Mfumu Yachuma ndi Nzeru
Kodi mumaganiza kuti chuma chingakupatseni chimwemwe? Kodi simungasangalale wina atakupatsani ndalama zambiri? Muyenera kuti mungasangalale. Mosakayika konse mungalingalire za mmene mungazigwiritsirire ntchito.
NDITHUDI, pali zinthu zambiri zimene mungagule pofuna kupangitsa moyo kukhala wokhutiritsa ndiponso wosangalatsa. Ndalama zingagwirenso ntchito monga ‘chochinjiriza’ ku mavuto adzidzidzi, monga matenda kapena ulova.—Mlaliki 7:12.
Koma kodi pali kugwirizana kotani pakati pa ndalama ndi chimwemwe? Kodi mumalingalira, monga momwe amalingalirira ambiri, kuti chimwemwe chimachokera pachuma? Kupeza mayankho a mafunso ameneŵa kungakhale kovuta chifukwa chakuti ndalama zingayesedwe mosavuta, kapena kuŵerengedwa, pamene chimwemwe sichingayesedwe kapena kuŵerengedwa. Simungaike chimwemwe pasikelo ndi kuchiyesa.
Ndiponso, anthu ena achuma amaoneka kuti ngachimwemwe, pamene ena ngopanda chimwemwe. Zilinso chimodzimodzi ndi anthu osauka. Komabe, anthu ambiri—ngakhale amene ali olemera kale—amakhulupirira kuti ndalama zochuluka zidzawapatsa chimwemwe chochuluka.
Munthu wina amene analemba za nkhani zimenezi anali Mfumu Solomo wa Israyeli wakale. Iye anali mmodzi wa anthu olemera kwambiri amene anakhalapo. Mungaŵerenge nkhani yonena za chuma chake chochuluka m’chaputala 10 cha Buku la m’Baibulo la Mafumu Woyamba. Mwachitsanzo, onani kuti vesi 14 limati: ‘Kulemera kwake kwa golidi anafika kwa Solomo chaka chimodzi kunali matalenti mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golidi.’ Chiŵerengero chimenechi nchofanana ndi matani 25 a golidi. Lerolino, mtengo wa golidi wochuluka motero ungapose $200,000,000, U.S.!
Komabe, Solomo sanali wolemera chabe; anapatsidwanso nzeru ndi Mulungu. Baibulo limati: “Mfumu Solomo anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru. Ndipo anthu onse a padziko anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m’mtima mwake.” (1 Mafumu 10:23, 24) Ifenso tingapindule ndi nzeru za Solomo, popeza kuti zolemba zake zili mbali ya zolemba za m’Baibulo. Tiyeni tione zimene iye ananena pankhani ya kugwirizana kwa chuma ndi chimwemwe.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Chotengedwa mu Die Heilige Schrift - Übersetzt von Dr. Joseph Franz von Allioli. Druck und Verlag von Eduard Hallberger, Stuttgart