Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 10/15 tsamba 8-9
  • Kodi Chuma cha Mfumu Solomo Nchokukumazidwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chuma cha Mfumu Solomo Nchokukumazidwa?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Muzifufuza Chuma Chamtengo Wapatali Kuposa Golide
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Mfumu Yachuma ndi Nzeru
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Nyumba ya Yehova
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 10/15 tsamba 8-9

Kodi Chuma cha Mfumu Solomo Nchokukumazidwa?

“Kulemera kwake kwa golidi anafika kwa Solomo chaka chimodzi kunali matalenti mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.”​—1 Mafumu 10:14.

MALINGA ndi kunena kwa vesi la Baibulo limenelo, Mfumu Solomo inapeza matani oposa 25 a golidi m’chaka chimodzi! Lerolino mtengo wake ungakhale $240,000,000. Golidi ameneyu ndi pafupifupi kuŵirikiza kaŵiri amene anakumbidwa mu 1800 padziko lonse. Kodi zimenezi nzotheka? Kodi umboni wa zofukula m’mabwinja umasonyezanji? Umasonyeza kuti mbiri ya Baibulo ya chuma cha Solomo ingakhaledi yoona. Biblical Archaeology Review imati:

◻ Mfumu Thutmose III wa Igupto (zaka za chikwi chachiŵiri B.C.E.) anapereka matani ngati 13.5 a zinthu zagolidi ku kachisi wa Amon-Ra ku Karnak​—ndipo zimenezi zinali chabe mbali ya mphatsoyo.

◻ Zolembedwa zachiaigupto zimafotokoza za mphatso zagolidi ndi zasiliva zonse pamodzi matani ngati 383 zoperekedwa ndi Mfumu Osorkon I (kuchiyambi kwa zaka za chikwi choyamba B.C.E.) kwa milungu.

Kuwonjezerapo, voliyumu yakuti Classical Greece ya mpambo wakuti Great Ages of Man imati:

◻ Migodi ya ku Pangaeum ku Thrace inatulutsa matani oposa 37 a golidi chaka chilichonse a Mfumu Philip II (359-336 B.C.E.).

◻ Pamene mwana wa Philip, Alexander Wamkulu (336-323 B.C.E.) analanda Susa, likulu la ufumu wa Perisiya, chuma chooposa matani 1,000 a golidi chinapezedwa.​—The New Encyclopædia Britannica.

Chotero mafotokozedwe a Baibulo a chuma cha Mfumu Solomo sali osakhulupirika. Kumbukiraninso kuti pa nthaŵiyo, Solomo “anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru.”​—1 Mafumu 10:23.

Kodi Solomo anagwiritsira ntchito motani chuma chake? Mpando wake wachifumu unali wokutidwa “golidi woyengetsa,” ndi zikho zake zomwera zinali “zagolidi,” ndipo anali ndi zikopa zazikulu 200 ndi malihawo 300 a “golidi wonsansantha.” (1 Mafumu 10:16-21) Koposa zonse, golidi wa Solomo anagwiritsiridwa ntchito pa kachisi wa Yehova mu Yerusalemu. Zoikapo nyali za m’kachisi ndi zipangizo zopatulika, monga zovuulira zangowe, mbale, ndi zikho, ndi mbiya zinali zopangidwa ndi golidi ndi siliva. Akerubi autali wa mamita 4.5 a m’Malo Opatulikitsa, guwa lansembe lofukizapo, ndipo ngakhale mkati mwa nyumba monsemo anakutamo ndi golidi.​—1 Mafumu 6:20-22; 7:48-50; 1 Mbiri 28:17.

Bwanji ponena za kachisi wokutidwa ndi golidi? Mokondweretsa, kugwiritsira ntchito golidi kotero sikunali kwachilendo konse m’nthaŵi yakale. Biblical Archaeology Review imanena kuti Amenophis III wa ku Igupto “analemekeza mulungu wamkulu Amun ndi kachisi ku Thebes amene anali ‘wokutidwa ndi golidi paliponse, pansi pake pokometseredwa ndi siliva, [ndi] poloŵera pake ponse pokometseredwa ndi msanganizo wa golidi ndi siliva.’” Ndiponso, Esar-haddon wa Asuri (zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E.) anakuta zitseko ndi golidi ndi kupaka golidi makoma a nyumba ya fano ya Ashuri. Ponena za kachisi wa Sin ku Harran, Nabonidus wa ku Babulo (zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E.) analemba kuti: “Ndinaveka makoma ake ndi golidi ndi siliva, ndi kuwang’animitsa ngati dzuŵa.”

Chotero, zolembedwa za m’mbiri zimasonyeza kuti nkhani ya m’Baibulo ya chuma cha Mfumu Solomo siili yokukumazidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena