Mwala Wachimoabu Wowonongedwa—Koma Wosataika
MWALA Wachimoabu, kapena Wamesa, unaswedwa mwadala mkati mwa chaka chimene unapezedwa mu 1868. Unali wazaka pafupifupi 3,000. Chidutswa cha mwala wakuda wa basalt wosalala wokhala ndi pamwamba poulungika bwino, unali wa msinkhu wa masentimita 112, mlifupi masentimita 71, ndipo muukulu masentimita 36. Nthaŵi ina pambuyo poswedwa, zidutswa zazikulu 2 ndi zazing’onozing’ono 18 zinapezedwanso, koma mbali imodzi mwa zitatu ya mwalawo inataika kotheratu.
Kodi ndimotani mmene chofukulidwa m’mainja chapadera choterocho chinataikira pafupifupi kwamuyaya? Ndipo kodi icho nchaphindu lanji kwa ophunzira a Baibulo?
Chinyengo ndi Kusakhulupirika
F. A. Klein anali Mzungu woyamba ndi wothera kuwona mwalawo m’mkhalidwe wake wosasweka. Unali wogona pakati pa mabwinja a Dibon kum’mawa cha kum’mpoto kwa Nyanja Yamchere. Iye anapanga zolemba zachidule zambali za mizera 34 ya mawu ozokotedwa m’malire mwake mokwezedwa ndipo, atabwerera ku Yerusalemu, anasimba chopezedwacho kwa mbuye wake wa ku Prussia. Sikiripitiyo mwamsanga inadziŵidwa kukhala Yachifoinike ndipo kufunika kwake kunazindikiridwa. Royal Museum ya ku Berlin inapereka ndalama kuti igule mwalawo, koma mwamsanga enanso anaulimbanira. Atadziŵa za mtengo wa malipiro awo, mafumu akumaloko anaubisa ndi kukweza mtengo wake modabwitsa.
Katswiri wa zofukulidwa pansi wa ku France anakhoza kusindikiza zilembozo pa pepala, koma chifukwa chakuti chosindikizidwapocho chinatsompholedwa chisanaume, zilembozo sizinakawoneka bwino. Panthaŵiyo, malamulo anabwera kuchokera ku Damasiko kuti Abedouin apereke mwala wawo kwa nduna zaboma. M’malo molabadira, Abedouin anagamulapo kuuwononga. Chotero anakoleza moto mozungulira mwala wam’mbiriwo wamtengo wapatali ndi kumauthira madzi mobwerezabwereza. Pamene mwalawo unasweka, zidutswazo zinagaŵiridwa mwamsanga pakati pa mabanja akumaloko kuti ziikidwe m’nkhokwe zawo, mowonetsera kuika dalitso pa mbewu zawo. Inalinso njira yabwino koposa kwa anthu kukambitsirana mwaumwini kaamba ka kugulitsa zidutswa zomwazikanazo.
Mbiri Yakale Yabaibulo Ikhala Yamoyo
Ndi thandizo la zomamatiza ndi zosindikiza pa pepala kukonza bwino zidutswa zogulidwazo, zilembo za pamwalawo pomalizira pake zinapezedwanso. Pamene zolembedwa zonse zinavumbulidwa, akatswiri ena anazizwa. Mwala wakalewo unalongosoledwa panthaŵiyo kukhala “mwala wosangalatsa koposa umene unapezedwapo chikhalire.”
Mfumu Mesa ya Moabu inaimika Mwala Wachimoabuwo kwa mulungu wake Kemosi kukumbukira kumasuka kwa Mesa ku ulamuliro wa Israyeli, umene, iye akuti, unakhala kwa zaka 40 ndipo unaloledwa ndi Kemosi chifukwa chakuti “anakwiya ndi dziko lake.” Chipanduko cha Moabu chimenechi kaŵirikaŵiri chimalingaliridwa kukhala chogwirizanitsidwa ndi zochitika zolembedwa m’mutu wachitatu wa 2 Mafumu. Pa choumba chachikumbukirocho, Mesa amadzitama za kukhala wachipembedzo kwambiri, za kumanga mizinda ndi msewu waukulu, ndi za chilakiko chake pa Israyeli. M’zonsezi, iye akupereka chitamando kwa mulungu wake Kemosi. Kugonjetsedwa kwa Mesa ndi nsembe ya mwana wake weniweni—zosimbidwa m’Baibulo—ziri, monga mmene wina angayembekezere, zosiidwa m’cholembedwa chodzilemekeza chimenechi.
Malo ambiri ondandalitsidwa ndi Mesa kukhala amene anawalanda akutchulidwa m’Baibulo, pakati pawo pali Medeba, Ataroti, Nebo, ndi Jahazi. Chotero, mwalawo umachirikiza kulongosoka kwa zolembedwa za Baibulo. Komabe, chapadera kwambiri ndicho kugwiritsira ntchito kwa Mesa Tetragrammaton, YHWH, dzina la Mulungu wa Israyeli, m’mzera wa 18 wa cholemberacho. Panopa Mesa akunyada nati: “Ndinatenga kumeneko [Nebo zotengera] za Yahweh, kudzikokera kwa Kemosi.” Kunja kwa Baibulo, mwinamwake chimenechi ndicho cholembera chakale koposa chogwiritsira ntchito dzina la Mulungu.
Mu 1873 Mwala Wachimoabu unabwezeretsedwanso, wokhala ndi zomatidwa za malemba osoŵawo atawonjezedwako, ndi kuikidwa monga chowonetsedwa m’malo osungiramo zakale a Louvre, Paris, kumene ukukhala. Kope lake lingawonedwe mu British Museum, London.
[Zithunzi patsamba 31]
(Pamwamba) Dziko la Moabu
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
(Kumanzere) Mwala Wachimoabu wopangidwanso
[Mawu a Chithunzi]
Musée du Louvre, Paris
(Kulamanja) Tetragrammaton monga mmene ikuwonekera pa chofukulidwacho
[Mawu a Chithunzi]
Baibulo mu British Museum