Chinsinsi m’Dzina la Ambuye
KUTSEGULIRA utsi wakupha m’njira ya pansi panthaka ku Tokyo, Japan m’March 1995 kunapha anthu 12, kudwalitsa ena zikwi zambiri, ndipo kunathandiza kuvumbula chinsinsi china. Gulu lachipembedzo la dzina lakuti Aum Shinrikyo (Choonadi Chachikulu) linali litasunga utsi wa sarin wogwiritsira ntchito pofuna kukwaniritsa zolinga zachinsinsi.
Patapita mwezi umodzi bomba linaphulika ndi kugwetsa nyumba ya boma ku Oklahoma City, U.S.A., ndi kupha anthu 167. Umboni unasonyeza kuti mwinamwake kuukirako kunali chifukwa cha kusagwirizana kumene kunalipo zaka zokwanira ziŵiri zapitazo pakati pa boma ndi gulu lachipembedzo la Branch Davidian la ku Waco, Texas. Panthaŵiyo mamembala a gululo ngati 80 anafa. Kuphulika kwa bombalo kunavumbulanso chimene chinali chinsinsi kwa anthu ambiri: Mu United States muli magulu ankhondo apadera ambirimbiri, mwa amene ena akuwaganizira kuti akufuna kuukira boma.
Pambuyo pake, chakumapeto kwa 1995, mitembo yotenthedwa ya anthu 16 inapezeka m’nkhalango ina pafupi ndi Grenoble, France. Iwo anali mamembala a Order of the Solar Temple, gulu lina laling’ono lachipembedzo limene mu October 1994 linali litamvekera kwambiri ku Switzerland ndi Canada pamene mamembala ake ena 53 anadzipha kapena kuphedwa. Koma ngakhale pambuyo pa tsokali, gululo linapitirizabe kukhalapo. Mpaka lero zimene zikulisonkhezera ndi zolinga zake sizikudziŵikabe.
Ngozi za Chinsinsi Chachipembedzo
Titalingalira zochitikazi, kodi tingadabwe kuti anthu ambiri amakayikira zolinga za magulu achipembedzo? Ndithudi palibe amene angafune kuchirikiza gulu lachinsinsi—lachipembedzo kapena losakhala lachipembedzo—limene limamdyerera pa kukhulupirika kwake ndi kumchititsa kulondola zolinga zimene sakuvomerezana nazo. Komano, kodi anthu angachitenji kuti apeŵe kugwidwa mumsampha woloŵa m’magulu achinsinsi okayikitsa?
Mosakayikira, aliyense wofuna kukhala membala wa gulu lachinsinsi angachite bwino kutsimikiza kuti zolinga zake zenizeni nzotani. Ayenera kupeŵa kukakamizidwa ndi mabwenzi kapena odziŵana nawo, ndipo ayenera kusankha malinga ndi mmene zinthu zililidi osati chifukwa chosonkhezereka mtima. Kumbukirani kuti ndi munthu iye mwini—osati ena—amene adzavutika ndi zilizonse zimene zingatsatirepo.
Kutsatira mapulinsipulo a Baibulo ndiko njira yotsimikizirika koposa yopeŵera magulu oipa okhala ndi zolinga zoipa. (Yesaya 30:21) Zimenezi zimaphatikizapo kusaloŵa m’ndale, kusonyeza chikondi kwa ena, ngakhale kwa adani, kupeŵa “ntchito za thupi,” ndi kukulitsa chipatso cha mzimu wa Mulungu. Chachikulu kwambiri nchakuti Akristu oona sayenera kukhala mbali ya dziko, monga momwe Yesu sanali mbali yake, ndipo zimenezi sizimatilola kugwirizana ndi magulu achinsinsi akudziko.—Agalatiya 5:19-23; Yohane 17:14, 16; 18:36; Aroma 12:17-21; Yakobo 4:4.
Mboni za Yehova ndi ophunzira Baibulo oona mtima amene amaona chikhulupiriro chawo kukhala chofunika kwambiri ndipo amayesa kuchitsatira poyera m’moyo wawo. Padziko lonse, iwo amadziŵika kuti ndi gulu lachipembedzo limene ‘likufunafuna mtendere ndi kuulondola.’ (1 Petro 3:11) Buku lawo lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom limanena molondola kuti: “Mboni za Yehova sizili gulu lachinsinsi ayi. Zikhulupiriro zawo zochokera m’Baibulo zafotokozedwa zonse m’zofalitsa zimene aliyense angapeze. Ndiponso, zimayesayesa kwambiri kuitanira aliyense kumisonkhano kuti adzadzionere ndi kudzimverera yekha zimene zimachitika.”
Chipembedzo choona sichimachita zinthu mwachinsinsi m’njira iliyonse. Olambira Mulungu woona alangizidwa kuti asadzibise kapena kubisa cholinga chawo monga Mboni za Yehova. Ophunzira a Yesu oyambirira anadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chawo. Zikhulupiriro zawo ndi zochita zawo zinali zodziŵika kwa aliyense. Ndi mmenenso zilili ndi Mboni za Yehova lerolino. Ee, ngati maboma opondereza alanda mosayenera ufulu wakulambira, Akristu mochenjera ndi molimba mtima ayenera kupitirizabe ndi ntchito yawo, kumvera “Mulungu koposa anthu,” mkhalidwe umene amawakakamiza kuloŵamo chifukwa cha kuchitira kwawo umboni poyera molimba mtima.—Machitidwe 5:27-29; 8:1; 12:1-14; Mateyu 10:16, 26, 27.
Ngati munayamba mwaganizapo kuti mwina Mboni za Yehova ndi gulu lachinsinsi lotsata munthu kapena lampatuko, zinali choncho mwina chifukwa chakuti inuyo simunawadziŵe bwino. Ziyenera kuti zinali choncho kwa ambiri m’zaka za zana loyamba.
Machitidwe chaputala 28 imatisimbira za msonkhano umene mtumwi Paulo anali nawo ku Roma ndi “akulu a Ayuda.” Iwo anamuuza kuti: “Tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.” (Machitidwe 28:16-22) Powayankha, Paulo “anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu,” ndipo “ena anamvera.” (Machitidwe 28:23, 24) Kumva choonadi chenicheni ponena za Chikristu choona kunawapindulitsadi kosatha.
Popeza Mboni za Yehova nzodzipereka chonchi pantchito yosabisa ndipo yapoyera ya Mulungu, izo zimafuna kwambiri kuvumbula zenizenidi za ntchito yawo ndi zikhulupiriro zawo kwa aliyense amene angafune kudziŵa zenizeni. Bwanji osadzifufuzira nokha, kuti muchidziŵe bwino chikhulupiriro chawo?
[Zithunzi patsamba 6]
Mboni za Yehova nzofunitsitsa kudzivumbula ndi kuvumbula zimene zikuchita