“Malaya Opatulika a ku Trier”
TRIER, wokhala ndi mbiri yoyambira zaka 2,000 kumbuyoku, ndiwo mzinda wakale koposa ku Germany.a Pazaka mazana ambiri Trier wakhala wogwirizana kwambiri ndi Tchalitchi cha Katolika. Mu 1996 tchalitchi chachikulu ku Trier chinasonyeza chovala cha masiye chopembedzedwa chimene amati nchakale ngati mzindawo. Chikutchedwa Malaya Opatulika a ku Trier.
Malayawo ali ndi utali wa mamita 1.57 ndi mamita 1.09 m’bwambi ndipo manja ake utali wake ndi theka la utali wa malayawo. Ndi opangidwa ndi nsalu yathonje ndipo ayenera kuti ankavalidwa monga malaya akunja, malinga ndi kunena kwa Hans-Joachim Kann m’buku lake lakuti Wallfahrtsführer Trier und Umgebung (Zitsogozo za Paulendo Wachipembedzo ku Trier ndi Malo Ozungulira). Ena poyerekezera amati malayawo enieni—mbali yake yaikulu imene aikonzanso ndi kuilimbitsa ndi nsalu zina pazaka mazana ambiriwa—ndi a m’zaka za zana lachiŵiri kapena ngakhale zaka za zana loyamba C.E. Ngati zimenezo nzolondola, zingatanthauze kuti malayawo ndi akale ndithu, kanthu kabwino ka m’myuziyamu.
Komabe, ena akulimbikira kunena kuti malayawo si akale chabe komanso ngopatulika—nchifukwa chake amatchedwa Malaya Opatulika. Zimenezi zakhala chonchi chifukwa chakuti alibe msoko, monga momwe malaya amkati a Yesu Kristu analili. (Yohane 19:23, 24) Ena amatinso kwenikweni “Malaya Opatulika” amenewo anali a Mesiya.
Sitikudziŵa bwino mmene malayawo anabwerera ku Trier. Buku lina la maumboni limanena kuti “anaperekedwa ku mzindawo ndi mfumukazi Helena, amayi wa Constantine Wamkulu.” Kann akunena kuti mbiri yodalirika ya kukhalapo kwa malayawo ku Trier ikuyambira mu 1196.
Malayawo, amene amasungidwa m’tchalitchi chachikulu, asonyezedwa nthaŵi zosiyanasiyana chiyambire zaka za zana la 16. Mwachitsanzo, anachita zimenezi mu 1655, mwamsanga pambuyo pa Nkhondo Yazaka Makumi Atatu, imene inaonongetsa chuma chambiri cha Trier. Kugulitsa zokumbutsa ulendo wachipembedzo nthaŵi ndi nthaŵi kwabweretsa ndalama zambiri.
Pakhala maulendo achipembedzo atatu okaona “Malaya Opatulika” m’zaka za zana lino—mu 1933, 1959, ndi 1996. Mu 1933 ulendowo anaulengeza tsiku limodzi ndi limene Hitler anaikidwa kukhala nduna yaikulu ya Ulamuliro wa German. Kann akunena kuti kuchitika kwa zinthu ziŵirizi padeti limodzi kukusonyeza mikhalidwe yochititsa ulendowo. Asilikali a Nazi ovala mayunifomu analandira odzachezawo kunja kwa tchalitchi chachikulu. Anthu mamiliyoni aŵiri ndi theka anaona mkanjowo chakacho.
Herbert, amene wakhala mu Trier zaka zambiri, anayerekeza kucheza kwa mu 1959 ndi mu 1996. “Mu 1959 makwalala anali tho ndi anthu, ndipo pagulaye lililonse la khwalala panali ogulitsa zikumbutso. Chaka chino kwangoti zii.” Eetu, 700,000 okha ndiwo anaona mkanjowo mu 1996, kupereŵera pachiŵerengero cha mu 1959 ndi miliyoni imodzi.
Kodi Nchifukwa Ninji Amapita Kukaona Mkanjowo?
Tchalitchi chimanena mogogomezera kuti mkanjowo suyenera kuonedwa monga chinthu chochipembedza. Mkanjo wopanda msokowo umaonedwa monga chizindikiro cha umodzi wa tchalitchi. Frankfurter Allgemeine Zeitung ikunena kuti polengeza kuchezako, Bishopu Spital anati: “Mkhalidwe wachilendo m’dziko lathu ukufuna kuti ife Akristu tikhale ndi mayankho achilendo. Tiyenera kutsutsa udani, nkhanza, ndi chiwawa chomawonjezekacho.” Bishopuyo anafotokoza kuti kuona mkanjowo kumakumbutsa munthu za umodzi.
Koma kodi nchifukwa ninji wina aliyense amafunikira “Malaya Opatulika” kuti akumbukire za umodzi wa tchalitchi? Bwanji nanga ngati mkanjowo wawonongeka kapena kumotsoka kapena kuvumbulidwa kuti si weniweni? Kodi pamenepo umodzi wa tchalitchi ungakhale pangozi? Bwanji ponena za anthu amene satha kupanga ulendo wachipembedzo umenewo wa ku Trier? Kodi iwo samaganizira kwambiri za umodzi uliwonse wa m’tchalitchi?
Malemba Oyera samatchula zilizonse zakuti Akristu oyambirira ankafunikira zinthu zowakumbutsa kufunikira kwa umodzi wachikristu. Ndithudi, mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu ndi mawu akuti: “Tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.” (2 Akorinto 5:7) Choncho umodzi umene Akristu oona akusangalala nawo ukufotokozedwa kuti ndi “umodzi wa chikhulupiriro.”—Aefeso 4:11-13.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Galamukani! yachingelezi ya April 22, 1980, masamba 21-3.