Tizichitira Ena “Zabwino” Pokhala Ochereza (Mat. 12:35a)
N’zosakayikitsa kuti aliyense amafuna kuchitira ena “zabwino” ‘pokhala wochereza.’ (Aroma 12:13) Mwachitsanzo, akulu amalimbikitsidwa kuti azipereka chitsanzo chabwino pa nkhani yocherezayi. Angachite zimenezi poonetsetsa kuti omwe abwera kudzakamba nkhani ku mpingo kwawo akonzeredwa chakudya komanso ndalama zoyendera. Amawaitana kunyumba kwawo komanso kuwapatsa ndalama zoyendera. Komabe, nthawi zina tingaone ngati sitingakwanitse kuchereza poganiza kuti tilibe zowapatsa. Kapena tingamachite mantha kulandira alendo kunyumba kwathu. Koma mawu amene Yesu anauza Marita angatithandize kuti tisamaope kulandira alendo. (Luka 10:39-42) Yesu ananena kuti “chinthu chabwino kwambiri” munthu akalandira alendo ndi kucheza komanso kulimbikitsana nawo, osati kuwakonzera chakudya chapamwamba kapena kukhala ndi nyumba yokongoletsedwa bwino. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tizichitira abale ndi alongo athu zinthu “zabwino” mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena.—3 Yoh. 5-8.