Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 10/15 tsamba 30-31
  • “Nyumba ya Davide” Yeniyeni Kapena Yopeka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Nyumba ya Davide” Yeniyeni Kapena Yopeka?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Umboni Winanso Wofukulidwa m’Mabwinja
  • Zimene Asayansi Afukula Zikutsimikizira Kuti Mfumu Davide Analikodi
    Nkhani Zina
  • Kodi Buku Limeneli Tingalikhulupirire?
    Buku la Anthu Onse
  • Mwala Wachimoabu Wowonongedwa—Koma Wosataika
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Dalirani Mzimu wa Mulungu Zinthu Zikasintha pa Moyo Wanu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 10/15 tsamba 30-31

“Nyumba ya Davide” Yeniyeni Kapena Yopeka?

DAVIDE​—mbusa wachinyamatayo amene anakhala woimba, wandakatulo, msilikali, mneneri, ndiponso mfumu​—ngwodziŵika kwambiri m’Baibulo. Dzina lake limatchulidwa nthaŵi 1,138; mawuwo “Nyumba ya Davide”​—amene kaŵirikaŵiri amatanthauza banja la Davide​—agwiritsiridwa ntchito nthaŵi 25. (1 Samueli 20:16) Kodi Mfumu Davide ndi banja lake anali anthu ongopeka? Kodi kufukula za m’mabwinja kumavumbulanji? Zopezedwa zapadera za posachedwapa pa malo ofukulidwa ku Tel Dan kumpoto kwa Galileya zanenedwa kuti zikuchirikiza kukhalapo kwa Davide ndi banja lake.

M’chilimwe cha 1993, gulu lofukula za m’mabwinja, lotsogoleredwa ndi Profesa Avraham Biran, linayeretsa malo ena kunja kwa chipata chakunja cha Dan wakale. Iwo anapeza khoma lamwala. Mwala wakuda wa basalt umene unatulukira kuchokera pansi unachotsedwa mosavuta. Pamene anatembenuzira mwalawo ku dzuŵa lamasana, panaoneka zilembo. “O, Mulungu wanga, pali zilembo!” Anadzuma motero Profesa Biran.

Profesa Biran ndi mnzake, Profesa Joseph Naveh wa ku Yunivesite ya Hebrew ku Jerusalem, nthaŵi yomweyo analemba lipoti lasayansi lonena za zilembo. Nkhani ya m’magazini a Biblical Archaeology Review, March/​April 1994, yozikidwa pa lipoti limeneli ikuti: “Si kaŵirikaŵiri pamene zofukulidwa m’mabwinja zimakhala nkhani ya patsamba loyamba la New York Times (makamaka magazini a Time). Koma zimenezo nzimene zinachitika chilimwe chathachi pa zopezedwa ku Tel Dan, chiunda chokongola chakumpoto kwa Galileya, munsi mwa Phiri la Hermoni pafupi ndi amodzi a magwero a mtsinje wa Yordano.

“Pamenepo Avraham Biran ndi gulu lake la ofukula za m’mabwinja anapeza zilembo zapadera za m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E. zimene zikunena za ‘Nyumba ya Davide’ ndi ‘Mfumu ya Israyeli’ yomwe. Kumeneku nkuyamba kuti dzina la Davide lipezedwe m’zolembedwa zakale zilizonse kusiyapo Baibulo. Kunena kuti zolembedwazo sizingonena za ‘Davide’ winawake koma Nyumba ya Davide, banja la mfumu yotchuka yachiisrayeli, nkwapadera.

“‘Mfumu ya Israyeli’ ndi mawu amene amapezeka kaŵirikaŵiri m’Baibulo, makamaka m’Buku la Mafumu. Komabe, zimenezi zingakhale umboni wakale koposa wosakhala wa m’Baibulo wonena za Israyeli m’zilembo zachisemu. Koposa zonse, zolembedwazo zikusonyeza kuti Israyeli ndi Yuda yemwe, mosiyana ndi zonena za akatswiri ena otsutsa maumboni a Baibulo, anali maufumu odziŵika panthaŵiyi.”

Kudziŵa nthaŵi yake kwazikidwa pa mpangidwe wa zilembo zake, kupenda mbiya zopezedwa pafupi ndi chidutswa cha mwalacho, ndi pa nkhani ya zilembozo. Njira zonse zitatuzo zimasonya ku nthaŵi imodzimodzi, mwinamwake zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E., pafupifupi zaka zana limodzi pambuyo pa Mfumu Davide. Akatswiri amakhulupirira kuti zilembozo zinali mbali ya choumba cha chipambano chimene chinaikidwa m’Dani ndi mdani wachiaramiya wa “Mfumu ya Israeli” ndi “[Mfumu ya] Nyumba ya Davide” yomwe. Aaramiya, omwe ankalambira mulungu wotchuka wa mkuntho, Hadad, ankakhala kummaŵa kwawo.

M’chilimwe cha 1994, zidutswa zinanso ziŵiri za mwala wolembedwapowu zinapezedwa. Profesa Biran akusimba kuti: “Pa zidutswa ziŵirizi pali dzina la mulungu wachiaramiya Hadad, limodzinso ndi kutchula za nkhondo ya pakati pa Aisrayeli ndi Aaramiya.”

Chidutswa chachikulucho chopezedwa mu 1993 chinali ndi mizere 13 yoonekera pang’ono yolembedwa m’zilembo za Chihebri chakale. Panthaŵiyo, mawu a m’nkhani anali kuwasiyanitsa mwa kusindikiza dontho pakati. Komabe, mawuwo “Nyumba ya Davide” ngolembedwa monga liwu limodzi ndi zilembo “bytdwd” (zitatembenuzidwira m’zilembo zachiroma) m’malo mwa “byt” (nyumba), kusindikiza dontho pakati, ndiyeno “dwd” (Davide). Motero panabuka mafunso onena za tanthauzo la “bytdwd.”

Katswiri wa zinenero Profesa Anson Rainey akufotokoza kuti: “Joseph Naveh ndi Avraham Biran sanafotokoze zolembedwazo mwatsatanetsatane, mwina chifukwa chakuti anangoganiza kuti oŵerenga azadziŵa kuti kaŵirikaŵiri m’malembedwe otero, samaikapo chizindikiro chosiyanitsira mawu pakati pa mbali zogwirizana ziŵiri, makamaka ngati mawuwo ali dzina lodziŵika lenileni. ‘Nyumba ya Davide’ linalidi dzina lenileni lotero la ndale ndi la malo chapakati pa zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E.”

Umboni Winanso Wofukulidwa m’Mabwinja

Zimenezo zitapezedwa, katswiri wa mwala wa Mesa (wotchedwanso kuti Mwala wachimoabu), Profesa André Lemaire, ananena kuti nawonso umatchula “Nyumba ya Davide.”a Mwala wa Mesa, wopezedwa mu 1868, ngwofanana kwambiri ndi mwala wa ku Tel Dan. Yonse ndi ya m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E., njopangidwa ndi zinthu zofanana, njofanana ukulu wake, ndipo njolembedwa pafupifupi m’zilembo zofanana zachisemu.

Ponena za kukonzanso mzere wowonongeka pa mwala wa Mesa, Profesa Lemaire analemba kuti: “Pafupifupi zaka ziŵiri chidutswa cha ku Tel Dan chisanapezedwe, ndinagamula kuti mwala wa Mesa umatchula za ‘Nyumba ya Davide.’ . . . Chifukwa chimene mawu ameneŵa onena za ‘Nyumba ya Davide’ sanaonedwe konse poyamba chingakhale chenicheni chakuti mwala wa Mesa sunakhalepo ndi editio priceps yeniyeni [kusindikiza koyamba]. Zimenezo nzimene ndikulinganiza, zaka 125 mwala wa Mesa utapezedwa.”

Chidziŵitso chimenechi choperekedwa ndi zofukulidwa m’mabwinja nchokondweretsa kwa ife chifukwa chakuti mngelo, Yesu iye mwini, ophunzira ake, ndi anthu ambiri anachitira umboni za kukhalako kwa Davide. (Mateyu 1:1; 12:3; 21:9; Luka 1:32; Machitidwe 2:29) Zopezedwa m’mabwinja mwachionekere zimavomereza kuti iye ndi banja lake, “Nyumba ya Davide,” ali enieni, osati opeka.

[Mawu a M’munsi]

a Mwala wa Mesa ngwodziŵika kwa oŵerenga mabuku a Watch Tower Society. (Onani Nsanja ya Olonda, April 15, 1990, masamba 30-1.) Amausonyeza ku Louvre Museum, Paris.

[Chithunzi patsamba 31]

Chidutswa cha ku Tel Dan,b chopezedwa mu 1993 ku mzinda wa Dani, kumpoto kwa Galileya

[Mawu a M’munsi]

b Chithunzi cholembedwachi chazikidwa pa chithunzi chomwe chili mu Israel Exploration Journal.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena