubwenzi?
2 Yehova Mulungu, Mpangi ndi Mlengi wa zinthu zonse, amadziŵa bwino lomwe kuti munthu amafuna ubwenzi. Monga Wolinganiza wa chilengedwe chake cha anthu, kuyambira pachiyambi penipenipo Mulungu anadziŵa kuti sikunali “kwabwino kuti munthu akhale yekha,” ndipo anachitapo kanthu. (Genesis 2:18, 21, 22) Mbiri ya m’Baibulo njodzaza zitsanzo za zochita zachifundo zimene Yehova ndi atumiki ake anachitira anthu. Zimenezi zimatikhozetsa kuphunzira ‘mocherezera alendo,’ kusangalatsa ndi kukondweretsa ena ndi kupeza chikhutiro ife eni.—Aroma 12:13.
Kukonda Alendo
3. Fotokozani tanthauzo lapafupi la kuchereza alendo.
3 Liwulo “kuchereza alendo” monga momwe lagwiritsidwira ntchito m’Baibulo latembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki lakuti phi·lo·xe·niʹa, lopangidwa ndi mawu aŵiri otanthauza “chikondi” ndi “mlendo.” Chotero, kuchereza alendo kumangotanthauza “kukonda alendo.” Komabe, kuchita zimenezi sindiko mwambo kapena khalidwe labwino chabe. Kumaphatikizapo malingaliro ndi mtima wa munthu. Verebulo phi·leʹo, malinga ndi kunena kwa Exhaustive Concordance of the Bible ya James Strong, limatanthauza “kukhala bwenzi la (kukonda [munthu kapena chinthu]), ndiko kuti kukhala ndi chikondi cha pa (kutanthauza kukonda kochokera mumtima).” Chotero kuchereza alendo kumaposa chikondi chozikidwa pa lamulo, mwinamwake chosonyezedwa chifukwa cha thayo. Kaŵirikaŵiri ndiko chisonyezero cha chikondi ndi ubwenzi weniweni.
4. Kodi kuchereza alendo kuyenera kusonyezedwa kwa yani?
4 Amene amasonyezedwa chikondi chimenechi ndi “mlendo” (Chigiriki, xeʹnos). Kodi ameneyu angakhale yani? Kachiŵirinso, Concordance ya Strong ikutanthauzira liwulo xeʹnos monga ‘wochokera kwina (kwenikweni wachilendo, kapena watsopano mofanizira); kutanthauza woitanidwa kapena (mwa njira ina) mlendo.’ Chotero kuchereza alendo, malinga ndi zitsanzo zomwe Baibulo limapereka, kungasonyeze kukomera mtima winawake amene timakonda, kapena kungasonyezedwe ngakhale kwa munthu amene ali mlendo weniweni. Yesu anafotokoza kuti: “Ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho? Ndipo ngati mulankhula abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho?” (Mateyu 5:46, 47) Kuchereza alendo kwenikweni kumagonjetsa magaŵano ndi tsankhu limene kukondera ndi mantha zimachititsa.
Yehova, Wochereza Alendo Wangwiro
5, 6. (a) Kodi Yesu anali kulingaliranji pamene anati, “Atate wanu wakumwamba ali wangwiro”? (b) Kodi kuoloŵa manja kwa Yehova kumaonekera motani?
5 Atasonyeza kupereŵera kwa chikondi chosonyezedwa ndi anthu kwa wina ndi mnzake, monga momwe mawu a pamwambapo akusonyezera, Yesu anawonjezera mawuŵa: “Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wakumwamba ali wangwiro.” (Mateyu 5:48) Zoona, Yehova ndi wangwiro m’zinthu zonse. (Deuteronomo 32:4) Komabe, Yesu anali kusonyeza mbali imodzi makamaka ya ungwiro wa Yehova, monga momwe ananenera poyamba kuti: “[Mulungu] amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:45) Ponena za kusonyeza kukoma mtima, Yehova samasankha.
6 Monga Mlengi, Yehova ndiye mwini wa zinthu zonse. “Zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng’ombe za pamapiri zikwi. Ndidziŵa mbalame zonse za m’mapiri: ndipo nyama za kuthengo zili ndi ine,” akutero Yehova. (Salmo 50:10, 11) Ngakhale ndi tero, palibe chimene amabisa mwadyera. Ndi kuoloŵa manja kwake, amapatsa zolengedwa zake zonse zofuna zawo. Wamasalmo anati ponena za Yehova: “Muoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.”—Salmo 145:16.
7. Kodi tingaphunzirenji pa njira imene Yehova amachitira ndi alendo ndi osoŵa?
7 Yehova amapatsa anthu zofunika zawo—ngakhale anthu amene samamdziŵa, amene ali alendo kwa iye. Paulo ndi Barnaba anakumbutsa olambira mafano mumzinda wa Lustra kuti Yehova “sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.” (Machitidwe 14:17) Makamaka kwa aja osoŵa, Yehova ali wokoma mtima ndi wooloŵa manja. (Deuteronomo 10:17, 18) Pali zambiri zimene tingaphunzire kwa Yehova pa kusonyeza kukoma mtima ndi kuoloŵa manja—kukhala wochereza alendo—kwa ena.
8. Kodi Yehova wasonyeza motani kuoloŵa manja kwake posamalira zosoŵa zathu zauzimu?
8 Kuwonjezera pa kupatsa zolengedwa zake zinthu zakuthupi zochuluka zofunikira, Yehova amasamalira zofunika zawo m’njira yauzimu. Yehova anachita mokoma mtima koposa kaamba ka ubwino wathu wauzimu, ngakhale pamene aliyense wa ife sanadziŵe kuti tinali mumkhalidwe wauzimu wodetsa nkhaŵa kwambiri. Timaŵerenga pa Aroma 5:8, 10 kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife. . . . Pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake.” Makonzedwe amenewo amatheketsa anthu ochimwa kuloŵa mu unansi wachimwemwe wa banja ndi Atate wathu wakumwamba. (Aroma 8:20, 21) Yehova anatsimikiziranso kuti tapatsidwa chitsogozo ndi malangizo abwino kotero kuti tipambane m’moyo mosasamala kanthu za mkhalidwe wathu wauchimo ndi wopanda ungwiro.—Salmo 119:105; 2 Timoteo 3:16.
9, 10. (a) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yehova ndiye wochereza alendo wangwiro? (b) Kodi olambira oona ayenera kumtsanzira motani Yehova pankhaniyi?
9 Chifukwa cha zimenezi, tinganene kuti Yehova alidi wochereza alendo wangwiro m’njira zambiri. Samanyalanyaza osoŵa ndi apansi. Amakondweradi ndi alendo, ngakhale adani ake, ndi kuwaderadi nkhaŵa, ndipo samafuna mphotho iliyonse yakuthupi. Pa zinthu zonsezi, kodi sindiye chitsanzo chabwino koposa cha wochereza alendo wangwiro?
10 Monga Mulungu wa kukoma mtima ndi kuoloŵa manja kotero, Yehova amafuna kuti olambira ake amtsanzire. M’Baibulo lonse, timaona zitsanzo zapadera za mkhalidwe wachifundo umenewu. Encyclopaedia Judaica imanena kuti “m’Israyeli wakale, kuchereza alendo sikunali chabe nkhani ya khalidwe labwino, koma chizoloŵezi chapadera cha makhalidwe abwino . . . Miyambo ya m’Baibulo ya kulandira wapaulendo wotopa ndi ya kulandira mlendo pakati pawo ndiyo inali magwero a kuchereza alendo ndi mbali zake zonse zofanana kukhala mkhalidwe wabwino wofunika koposa pa mwambo wachiyuda.” M’malo mokhala mkhalidwe wapadera wa mtundu kapena fuko lakutilakuti, kuchereza alendo kuyenera kukhala mkhalidwe wa olambira oona onse a Yehova.
Wochereza Angelo
11. Kodi ndi chitsanzo chiti chapadera chimene chikusonyeza kuti kuchereza alendo kunadzetsa madalitso osayembekezereka? (Onaninso Genesis 19:1-3; Oweruza 13:11-16.)
11 Imodzi ya nkhani za m’Baibulo zodziŵika kwambiri za kusonyeza mkhalidwe wa kuchereza alendo ndiyo ija ya Abrahamu ndi Sara pamene anaimika mahema pakati pa mitengo yaikulu ya ku Mamre, pafupi ndi Hebroni. (Genesis 18:1-10; 23:19) Mosakayikira mtumwi Paulo anali kulingalira za chochitika chimenechi pamene anapereka uphungu uwu wakuti: “Musaiŵale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziŵa.” (Ahebri 13:2) Kuphunzira nkhaniyi kudzatithandiza kuona kuti kuchereza alendo si nkhani ya mwambo kapena makulidwe a munthu chabe. M’malo mwake, ndi mkhalidwe waumulungu umene umadzetsa madalitso abwino kwambiri.
12. Kodi Abrahamu anasonyeza motani chikondi chake cha pa alendo?
12 Genesis 18:1, 2 amasonyeza kuti alendowo anali osadziŵika kwa Abrahamu ndipo sanali kuwayembekezera, anali monga chabe alendo atatu okhala paulendo kupita kwina. Mwambo pakati pa anthu Akummaŵa, malinga ndi kunena kwa akatswiri ena, unali wakuti wapaulendo m’dziko lachilendo anayenera kuyembekezera kulandiridwa ngakhale kuti sanali kudziŵa aliyense kumeneko. Koma Abrahamu sanayembekezere kuti alendowo agwiritsire ntchito ufulu umenewu; anayambirira kuchitapo kanthu. ‘Anathamanga’ kukakomana ndi alendo ameneŵa amene anali patali ndi iye—kuchita zonsezi “pakutentha dzuŵa,” ndipo Abrahamu anali ndi zaka 99 zakubadwa! Kodi zimenezi sizikusonyeza chifukwa chake Paulo ananena za Abrahamu monga chitsanzo choti titsanzire? Ndicho chimene kuchereza alendo kumatanthauza, kukonda alendo, kudera nkhaŵa zofunika zawo. Ndi mkhalidwe wabwino.
13. Kodi nchifukwa ninji Abrahamu ‘anaŵerama pansi’ kwa alendo?
13 Nkhaniyo imatiuzanso kuti atakomana ndi alendowo, Abrahamu ‘anaŵerama pansi.’ Kuŵeramira alendo enieni? Eya, kuŵerama, monga kumene Abrahamu anachita, kunali njira yopatsira moni kwa mlendo wolemekezeka kapena winawake wapamwamba, kumene sikuyenera kuonedwa monga mchitidwe wa kulambira, woyenerera Mulungu yekha. (Yerekezerani ndi Machitidwe 10:25, 26; Chivumbulutso 19:10.) Mwa kuŵerama, osati kuzyolika koma kuŵerama “pansi,” Abrahamu anapatsa alendowa ulemu wa kukhala ofunika. Iye anali mutu wa banja lalikulu ndi lolemera, komabe anaona alendowa kukhala oyenera ulemu waukulu kuposa iye. Zimenezi nzosiyana chotani nanga ndi mkhalidwe wowopa alendo, malingaliro a kusadalira alendo! Abrahamu anasonyezadi tanthauzo la mawuwa akuti: “Mutsogolerane kuchitira wina mnzake ulemu.”—Aroma 12:10.
14. Kodi mkhalidwe wa kuchereza alendo umene Abrahamu anasonyeza alendowo unaloŵetsamo kuyesayesa ndi kudzipereka kotani?
14 Nkhani yonseyo imasonyeza kuti malingaliro a Abrahamu anali oona. Chakudya chenichenicho chinali chapadera. Ngakhale pabanja lalikulu lokhala ndi zoŵeta zambiri, “kamwana ka ng’ombe kofeŵa ndi kabwino” si chakudya cha nthaŵi zonse. Ponena za miyambo yofala ya ku deralo, Daily Bible Illustrations ya John Kitto ikuti: “Zosangulutsa sizimachitidwa kusiyapo pa mapwando ena, kapena pakabwera mlendo; ndipo ndi pa zochitika zimenezi zokha pamene amadya nyama, ngakhale ndi mwini ziŵeto zambiri zosiyanasiyana.” Mkhalidwe wotentha sunkalola kusunga chakudya chilichonse chokhoza kuwola, chotero kuti akonze chakudya chotero, anayenera kuchitiratu zonse panthaŵi imodzi. Nkosadabwitsa kuti m’nkhani yaifupi imeneyi liwu lakuti “msanga” kapena ‘kufulumira’ likupezeka katatu, ndipo Abrahamu ‘anafulumiradi’ kukonza chakudyacho!—Genesis 18:6-8.
15. Kodi ndi kaonedwe kati kabwino ka zinthu zakuthupi kofunika posonyeza mkhalidwe wa kuchereza alendo, malinga ndi chitsanzo cha Abrahamu?
15 Komabe, chifuno chake sindicho kungokonza phwando lalikulu kuti mukondweretse winawake. Ngakhale kuti Abrahamu ndi Sara anachita ntchito yonseyo kuti akonze ndi kupereka chakudyacho, taonani mmene Abrahamu ananenera za icho poyamba: “Nditengetu madzi pang’ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo; ndipo ndidzatenga chakudya pang’ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu.” (Genesis 18:4, 5) “Chakudya pang’ono” chimenecho chinakhala phwando la mwana wa ng’ombe wonenepa pamodzi ndi mikate ya ufa wosalala, mafuta a mkaka, ndi mkaka—phwando loyenerera mfumu. Kodi pali phunziro lanji? Pamene tichereza alendo, chinthu chofunika, kapena chachikulu koposa, sindicho zakudya ndi zakumwa zapamwamba, kapena zosangulutsa zambambande, ndi zina zotero. Kuchereza alendo sikumadalira pa mmene munthu angakwanitsire zinthu zapamwamba. M’malo mwake, kumazikidwa pa nkhaŵa yeniyeni ya ubwino wa ena ndi pa chikhumbo cha kuchitira ena zabwino zimene munthu angakwanitse. “Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng’ombe yonenepa pali udani,” umatero mwambi wa Baibulo, ndipo imeneyo ndiyo mfungulo ya kuchereza alendo kwenikweni.—Miyambo 15:17.
16. Kodi Abrahamu anasonyeza motani kuyamikira zinthu zauzimu mwa zimene anachitira alendowo?
16 Komabe, tiyenera kudziŵa kuti panalinso mkhalidwe wauzimu pachochitika chonsecho. M’njira ina yake Abrahamu anazindikira kuti alendowa anali amithenga ochokera kwa Yehova. Zimenezi zikusonyezedwa mwa mawu ake kwa iwo akuti: “[Yehova, NW] ngatitu ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu.”a (Genesis 18:3; yerekezerani ndi Eksodo 33:20.) Abrahamu sanadziŵe poyamba ngati kuti iwo anali ndi uthenga wake kapena ngati anali kungopyola kupita kwina. Mosasamala kanthu za zimenezo, anazindikira kuti chifuno cha Yehova chinali kuchitika. Anthu ameneŵa anali pantchito ina yake ya Yehova. Akanakonda kuchita chinachake kuthandizira ntchitoyo. Anazindikira kuti atumiki a Yehova afunikira zinthu zabwino koposa, ndi kuti adzapereka zabwino koposa malinga ndi mkhalidwe wawo. Mwakutero, padzakhala dalitso lauzimu, kaya kwa iyeyo kapena kwa winawake. Monga mmene zinakhalira, Abrahamu ndi Sara anadalitsidwa kwambiri chifukwa cha kuchereza alendo kwawo koona mtima.—Genesis 18:9-15; 21:1, 2.
Anthu Ochereza Alendo
17. Kodi Yehova anafunanji kwa Aisrayeli ponena za alendo ndi osoŵa omwe anali pakati pawo?
17 Mtundu umene unachokera kwa Abrahamu sunayenera kuiŵala chitsanzo chakecho chapadera. Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisrayeli chinaphatikizapo makonzedwe a kusonyeza mkhalidwe wa kuchereza alendo kwa alendo okhala pakati pawo. “Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto; ine ndine Yehova Mulungu wanu.” (Levitiko 19:34) Anthuwo anafunikira kupereka chisamaliro chapadera kwa aja ofuna chichirikizo chakuthupi ndi kusangowanyalanyaza. Pamene Yehova anawadalitsa ndi zotuta zochuluka, pamene anali kusangalala pa mapwando awo, pamene anali kupuma pa ntchito zawo m’zaka za Sabata, ndi pa nthaŵi zina, anthu anayenera kukumbukira aja osoŵa—akazi amasiye, ana amasiye, ndi alendo.—Deuteronomo 16:9-14; 24:19-21; 26:12, 13.
18. Ponena za kulandira chiyanjo cha Yehova ndi dalitso lake, kodi kuchereza alendo nkofunika motani?
18 Kufunika kwa kukoma mtima, kuoloŵa manja, ndi kuchereza alendo kulinga kwa ena, makamaka kwa aja osoŵa, kungaonedwe mwa njira imene Yehova anachitira ndi Aisrayeli pamene iwo ananyalanyaza kukhala ndi mikhalidwe imeneyi. Yehova ananena momveka kuti kukoma mtima ndi kuoloŵa manja kulinga kwa alendo ndi osoŵa kunali pakati pa zinthu zofunika kuti anthu ake apitirize kulandira madalitso ake. (Salmo 82:2, 3; Yesaya 1:17; Yeremiya 7:5-7; Ezekieli 22:7; Zekariya 7:9-11) Pamene mtunduwo unakangalika kuchita zinthu zofunika zimenezi ndi zina, iwo analemera nakhala ndi zinthu zochuluka zakuthupi ndi zauzimu. Pamene analoŵerera pa kulondola zinthu zawo zadyera ndi kunyalanyaza kusonyeza mikhalidwe yachifundo imeneyi kwa aja osoŵa, anatsutsidwa ndi Yehova, ndipo m’kupita kwa nthaŵi chiweruzo choŵaŵa chinaperekedwa pa iwo.—Deuteronomo 27:19; 28:15, 45.
19. Kodi tiyenera kukambitsirananso chiyani?
19 Chotero, nkofunika kwambiri chotani nanga kwa ife kudzisanthula ndi kuona ngati tikuchita mogwirizana ndi zimene Yehova amatiyembekezera kuchita pankhaniyi! Zimenezi zili choncho makamaka lerolino polingalira za mzimu wadyera ndi wa magaŵano umene uli m’dziko. Kodi tingasonyeze motani kuchereza alendo kwachikristu m’dziko logaŵanikana? Umenewo ndiwo mutu umene nkhani yotsatira ikufotokoza.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mukufuna kuŵerenga nkhani yonse ya mfundoyi, onani nkhani yakuti “Kodi Winawake Anawonapo Mulungu?” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1988, masamba 21-3.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi tanthauzo la liwu la m’Baibulo lotembenuzidwa kuti “kuchereza alendo” nchiyani?
◻ Kodi ndi m’njira zotani zimene Yehova alili chitsanzo changwiro pa kusonyeza mkhalidwe wa kuchereza alendo?
◻ Kodi Abrahamu anali wochereza alendo kufikira pa mlingo uti?
◻ Kodi nchifukwa ninji olambira oona onse ayenera ‘kuchereza alendo’?