Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 9/15 tsamba 21-24
  • Mmene Mungasungire Chimwemwe mu Utumiki wa Nthaŵi Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungasungire Chimwemwe mu Utumiki wa Nthaŵi Zonse
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupirira Kukhumudwa
  • Kugwirizana ndi Ena
  • Ngati Mumadwaladwala
  • Kukhalabe Achimwemwe Ngakhale Dziko Nlamphwayi
  • Kulimbikitsidwa ndi Ena
  • Chimwemwe cha Yehova​—Mphamvu Yathu
  • Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kuyamikira Mwayi wa Utumiki Wopatulika
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Utumiki Wathu Ukasintha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 9/15 tsamba 21-24

Mmene Mungasungire Chimwemwe mu Utumiki wa Nthaŵi Zonse

KUKWANIRITSIDWA kwa ulosi wa m’Baibulo kumasonyeza bwino kuti tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo lino losaopa Mulungu. Pozindikira izi, atumiki a Yehova Mulungu amathera nthaŵi yochuluka yomwe ali nayo kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wake. Mboni za Yehova zoposa 600,000 zalinganiza moyo wawo kuti zizichita nawo utumiki wa nthaŵi zonse. Ena a iwo ndi alaliki a Ufumu a nthaŵi zonse otchedwa apainiya. Ena ndi atumiki odzifunira pa Beteli ku malikulu a dziko lonse a Watch Tower Society kapena pamaofesi ake a nthambi. Komanso, ena ndi amishonale ndi oyang’anira oyendayenda.

Baibulo limasonya kuti m’masiku otsiriza, kudzakhala “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Lemba la m’Baibulo lachigiriki limagwiritsira ntchito mawu amene angatanthauziridwe kuti “nthaŵi zoikidwiratu zoopsa.” Motero, palibe amene ayenera kuyembekeza kukhala ndi moyo wopanda mavuto m’tsiku lathu. Kwa atumiki ena achikristu, mavuto amaoneka kukhala aakulu kwambiri kwakuti angadzifunse kuti, ‘Kodi ndipitirize utumiki wa nthaŵi zonse, kapena ndisiye?’

Kodi ndi mikhalidwe yotani imene ingapangitse munthu kulingaliranso kachiŵiri za utumiki wake monga mpainiya, mtumiki wodzifunira wa pa Beteli, woyang’anira woyendayenda kapena mmishonale? Mwinamwake amadwaladwala kwambiri. Mwina wachibale wake wokalamba kapena wofooka akufunikira kusamaliridwa nthaŵi zonse. Mwina nkukhala kuti okwatirana akuyamba kukhala ndi ana. Aliyense amene amaleka utumiki wa nthaŵi zonse pa zifukwa zimenezi ndipo pa zifukwa za Malemba sayenera kuchita manyazi chifukwa cha kusinthako.

Komabe, bwanji ngati wina akuganiza zosiya utumiki wa nthaŵi zonse chifukwa chakuti sakukondwa? Mwina mpainiya akupeza okondwerera ochepa mu utumiki wake ndiye akufunsa kuti, ‘Nkwanji kupitiriza ndi moyo wanga wodzimana pamene ndi ochepa kwambiri amene amamvetsera?’ Mwinamwake mtumiki wodzifunira wa pa Beteli siwokondwa kwenikweni ndi ntchito yake. Mwina nkudwaladwala, ngakhale kuti sikungamsiyitse utumiki wa nthaŵi zonse, potsiriza kwamchotsera chimwemwe. Kodi oterowo angasunge motani chimwemwe chawo? Tiyeni tione zimene atumiki ena ozoloŵera akunena.

Kupirira Kukhumudwa

Anny, amene amachokera ku Switzerland, analoŵa nawo Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower mu 1950. Anayembekezera kutumizidwa kuntchito yaumishonale kumaiko akutsidya kwa nyanja. Pamene anatumizidwa kukagwira ntchito pa Beteli ku Ulaya, Anny anakhumudwa. Komabe, anavomera utumiki mu Dipatimenti Yotembenuza ndipo akugwirabe ntchito imeneyo. Kodi anakuthetsa motani kukhumudwa kwake? “Panali ntchito yambiri yoichita ndipo idakalipobe. Zofuna zanga ndi zosankha zanga sizili zofunika kwambiri monga ntchitoyi,” akutero Anny.

Ngati tili okhumudwa ndi ntchito yomwe tagaŵiridwa, mwina tiyenera kutsanzira maganizo a Anny. Zosankha zathu sindizo zofunika koposa. Chofunika kwambiri nchakuti maudindo onse okhudzana ndi kufalitsa uthenga wa Ufumu akusamaliridwa bwino. Miyambo 14:23 imatiuza kuti “m’ntchito zonse muli phindu.” Mosasamala kanthu kuti ndi utumiki wotani umene tapatsidwa, kuuchita mokhulupirika kumathandiza kukwaniritsa ntchito ya Ufumu. Ndipo pangakhale chikhutiro chachikulu​—inde, chimwemwe​—pantchito yopatsidwa ndi Mulungu imeneyo.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 12:18, 27, 28.

Kugwirizana ndi Ena

Utumiki wa nthaŵi zonse umapangitsa kuchita zinthu ndi anthu a mitundu yonse​—mu utumiki wakumunda, pa Beteli, panyumba za amishonale, mwina pochezera mpingo ndi mpingo monga woyang’anira woyendayenda. Motero, chimwemwe kwakukulukulu chimadalira pa kugwirizana ndi ena. Komabe, ‘nthaŵi zoopsa’ zonenedweratu za masiku ano otsiriza zimapangitsa maubwenzi a anthu kukhala ovuta. Kodi mtumiki angapeŵe motani kutaya chimwemwe chake, ngakhale ngati wina amkhumudwitsa? Mwina tikhoza kuphunzirapo kanthu kwa Wilhelm.

Wilhelm anakhala wa banja la Beteli ku Ulaya mu 1947. Kenako, anachita ntchito ya upainiya ndi kutumikira monga woyang’anira woyendayenda. “Ine ndi mkazi wanga tikaona kanthu kamene tiganiza kuti si kabwino kapena kamadetsa nkhaŵa, timauza Yehova mmene tikumvera ndiye kenaka timasiya zonse kwa iye kuti achitepo kanthu,” akulongosola motero Wilhelm.​—Salmo 37:5.

Mwinamwake inu mwininu mwavutikapo ndi khalidwe la Mkristu mnzanu amene analankhula nanu mopanda ulemu kapena mosalingalira. Kumbukirani kuti tonsefe timakhumudwa pa mawu. (Yakobo 3:2) Motero bwanji osagwiritsira ntchito mpata umenewu kuyandikira kwa “Wakumva pemphero”? (Salmo 65:2) Lankhulani kwa Yehova za chinthucho, ndiye kenako zisiyeni m’manja mwake. Ngati Mulungu afuna kusintha zinthu, adzatero. Awo amene amakhala m’nyumba za amishonale ayenera kukumbukira zimenezi ngati mavuto otere ayamba kuwapsinja maganizo, popeza zimenezi zidzawathandiza kukhalabe ndi chimwemwe mu utumiki kwa Yehova.

Ngati Mumadwaladwala

Ndi anthu ochepa amene amakhala ndi thanzi labwino nthaŵi zonse. Ngakhale amene amakhala moyo wapamwamba akhoza kupsinjika maganizo kapena kudwala. Kudwala kumapangitsa kukhala koyenera kwa ena kuleka utumiki wa nthaŵi zonse, komabe amachita bwino kwambiri pambuyo pake monga alaliki a Ufumu. Komabe, ena amatha kupitirizabe utumiki wa nthaŵi zonse ngakhale amadwaladwala. Mwachitsanzo, lingalirani za Hartmut ndi Gislind.

Hartmut ndi Gislind ndi okwatirana amene atha zaka 30 monga apainiya, amishonale, ndi m’ntchito yoyendayenda. Onsewa avutikapo ndi matenda aakulu amene nthaŵi zina ankawapangitsa kutheratu mphamvu ndiponso kugwa mphwayi. Komabe, achita ntchito yabwino ndipo akwanitsa kulimbikitsa ena omwe akukumana ndi ziyeso zofananazo. Kodi amapereka malangizo otani? “Yang’anani kutsogolo osati kumbuyo. Chitani zonse zomwe mungathe pamkhalidwe uliwonse. Tsiku lililonse lingapereke mpata umodzi basi wotamandira Yehova. Gwiritsirani ntchito mpata umenewo, ndipo sangalalani nawo.”

Lingalirani za Hannelore. Wavutika ndi matenda obwerezabwereza pazaka 30 zimene wakhala mpainiya, mmishonale, mu ntchito yoyendayenda ndi mwamuna wake, ndiponso mu utumiki wa pa Beteli. Hannelore akuti: “Ndimalingalira zankhani yodzutsidwa ndi Satana​—yakuti anthu amatumikira Yehova pokhapokha ngati kuchita zimenezo sikovuta. Mwa kupirira ziyeso, ndingakhale ndi mbali m’kusonyeza kuti Satana ndi wabodza.” Ichi chingakhale chilimbikitso chachikulu. Kumbukirani kuti kukhulupirika kwanu kwa Yehova pamene muli pachiyeso nkofunika kwa iye.​—Yobu 1:8-12; Miyambo 27:11.

Pamene mukuyesa kupanga chosankha choyenera malinga ndi thanzi lanu, lingalirani za mfundo ziŵiri za ulosi wa Yesu Kristu wonena za mapeto a dongosolo lino la zinthu. Yesu ananeneratu za miliri m’malo akutiakuti. Anatinso: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:3, 14; Luka 21:11) Yesu anadziŵa kuti m’masiku otsiriza, otsatira ake adzavutika ndi matenda. Komabe anadziŵa kuti ntchito yolalikira idzachitidwa osati ndi okhawo ali ndi thanzi labwino komanso ndi omwe amavutika ndi matenda aakulu. Ngati tingathe kupitiriza utumiki wa nthaŵi zonse ngakhale tilibe thanzi labwino, Yehova sadzaiŵala chikondi tikuchionetsera ku dzina lake.​—Ahebri 6:10.

Kukhalabe Achimwemwe Ngakhale Dziko Nlamphwayi

Mzimu wathu ungakhudzidwe ndi mmene anthu amachitira pantchito yathu yolalikira Ufumu. “Ngakhale apainiya zimawavuta kuyambitsa makambitsirano ndi mwini nyumba,” anatero mtumiki wina wozoloŵera. “Tonsefe timayenera kuyesayesa kuti tisungebe chimwemwe chathu.” Inde, mphwayi ya anthu ikhoza kuchepetsa chimwemwe chathu mu utumiki wakumunda. Choncho, kodi ndi motani mmene mpainiya amene kaŵirikaŵiri amakumana ndi anthu amphwayi angasungire chimwemwe chake? Atumiki ozoloŵera apereka malingaliro otsatirawa amene ayesedwa ndipo athandizadi.

Mphwayi imakhaladi vuto, koma siiyenera kutigonjetsa. Kuchuluka kwa anthu amphwayi kokhako sichifukwa cholekera utumiki wa nthaŵi zonse. Tikhoza kusungabe chimwemwe pamene tikulimbana ndi mphwayi ngati tikhala ndi nthaŵi yokwana yophunzira Malemba mwakhama. Iwo ‘amatikonzekeretsa kuchita ntchito iliyonse yabwino,’ ndipo zimenezi zimaphatikizapo kulankhula ndi anthu omwe samvetsera uthenga wabwino. (2 Timoteo 3:16, 17) Ngakhale kuti anthu sankafuna kumvetsera mneneri Yeremiya, sizinampangitse kuleka. (Yeremiya 7:27) Pamene tikuphunzira Baibulo mothandizidwa ndi zofalitsa zachikristu, tikhoza kupindula kwambiri ngati timaonapo malingaliro amene amalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutithandiza kulimbana ndi mphwayi.

Titavomereza kuti mphwayi ndi vuto, tiyeni tipende mzimu wathu, kwa aja amene timawalalikira. Kodi nchifukwa ninji ndi amphwayi? Mwachitsanzo, chifukwa chimodzi chochititsa mphwayi kufalikira mu Ulaya ndi mbiri yoipa ya chipembedzo chonyenga. Anthu saonanso kuti chipembedzo chili ndi ntchito iliyonse m’miyoyo yawo, ndiponso safuna kuchita kalikonse kokhudzana ndi chipembedzo. Tiyenera kumasintha, kukamba ndi anthu zinthu zomwe zimawakhudza, monga ulova, matenda, upandu, kusagwirizana, kuwonongeka kwa malo okhala, ndi chiopsezo cha nkhondo.

M’mawu athu oyamba kwa mwini nyumba, tikhoza kutchulapo kanthu kokhudza anthu akumaloko. Ndizo zomwe Dietmar anayesa kuchita pamene anali kulalikira m’mudzi mmene sankapezamo anthu okondwerera. Wina wa m’mudzimo ananena kuti mudziwo unali utakumana ndi tsoka dzulo lake. Atachoka pamenepo, Dietmar ankasonyeza chisoni chake chifukwa cha tsokalo pakhomo lililonse. “Modabwitsa, anthu anayamba kulankhula,” iye anatero. “Tsokalo linali m’maganizo mwa aliyense. Ndinali ndi makambitsirano abwino tsiku limenelo chifukwa ndinasonyeza chidwi pa miyoyo yawo.”

Tifunikira kupatsa anthu umboni wa Ufumu kulikonse kumene tingawapeze. Umboni wamwamwaŵi ungabale zipatso, ndipo tikhoza kudziphunzitsa zimenezi mwa kugwiritsira ntchito njira zoperekedwa m’zofalitsa zofotokoza Baibulo. Mukhoza kupeza chimwemwe mwakugwiritsira ntchito mawu aubwenzi pang’ono mwina mwa kugaŵira makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa mwini nyumba. Ngati tapanga maulendo obwereza ndipo tayamba phunziro la Baibulo ndi munthu wokondwerera, tikhoza kufunsa kuti: “Kodi mukudziŵapo aliyense yemwe angakonde kuphunzira Baibulo?” Zimenezi zingapangitse kuti tikhazikitse phunziro lina la Baibulo lapanyumba. Mulimonse momwe zingakhalire, tiyeni tikhale olimbikira, kudalira pa Yehova mwa pemphero, osalola kuti mphwayi zitifooketse.

Kulimbikitsidwa ndi Ena

Jürgen ndi Christiane akhala akuchita upainiya ndi kugwira ntchito yoyendayenda kwa zaka zoposa 30. Nthaŵi ina anagaŵiridwa kulalikira m’dera limene anthu ambiri anali amphwayi ndiponso oumirira zinthu. Jürgen ndi mkazi wake amachifuna motani nanga chilimbikitso! Komabe, pa zifukwa zina, ena mumpingo sanachitepo kanthu pa zomwe ankafunazo.

Motero Jürgen amazindikira kuchokera pa zokumana nazo zake kuti “Apainiya ena amakumana ndi mavuto. Amafunikira kulimbikitsidwa kwambiri ndi akulu ndiponso ofalitsa ena.” Mulungu anauza Mose kulimbikitsa ndi kulimbitsa Yoswa. (Deuteronomo 3:26-28) Ndiponso Akristu ayenera kumalimbikitsana. (Aroma 1:11, 12) Olengeza Ufumu akhoza kulimbikitsa amene ali mu utumiki wa nthaŵi zonse mwa mawu olimbikitsa ndiponso mwa kutsagana nawo mu utumiki nthaŵi ndi nthaŵi.

Chimwemwe cha Yehova​—Mphamvu Yathu

Akristu amene athera nthaŵi yaitali yamoyo wawo monga apainiya kapena amishonale, kutumikira pa Beteli, kapena kuchezera mipingo m’ntchito yoyendayenda apeza kuti mavuto ambiri amatenga nthaŵi yochepa, koma ena amakhalitsa. Ngakhale mavuto amene amaoneka ngati kuti sadzachoka sayenera kutichotsera chimwemwe. Ramon, amene watumikira kumaiko ena kwazaka zoposa 45, akupereka ganizo lakuti nthaŵi iliyonse pamene mavuto atichititsa chisoni, “tiyenera kuganizira za madalitso ambiri amene tili nawo ndiponso zikwizikwi za ena amene amavutika ndi mavuto aakulupo.” Ndithudi, okhulupirira anzathu akukumana ndi mavuto padziko lonse lapansi, ndipo Yehova amasamaliradi za ife tonse.​—1 Petro 5:6-9.

Choncho, ngati ife mpata utilola kuti tichite nawo utumiki wa nthaŵi zonse ndi kupitirizabe kuuchita, tiyeni tisungebe chimwemwe mwakudalira pa Atate wathu wakumwamba. Amalimbikitsa atumiki ake, ndipo tonsefe tiyenera kukumbukira kuti ‘chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yathu.’​—Nehemiya 8:10.

[Chithunzi patsamba 21]

“Zofuna zanga ndi zosankha zanga sizili zofunika kwambiri monga ntchitoyi”

[Chithunzi patsamba 22]

“Timauza Yehova mmene tikumvera ndiye kenaka timasiya zonse kwa iye”

[Zithunzi patsamba 23]

“Chitani zonse zomwe mungathe pamkhalidwe uliwonse. Tsiku lililonse lingapereke mpata umodzi basi wotamandira Yehova”

[Chithunzi patsamba 23]

“Mwa kupirira ziyeso, ndingakhale ndi mbali m’kusonyeza kuti Satana ndi wabodza”

[Zithunzi patsamba 24]

“Apainiya ena amakumana ndi mavuto. Amafunikira kulimbikitsidwa kwambiri ndi akulu ndiponso ofalitsa ena”

[Chithunzi patsamba 24]

“Tiyenera kuganizira za madalitso ambiri amene tili nawo”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena