Mavuto Ochuluka Kwambiri
“NCHIFUKWA ninji pali mavuto ambiri aakulu chonchi okhudza anthu mmodzi ndi mmodzi ndi okhudza anthu ambiri . . . ? Mulungu ayenera kukhala ndi chifuno komabe pali zochuluka m’dzikoli zimene zili zopanda pake, mavuto ochuluka opanda tanthauzo ndi uchimo wachabechabe. Kodi Mulungu ameneyu angakhale zimene Nietzsche anamneneza nazo: wopondereza, wonyenga, waukathyali, wakupha?”—On Being a Christian, lolembedwa ndi Hans Küng.
Mutha kuona kuti Mkatolika ameneyu Hans Küng, katswiri wa zaumulungu, akungotchula nkhani imene yavutitsa maganizo ambiri—nchifukwa ninji Mulungu wamphamvuyonse ndi wachikondi amalola mavuto ochuluka chonchi? Kodi simunawamvepo anthu akufunsa zimenezo? Munthu aliyense wachifundo amachita chisoni ndi zimene Küng akutcha “mtsinje wosatha wa mwazi, thukuta ndi misozi, zopweteka, chisoni ndi mantha, kusungulumwa ndi imfa.” Kunena zoona, zili ngati mtsinje wothamanga, chigumula cha mantha ndi nsautso, chimene chawononga anthu miyandamiyanda m’mbiri yonse.—Yobu 14:1.
Zodzala ndi “Chivuto ndi Chopanda Pake”
Talingalirani za mavuto amene amatsatira nkhondo, kupweteka kumene amamva osati omafawo okha komanso otsala akulira, monga makolo ndi achibale a ana ophedwa ndi ena ochitidwa nkhanzawo. Posachedwapa bungwe la Red Cross linatero kuti “pazaka 10 zapitazo, ana 1.5 miliyoni anaphedwa m’nkhondo.” Ku Rwanda mu 1994, bungwe la Red Cross likutero kuti, “amuna, akazi ndi ana zikwi mazana ambiri anaphedwa mwachiŵembu ndiponso mwankhanza.”
Tisaiŵalenso kupweteka mtima kumene anthu opotoka maganizo ogona ana amadzetsa. Mayi wina wolira, yemwe anati mwana wake wamwamuna anadzipha atamuipsa wantchito yosamalira ana, anati: “Mwamuna yemwe anaipsa mwana wanga . . . anamuwononga iye ndi anyamata ena ambiri mwanjira yachiŵembu ndi yonyansitsa imene simungaiyembekezere.” Ndipo bwanji nanga za kupweteka mtima kosautsa kumene amamva aja ovutika chifukwa cha ambanda ouma mtima kapena chifukwa cha aja ongokhalira kupha anzawo, onga aja ogwidwa ku Britain amene “anaba anthu, kuwagona, kuwazunza ndi kuwapha popanda kulangidwa kwazaka 25”? Zikuoneka kuti m’mbiri yonse zopweteka ndi zosautsa zimene amuna ndi akazi achitirana zakhala zopanda malire.—Mlaliki 4:1-3.
Onjezaniponi mavuto amene kupsinjika ndi matenda zimadzetsa ndiponso kupweteka koŵaŵa kwa chisoni chimene chimasautsa mabanja wokondedwa wawo atafa mosayembekezera. Palinso nsautso imene amavutika nayo anjala kapena aja amene amawagwera masoka ena otchedwa achilengedwe. Ndi oŵerengeka chabe omwe angatsutse mawu a Mose akuti zaka zathu 70 kapena 80 nzodzala ndi “chivuto ndi chopanda pake.”—Salmo 90:10.
Kodi Ndi Cholinga cha Mulungu?
Kodi zingakhale kuti mavuto osatha ameneŵa ali cholinga cha Mulungu chimene sitingathe kuchimvetsa, malinga ndi zimene ena anena? Kodi tiyenera kuvutika tsopano kuti tizindikire ubwino wa moyo ‘m’dziko lotsatiralo’? Malinga ndi zimene Mfalansa wafilosofi Teilhard de Chardin anakhulupirira, kodi nzoona kuti “mavuto omwe amapha ndi kuvunditsa, ngofunika kwa munthu kuti apitirize kukhalako nakhale mzimu”? (The Religion of Teilhard de Chardin; kanyenye ngwathu.) Ayi!
Kodi katswiri wopanga zinthu wachifundo angalengere dala malo angozi ndiyeno nanena kuti ali wachifundo atapulumutsa anthu ku zotsatirapo zake? Kutalitali! Kodi Mulungu wachikondi angachitirenji chinthu choipa chotero? Nanga nchifukwa ninji Mulungu amalola mavuto? Kodi mavuto adzathadi? Nkhani yotsatira idzayankha mafunsowa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Chithunzithunzi cha WHO chojambulidwa ndi P. Almasy