Msonkhano wa Pachaka
October 4, 1997
MSONKHANO WA PACHAKA wa mamembala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennslyvania udzachitika pa October 4, 1997, pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, pa 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, ku New Jersey. Kukumana koyambirira kwa mamembala okhaokha kudzakhalako pa 9:15 a.m., ndiyeno msonkhano wa onse wa pachaka udzatsatira pa 10.00 a.m.
Mamembala a Bungweli ayenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano lino za kusintha kulikonse kwa makeyala awo a makalata mkati mwa chaka chapita kotero kuti makalata odziŵitsa anthaŵi zonse ndi mapepala a voti awapeze mkati mwa July.
Mapepala a voti, amene adzatumizidwa kwa mamembalawo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pachaka, ayenera kubwezeredwa kotero kuti afike ku Ofesi ya Mlembi wa Sosaite August 1 isanakwane. Membala aliyense ayenera kudzaza ndi kutumiza pepala lake la voti nthaŵi yomweyo, akufotokoza kaya ngati adzapezeka pamsonkhanowo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa pepala la voti lililonse chiyenera kukhala chotsimikizirika panthaŵiyi, popeza kuti chidzakhala chodziŵira amene adzapezekapo.
Tikuyembekezera kuti programu yonse, kuphatikizapo msonkhano wa kayendetsedwe ka zinthu ndi malipoti, zidzamalizidwa pa 1.00 p.m. kapena kupitirira pang’ono pamenepo. Sipadzakhala programu yamasana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, okhala ndi matikiti okha ndiwo amene adzaloledwa kuloŵa. Sipadzakhala makonzedwe alionse a akugwirizanitsa matelefoni ndi nyumba zina zosonkhanira pamsonkhano wa pachaka.