Chochitika Chosangalatsa Kumaliza Maphunziro kwa Kalasi la 104 la Gileadi
“LERO ndi tsiku losangalatsa, ndipo tonsefe tikukondwera.” Ndi mawu amenewo Carey Barber, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anatsegulira mwambo wa patsiku lomaliza maphunziro a kalasi la 104 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower pa March 14, 1998. Omvetsera okwanira 4,945 anapemphedwa kuti ayambe chochitikacho mwa kuimba nyimbo ya Ufumu nambala 208, ya mutu wakuti “Nyimbo ya Chikondwelero.”
Uphungu Wothandiza Kuti Munthu Akhalebe Wachimwemwe
Mbali yotsegulira programuyo inali ndi nkhani za Baibulo zisanu zazifupi zotsatizana, zomwe zinapereka uphungu wothandiza wa mmene iwo angapitirizire kukhala ndi mzimu wachimwemwe umene unali patsiku lomaliza maphunzirolo.
Nkhani yoyamba inakambidwa ndi Joseph Eames wa m’Dipatimenti Yolemba. Mutu wa nkhani yake unali wakuti “Tsanzirani Mzimu wa Okhulupirika,” yozikidwa pa nkhani ya m’Baibulo ya pa 2 Samueli machaputala 15 ndi 17, yomwe imasimba kuti Abisalomu, mwana wa Davide, anachita chiŵembu chofuna kulanda ufumu wa atate wake wopatsidwa ndi Mulungu mwa kuyambitsa chipanduko. Komabe, panali anthu ena amene anakhalabe okhulupirika kwa wodzozedwa wa Yehova, Mfumu Davide. Kodi amishonale atsopanowo anatengapo phunziro lotani pamenepa? “Kulikonse kumene mudzapita pantchito yanu yaumishonale, mokhulupirika, kulitsani mzimu wogwirizana ndi anzanu ndiponso wolemekeza ulamuliro wateokrase. Thandizani ena kuchita zofananazo,” anamaliza motero Mbale Eames.
Wotsatira kukambapo pa programuyo anali David Sinclair, amene anafotokoza za ziyeneretso khumi, zotchulidwa mu Salmo 15, zokhalira ogonera ‘m’chihema mwa Yehova.’ Nkhani yake, ya mutu wakuti “Pitirizani Kukhala Monga Ogonera m’Chihema Chanu Chaumishonale,” inalimbikitsa ophunzira omaliza maphunzirowo kuti akagwiritsire ntchito salmo limeneli m’magawo awo aumishonale, kumene akakhale ngati ogonera. Mbale Sinclair anagogomezera za kufunika kwa kukhala mogwirizana ndi malamulo aumulungu nthaŵi zonse. Chotsatirapo chake? Salmo 15:5 limafotokoza kuti: “Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka ku nthaŵi zonse.”
John Barr, wa m’Bungwe Lolamulira, anatsatira ndipo anasumika maganizo pa mphamvu yolimbikitsa ya kuimba nyimbo pamisonkhano yachikristu. Koma kodi nyimbo yosangalatsa kwambiri imene ikuimbidwa padziko lonse lapansi lerolino ndi iti? Ndi nyimbo ya uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu Waumesiya. Kodi chikutsatirapo nchiyani pa kuimba konseku, kapena kulalikira za Ufumuwo? Vesi lachiŵiri la nyimbo nambala 208 limanena mosapita m’mbali kuti: “Mwakulalika ndi kuphunzitsa, ambiri adza kwa Yehova. Amaimbanso mosangalala, zikumamveka konsekonse!” Inde, tsiku lililonse ophunzira atsopano pafupifupi 1,000 akubatizidwa. Mbale Barr anamaliza ndi mawu akuti: “Abale inu, kodi si zosangalatsa kulingalira kuti mukutumizidwa kumagawo kumene mukakumana ndi anthu amene akhala akungoyembekezera kumvetsera nyimbo yanu yachitamando?”
“Mvetserani Mawu a Ozoloŵera,” unali mutu wa nkhani yotsatira yomwe inakambidwa ndi James Mantz wa m’Dipatimenti Yolemba. Iye anafotokoza kuti zinthu zina ungangoziphunzira mwa kuyang’anizana nazo iwemwini. (Ahebri 5:8) Komabe, Miyambo 22:17 imatilimbikitsa ‘kutchera makutu athu ndi kumvera mawu a anzeru,’ kapena ozoloŵera. Ophunzira omaliza maphunzirowo angaphunzire zambiri kwa amene anayamba kale ntchitoyo. “Iwo amadziŵa kukambirana ndi ogulitsa m’masitolo a kumaloko. Amadziŵa madera a mumzindamo amene ayenera kuwapeŵa pokana kuvulazidwa mwakuthupi kapena kukumana ndi anthu amakhalidwe oipa. Amadziŵa kuti kaya anthu a kumaloko amakwiya msanga kapena ayi. Amishonale omwe akhala akugwira ntchitoyi kwa nthaŵi yaitali amadziŵa zinthu zimene muyenera kuchita kuti mukhale achimwemwe ndiponso achipambano m’gawo lanu,” anatero Mbale Mantz.
Pokamba nkhani yakuti “Yamikirani Magawo Anu a Teokrase,” Wallace Liverance, wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi, anafotokoza kuti pamene kuli kwakuti amishonale ena, monga mtumwi Paulo, Timoteo, ndiponso Barnaba, analandira ntchito zawozo kuchokera kwa Mulungu mwa mzimu woyera kapena mwa chochitika china chozizwitsa, amishonale ophunzitsidwa pa Gileadi amapatsidwa munda wa padziko lonse ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Iye anayerekezera magawo a amishonale ndi malo amene Gideoni anagaŵira amuna ake amene anali kuyembekezera kuthira nkhondo Amidyani. (Oweruza 7:16-21) “Yamikirani magawo anu aumishonale ateokrase. Mongadi momwe ankhondo a Gideoni ‘anaimira yense m’mbuto mwake,’ onani gawo lanu monga mbuto imene muyenera kukhalapo. Khulupirirani kuti Yehova angakugwiritsireni ntchito monga momwe anagwiritsirira ntchito amuna a Gideoni mazana atatu,” analimbikitsa motero Mbale Liverance.
Kukonda Anthu Kumadzetsa Chimwemwe
Nsanja ya Olonda nthaŵi ina inati: “M’malo mokondetsa katundu ndi zipangizo za m’dongosolo lino, zinthu zomwe zilibe chitsimikizo chakuti zingakhale nthaŵi yaitali, kuli bwino ndiponso nkwanzeru chotani nanga kuti tizikonda anthu kwambiri ndiponso kuphunzira kupeza chimwemwe chenicheni mwa kuchitira zinthu ena.” Mogwirizana ndi zimenezo, Mbale Mark Noumair, mmodzi mwa alangizi a m’Sukulu ya Gileadiyo, anakambirana ndi gulu la ophunziralo za zokumana nazo zawo za mu utumiki wakumunda ndipo anati: “Kukonda anthu ena ndiko kumene kukakupangitsani kukhala amishonale abwino.”
Zinthu Zodzetsa Chimwemwe m’Munda wa ku Dziko Lina
Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimadzetsa chipambano ndi chimwemwe m’ntchito yaumishonale? Mbale Charles Woody wa m’Dipatimenti ya Utumiki ndiponso Mbale Harold Jackson, mmishonale wakale wa ku Latin America yemwenso ndi wothandizira m’Komiti Yophunzitsa, anafunsa mamembala a m’Makomiti Anthambi zosiyanasiyana amene anali kuphunzira m’kalasi lachisanu ndi chinayi la sukulu ya oyang’anira nthambi. Otsatirawa ndi ena mwa malangizo amene iwo anapereka:
Albert Musonda wa ku Zambia anati: “Pamene mmishonale ayamba ndiye kupereka moni kwa abale, zimenezi zimakulitsa mzimu wabwino kwambiri chifukwa chakuti abalewo adzayandikira kwa mmishonaleyo, ndipo mmishonaleyo adzayandikiranso kwa iwo.”
Rolando Morales wa ku Guatemala anafotokoza kuti pamene amishonale atsopanowo apatsidwa chakumwa ndi anthu okoma mtima, iwo angayankhe moleza mtima ndiponso mochenjera kuti: “Ndine mlendo m’dziko muno. Ndinafunitsitsa nditamwa ndithu, koma thupi langa lilibe mphamvu yodziteteza yofanana ndi yomwe ili m’thupi mwanu. Ndikhulupirira kuti tsiku lina ndidzamwa, ndipo ndidzakhala wosangalala kuchita zimenezo.” Kodi mapindu a kuyankha kotero ngotani? “Anthu sadzakhumudwa, ndipo amishonalewo adzasonyeza kukoma mtima kwa ena.”
Kodi nchiyani chomwe chingathandize amishonale kupirira m’magawo awo? Mbale Paul Crudass, yemwe anaphunzira m’kalasi la 79 la Gileadi, amene wakhala akutumikira ku Liberia kwa zaka 12 tsopano, anafotokoza zotsatirazi: “Ndimadziŵa kuti makolo amalakalakadi kuonana ndi ana awo. Koma pamakhala nthaŵi zina pamene mmishonale amayesetsa kuzoloŵerana ndi dzikolo, kumene akukhala, mwambo wake, ndi anthu ake. Iye mwina angalingalire zobwerera kwawo. Ngati alandira kalata yochokera kumudzi yonena kuti, ‘Tapukwa kwambiri; sitikudziŵa kuti tidzatani,’ zimenezi zingamsonkhezere kulongedza katundu m’chola chake ndi kubwerera kumudzi. Nkofunika kwambiri kuti abale a amishonale amene muli pano lerolino muzikumbukira zinthu zimenezi.”
Atatsiriza kufunsako, nkhani yomaliza ya programuyo inakambidwa ndi Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira. Mutu wake unali wakuti: “Ikani Ufumu Pamalo Oyamba m’Moyo Wanu.” Kodi ndi motani mmene amishonalewo angasumikirebe maganizo ndi kusachenjenetsedwa pantchito yawo? Iye anawalimbikitsa kuti azikhala ndi ndandanda ya phunziro la Baibulo laumwini, limene lidzawathandiza kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’moyo wawo. Ndipo panalinso chokumbutsa chapanthaŵi yake chakuti: “Amishonale ena anyalanyaza phunziro laumwini chifukwa chomwerekera ndi zipangizo zamagetsi, mauthenga a pakompyuta, ndiponso makompyuta enieniwo. Tiyenera kumalinganiza zinthu bwino kuti tikhale ochita zinthu mwachikatikati pogwiritsira ntchito chipangizo chilichonse ndipo tisataye nthaŵi yambiri pa chinthu chimene chingachenjenetse phunziro lathu laumwini la Mawu a Mulungu.”
Itatha nkhani ya Mbale Jaracz tsopano inali nthaŵi yopereka madipuloma ndi kuŵerenga kalata yachiyamiko yolembedwa ndi kalasilo. Woimira kalasilo anafotokoza za malingaliro a aliyense wa iwo kuti: “Taona umboni waukulu wa chikondi chomwe Yesu ananena kuti chidzakhala chizindikiro cha ophunzira ake, ndipo zimenezi zatitsimikiziranso kuti mosasamala kanthu za kumene tili, pali gulu longa mayi, lokoma mtima ndi lachikondi lotichirikiza. Mwa chichirikizo chimenechi, ife tili okonzeka kupita kumalekezero a dziko lapansi.” Kumeneku kunali kumaliza kokhudza mtima kwa tsiku losangalatsa la kumaliza maphunziro kwa kalasi la 104 la Gileadi.
[Bokosi patsamba 24]
Ziŵerengero za Kalasi
Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 9
Chiŵerengero cha maiko kumene anatumizidwa: 16
Chiŵerengero cha ophunzira: 48
Chiŵerengero cha mabanja: 24
Avareji ya zaka zakubadwa: 33
Avareji ya zaka m’choonadi: 16
Avareji ya zaka mu utumiki wanthaŵi zonse: 12
[Chithunzi patsamba 25]
Kalasi la 104 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.
(1) Romero, M.; Howarth, J.; Blackburne-Kane, D.; Hohengasser, E.; West, S.; Thom, S. (2) Colon, W.; Glancy, J.; Kono, Y.; Drews, P.; Tam, S.; Kono, T. (3) Tam, D.; Zechmeister, S.; Gerdel, S.; Elwell, J.; Dunec, P.; Tibaudo, H. (4) Taylor, E.; Hildred, L.; Sanches, M.; Anderson, C.; Bucknor, T.; Hohengasser, E. (5) Howarth, D.; Ward, C.; Hinch, P.; McDonald, Y.; Sanches, T.; Thom, O. (6) Drews, T.; Tibaudo, E.; Elwell, D.; Dunec, W.; Blackburne-Kane, D.; Ward, W. (7) Anderson, M.; Zechmeister, R.; McDonald, R.; Bucknor, R.; Glancy, S.; Gerdel, G. (8) Romero, D.; Hinch, R.; Hildred, S.; Taylor, J.; Colon, A.; West, W.
[Chithunzi patsamba 26]
Abale amene analangiza nawo kalasi la 104: (kuyambira kulamanzere) W. Liverance, U. Glass, K. Adams, M. Noumair