Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/15 tsamba 29
  • ‘Amamvera Zomwe Amaphunzira Kuchipembedzo Kwawo’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Amamvera Zomwe Amaphunzira Kuchipembedzo Kwawo’
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Timafuna Anthu Oona Mtima’
    Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/15 tsamba 29

‘Amamvera Zomwe Amaphunzira Kuchipembedzo Kwawo’

MKAZI wina wa ku Miami, Florida, U.S.A., analembera kalata nyuzipepala ina ya kwawo komweko kuti: “Pa Dec. 10, wakuba anasolola chikwama m’thumba la mwana wanga pamsika wa kaunjika. Munali laisensi yake ya galimoto, khadi la Social Security, ndi zina zambiri kuphatikizapo $260.

“Atamuuza manijala kuti andibera, anabwerera kunyumba. Madzulo analandira foni kuchokera kwa mkazi wina wolankhula Chispanya, amene mothandizidwa ndi [telefoni] opaleta yemwe amatanthauzira, anamuuza kuti anapeza chikwamacho.

“Mkaziyo anamuuza adresi yake. . . . ndipo anampatsa chikwama, chomwe munali zonse monga momwe zinalili, kuphatikizapo $260.

“Mkaziyo anaiona mbalayo pamene imaba chikwamacho ndipo anakuwa. Mbalayo inataya chikwamacho ndi kuthaŵa. Panthaŵiyi nkuti mwana wanga atapita, ndiye anatenga chikwamacho nkupita nacho kunyumba ndi kuimba telefoni.

Iye pamodzi ndi banja lake ndi Mboni za Yehova. Nzachionekere kuti amamvera zomwe amaphunzira kuchipembedzo kwawo.”

Mboni za Yehova sizikhala zoona mtima ncholinga choti anthu azizitamanda. (Aefeso 6:7) M’malo mwake, zimafunitsitsa kutamanda Atate wawo wakumwamba, Yehova. (1 Akorinto 10:31) Kukonda kwawo Mulungu ndiponso anthu ena onse kumawapangitsa kulalikira “uthenga . . . wabwino” wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Mwa Ufumuwo, Mulungu walonjeza kupanga dzikoli kukhala paradaiso wokongola. Zikadzatero dzikoli lidzakhala osati lokongola chabe, komanso la makhalidwe abwino, ndipo kuona mtima kudzakhalapo kwamuyaya.​—Ahebri 13:18; 2 Petro 3:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena