Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/1 tsamba 3-4
  • Nchifukwa Ninji Pali Zachinsinsi Chonchi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Ninji Pali Zachinsinsi Chonchi?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Zachinsinsi Zikhala Zangozi
  • Kodi Akuchitanji Tsopano?
  • Chinsinsi Chimene Ufunika Kuuzako Ena
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Chinsinsi Chimene Tonsefe Timafuna Titachidziwa
    Phunzitsani Ana Anu
  • Chinsinsi Chimene Akristu Sayenera Kusunga!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Chinsinsi m’Dzina la Ambuye
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/1 tsamba 3-4

Nchifukwa Ninji Pali Zachinsinsi Chonchi?

“PALIBE chinthu chothodwetsa kwambiri monga chinsinsi.” Mulimonse mmene zingakhalire, mwambi wina wachifalansa umatero. Kodi ndiye chifukwa chake timamva bwino tikadziŵa chinsinsi chinachake koma nthaŵi zina nkumva womangika ngati sitingalankhule za icho? Ngakhale zili choncho, pazaka mazana ambiriwa anthu ambiri akonda kuchita zinthu mwachinsinsi, ndipo agwirizana m’magulu achinsinsi pofuna kukwaniritsa cholinga chimodzi.

Zipembedzo zachinsinsi zopezeka ku Egypt, Greece, ndi Rome ndizo zina mwa magulu akale kwambiri achinsinsi ameneŵa. Kenako ena mwa magulu ameneŵa anapatuka pazochita zawo zachipembedzo nayamba kuloŵanso m’ndale, m’zachuma, kapena m’zakakhalidwe ka anthu. Mwachitsanzo, amalonda atagwirizana kupanga timagulu ku Ulaya m’nyengo zapakati, mamembala ake anayamba kuchita zinthu mwachinsinsi makamaka kuti atetezere chuma chawo.

Makono, magulu achinsinsi ambiri apangidwa pazifukwa zabwino ndithu, mwinamwake “pazifuno za kakhalidwe ndi kuchitira ena zabwino,” malinga ndi kunena kwa Encyclopædia Britannica, ndi “kuchita maprogramu othandiza ena ndi kuwaphunzitsa.” Magulu ena aubwenzi, makalabu a achinyamata, makalabu a anthu onse, ndi magulu ena nawonso ngachinsinsi, kapena ngachinsinsi pazinthu zina. Nthaŵi zambiri, magulu ameneŵa amangokhala magulu wamba, mamembala ake amangosangalala ndi kusunga zinsinsi. Miyambo yachinsinsi yoloŵera maguluwo imasangalatsa kwambiri mtima ndi kulimbitsa mayanjano aubwenzi ndi umodzi. Mamembala ake amamva kuti ali oyandikana kwambiri ndi kuti ali ndi chifuno. Magulu achinsinsi a mtundu umenewu nthaŵi zambiri alibe ngozi iliyonse kwa anthu ena. Kusadziŵa zinsinsi za gululo sikumaika ena pangozi iliyonse.

Pamene Zachinsinsi Zikhala Zangozi

Si magulu onse achinsinsi amene amafanana. Koma aja amene ali ndi “zinsinsi pakati pa zinsinsi,” monga momwe Encyclopædia Britannica imazinenera, ali ndi ngozi ina. Bukuli limafotokoza kuti “mwa kugwiritsira ntchito maina ena, malumbiro kapena mavumbulutso,” akuluakulu ake amatha “kudzipatula,” choncho kusonkhezera “apansi pawo kuti aziyesayesa kufika pamalo apamwambawo.” Ngozi yaikulu ya magulu ameneŵa njodziŵikiratu. Aja a maudindo aang’ono sangadziŵe kalikonse ponena za zolinga zenizeni za gululo, nanga sikuti sanafikebe paudindo woti adziŵe zimenezo. Utha kungoloŵa m’gulu limene sukulidziŵa bwino zolinga zake ndi njira zake zozichitira ndipo, mwinanso sanakufotokozereni bwino nkomwe. Koma munthu amene waloŵa gulu limeneli pambuyo pake angavutike kutulukamo; amakhala atamangidwa m’maunyolo a chinsinsi.

Komabe, kuchita zachinsinsi kulinso ndi ngozi ina yaikulu pamene gululo zolinga zake nzaukatangale kapena zaupandu ndiyeno nkumayesa kubisa kukhalapo kwake. Kapena ngati kukhalapo kwake kapena zolinga zake zazikulu nzodziŵika, mamembala ake angamayese kudzibisa ndi kubisa zimene akufuna kuchita nthaŵi yomweyo. Ndi mmene zakhalira ndi magulu auchigaŵenga otengeka maganizo amene nthaŵi ndi nthaŵi amaopsa dziko ndi zochita zawo zauchigaŵenga.

Inde, kuchita zinthu zachinsinsi kungakhale kwangozi, kwa munthu aliyense payekha ndi kwa anthu onse. Lingalirani za magulu achiwawa achinsinsi a achinyamata amene amaukira anthu osadziŵa kalikonse, magulu aupandu monga Mafia yachinsinsiyo, magulu monga Ku Klux Klan omwe amati azungu ndiwo apamwamba,a ndi magulu ena ambirimbiri auchigaŵenga a padziko lonse amene akupitirizabe kulepheretsa zoyesayesa zodzetsa mtendere wapadziko lonse ndi chisungiko.

Kodi Akuchitanji Tsopano?

M’ma 1950, monga zotsatirapo za Nkhondo ya Mawu, magulu achinsinsi anabadwa m’maiko angapo a ku Western Europe kuti akhale maziko a zochita zolimbana ndi Asovieti atayesa kulanda Western Europe. Mwachitsanzo, malinga ndi magazini yachijeremani ya Focus, “malo 79 achinsinsi osungirapo zida” anakhazikitsidwa ku Austria panthaŵi imeneyo. Maiko ena a ku Ulaya sanawadziŵe nkomwe maguluwa. Magazini ina inanena mosabisa kuchiyambi kwa ma 1990 kuti: “Sitikudziŵabe kuti lero magulu ameneŵa alipo angati ndi kuti akhala akuchitanji posachedwapa.”

Ntheradi. Ndani angadziŵedi kuti ndi magulu angati achinsinsi amene panopo chonchi ali chiopsezo chachikulu kwambiri kuposa chimene aliyense wa ife angaganizire?

[Mawu a M’munsi]

a Gulu la ku United States limeneli linasungabe miyambo ina yachipembedzo ya magulu ena akale achinsinsi mwa kugwiritsira ntchito mtanda umene ukupsa moto monga chizindikiro chake. Kalelo, gululi linali kuukira adani awo usiku, mamembala ake atavala mikanjo ndi nsalu zoyera ndi kufuzira mkwiyo wawo pa anthu akuda, Akatolika, Ayuda, anthu osakhala Aamereka, ndi mabungwe a antchito.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena