Yehova Wokonda Chilungamo ndi Chiweruzo
KAMSUNGWANA kena ku Sarajevo kakudzifunsa chifukwa chake ana a mumzinda wakwawo akuvutika kwambiri. “Sitinachite chilichonse. Ndife osalakwa,” iko kakutero. Anakubala ovutika maganizo a ku Argentina achita chionetsero pabwalo la onse mu Buenos Aires kwa zaka 15, ponena za kuzimiririka kwa ana awo aamuna. Munthu wina wa mu Afirika wotchedwa Emmanuel, amene amake ndi alongo ake atatu anaphedwa mwankhanza mkati mwa kuulika kwa chiwawa cha mafuko, akunena motsimikiza kuti: “Aliyense ayenera kulandira mphotho yake yomuyenerera . . . Tikufuna chiweruzo choyenera.”
Chiweruzo chili umodzi wa mikhalidwe yaikulu ya Yehova Mulungu. “Njira zake zonse ndi chiweruzo,” Baibulo limatero. Indedi, Yehova ndiye “wakukonda chilungamo ndi chiweruzo.” (Deuteronomo 32:4; Salmo 33:5) Kuti timdziŵe bwino Mulungu, tiyenera kumvetsa lingaliro lake la chiweruzo ndi kuphunzira kulitsanzira.—Hoseya 2:19, 20; Aefeso 5:1.
Lingaliro lathu pa chiweruzo mwinamwake laumbidwa ndi mmene anthu amaulingalirira mkhalidwewu. M’mbali zina za dziko, kaŵirikaŵiri chiweruzo chimasonyezedwa monga mkazi amene wamangidwa kumaso atagwira m’manja lupanga ndi muyezo. Chiweruzo cha anthu chifunikira kukhala chopanda tsankhu, ndiko kuti, chosayang’ana pa chuma kapena mphamvu za munthu. Chiyenera kupima mosamalitsa woimbidwa mlandu kuti aone ngati ali ndi liwongo kapena alibe liwongo. Limodzi ndi lupanga lake, chiweruzo chiyenera kutetezera opanda liwongo ndi kulanga ochimwa.
Buku lakuti Right and Reason—Ethics in Theory and Practice likunena kuti “chiweruzo nchogwirizana ndi lamulo, thayo, zoyenera, ndi mangawa, ndipo chimapereka chigamulo chake molinganiza kapena moyenerera.” Koma chiweruzo cha Yehova chimaposa pamenepo. Tingathe kuona zimenezi mwa kulingalira zochita ndi mikhalidwe ya Yesu Kristu, amene ali wofanana kwambiri ndi Atate wake wakumwamba.—Ahebri 1:3.
Mawu a Yesaya 42:3 anagwiritsidwa ntchito pa Yesu ndi mlembi wa Uthenga Wabwino Mateyu, amene anati: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi laŵi lozirala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m’zoona.” Yesu analengeza za uthenga wotonthoza kwa anthu amene anali ngati bango lophwanyika limene linapindidwa ndi kupondedwa. Anali ngati laŵi lozirala la nyali, monga ngati kuti mphamvu yawo ya moyo yomaliza inali itatsala pang’ono kutha. M’malo mwa kupera mabango ophwanyika mophiphiritsira ndi kuzima malaŵi oziralawo, Yesu anachitira chifundo odwala, anawaphunzitsa ndi kuwachiritsa, ndipo anamveketsa kwa iwo chiweruzo cha Yehova Mulungu. (Mateyu 12:10-12) Monga momwe ulosi wa Yesaya unaneneratu, chiweruzo cha mtundu umenewo chinasonkhezera chiyembekezo.
Chifundo ndi Chiweruzo cha Yehova
Chifundo chili mbali yofunika ya chiweruzo cha Mulungu. Zimenezi zinadziŵika pamene Yesu anali padziko lapansi. Iye anasonyeza mwangwiro miyezo ya Mulungu ya chiweruzo ndi chilungamo. Komabe, alembi achiyuda ndi Afarisi anafunafuna chilungamo mwa kutsatira malamulo ouma—ochuluka ake odzipangira. Chiweruzo chawo choumirira pa malamulo mopambanitsa nthaŵi zambiri chinali chopanda chifundo. Mikangano yambiri pakati pa Yesu ndi Afarisi inazikika pankhani iyi: Kodi chiweruzo ndi chilungamo choona nzotani?—Mateyu 9:10-13; Marko 3:1-5; Luka 7:36-47.
Yesu anasonyeza mmene tingachitire ndi ena moyenera ndi molungama. Mwamuna wina yemwe anadziŵa bwino Chilamulo panthaŵi ina anafunsa Yesu za chimene chinafunika kuti adzalandire moyo wosatha. Poyankha Yesu anamfunsa funso ndi kumuyamikira pamene anayankha kuti malamulo aŵiri ofunika koposa anali a kukonda Mulungu ndi mtima wonse, moyo wonse, nzeru zonse, ndi mphamvu zonse za munthu ndi kukonda mnansi wake monga iye mwini. Ndiyeno mwamunayo anafunsa kuti: “Mnansi wanga ndani?” Yesu anayankha mwa kufotokoza fanizo la Msamariya wachifundo.—Luka 10:25-37.
Chilungamo cha Yehova ndi chiweruzo cha chifundo zinasonyezedwa m’fanizo la Yesu la Msamariya. Mwa kuthandiza munthu wovulazidwa mopanda dyera amene sanamdziŵe, Msamariyayo anachita chinthu china, cholungama, choyenera ndi chachifundo. Yesu mwiniyo anasonyeza mzimu umodzimodziwo pamene anali padziko lapansi. Anali wolungama. Ndiponso, anataya moyo wake chifukwa cha anthu osauka, chifukwa cha anthu ochimwa ndi opanda ungwiro omavutika, kudwala, ndi kufa. Mtumwi Paulo anagwirizanitsa chilungamo ndi makonzedwe a dipo. Iye analemba kuti: “Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.” (Aroma 5:18) “Chilungamitso chimodzi” chimenechi chinali njira ya Mulungu yopulumutsira anthu omvera pa zotulukapo zowopsa za uchimo wa Adamu, umene sunali mlandu wawo.
Chiweruzo cha Mulungu chinafuna kuwombola anthu ochimwa ndipo panthaŵi imodzimodziyo kuchirikiza mapulinsipulo olungama. Kunyalanyaza tchimo kukanakhala ponse paŵiri kupanda chilungamo ndi kupanda chikondi, pakuti kukanachirikiza kusayeruzika. Komanso, ngati chiweruzo cha Mulungu chikanangokhala cha kupereka chilango, mkhalidwe wa anthu ukanakhala wopanda chiyembekezo. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, “mphotho yake ya uchimo ndi imfa” ndipo “palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi.” (Aroma 3:10; 6:23) Mwa kudzimana kwake kwakukulu ndi kwa Mwana wake wokondedwa, Yehova anapereka nsembe ya chiombolo cha machimo athu.—1 Yohane 2:1, 2.
Dipo limasonyeza kuti chiweruzo chaumulungu nchosanganizidwa ndi chikondi chalamulo (Chigiriki, a·gaʹpe). Indedi, chiweruzo cha Mulungu ndicho chipatso cha mapulinsipulo ake olungama—chisonyezero cha khalidwe lake. Chotero, pamene Mulungu achigwiritsira ntchito, chiweruzo chaumulungu chimazikidwa pa chikondi cha a·gaʹpe. (Mateyu 5:43-48) Chotero ngati tizindikira chiweruzo cha Yehova, tidzakhala ndi chikhulupiriro chotheratu m’zigamulo zake zachiweruzo. Monga “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” iye nthaŵi zonse amachita zimene zili zabwino.—Genesis 18:25; Salmo 119:75.
Tsanzirani Chiweruzo cha Yehova
Baibulo limatilimbikitsa ‘kukhala akutsanza a Mulungu.’ (Aefeso 5:1) Zimenezi zimatanthauza kutsanzira chiweruzo chake ndiponso chikondi chake. Komabe, popeza kuti ndife opanda ungwiro, njira zathu sizili zapatali monga zija za Yehova Mulungu. (Yesaya 55:8, 9; Ezekieli 18:25) Chotero kodi tingasonyeze motani kuti ndife okonda chilungamo ndi chiweruzo? Mwa ‘kuvala munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ (Aefeso 4:24) Pamenepo tidzakonda zimene Mulungu amakonda ndi kuda zimene amada. “Chilungamo” chimada chiwawa, makhalidwe oipa, chidetso, ndi mpatuko, pakuti zimenezi zimaipitsa zinthu zoyera. (Salmo 11:5; Aefeso 5:3-5; 2 Timoteo 2:16, 17) Chiweruzo cha Mulungu chimatisonkhezeranso kusonyeza chidwi chathu mwa ena.—Salmo 37:21; Aroma 15:1-3.
Ndiponso, ngati tizindikira mkhalidwe wachifundo wa chiweruzo cha Mulungu, sitidzakhala okonda kuweruza abale ndi alongo athu. Kodi tingawamvetse motani monga momwe Yehova amachitira? Kodi sitidzawaweruza ndi lingaliro lathulathu lopotoka? Nchifukwa chake Yesu anachenjeza kuti: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nawo, kudzayesedwa kwa inunso. Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m’diso lakoli. Wonyenga iwe! tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.” (Mateyu 7:1-5) Kudzipenda koona mtima kwa kupanda ungwiro kwathu kudzatiletsa kupereka ziweruzo zimene Yehova adzaziona kukhala zosalungama.
Akulu ampingo oikidwa ali ndi thayo la kuweruza milandu ya cholakwa chachikulu. (1 Akorinto 5:12, 13) Pochita zimenezo, amakumbukira kuti chiweruzo cha Mulungu chimafuna kuti chifundo chisonyezedwe ngati kuli koyenera. Ngati palibe maziko ake—monga momwe zilili ndi ochimwa osalapa—chifundo sichingasonyezedwe. Koma akulu samathamangitsa wolakwa mumpingo chifukwa cha kufuna kubwezera. Amakhulupirira kuti mchitidwe wa kuchotsawo udzamchititsa kulingalira bwino. (Yerekezerani ndi Ezekieli 18:23.) Pansi pa umutu wa Kristu, akulu amachirikiza chiweruzo, ndipo zimenezi zimaphatikizapo kukhala monga “pobisalira mphepo.” (Yesaya 32:1, 2) Chotero ayenera kusonyeza kusakondera ndi nzeru.—Deuteronomo 1:16, 17.
Bzalani m’Chilungamo
Pamene tikuyembekezera dziko latsopano la Mulungu lolungama, tiyenera ‘kufuna chilungamo’ kuti tipeze chiyanjo cha Mulungu. (Zefaniya 2:3; 2 Petro 3:13) Lingaliro limeneli lafotokozedwa bwino kwambiri m’mawu awa, opezeka pa Hoseya 10:12: “Mudzibzalire m’chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthaŵi ya kufuna Yehova, mpaka afika iye, navumbitsira inu chilungamo.”
M’moyo wathu watsiku ndi tsiku, tili ndi mipata yambiri ya ‘kubzala m’chilungamo,’ monga momwe Yesu anasonyezera m’fanizo lake la Msamariya wachifundo. Yehova adzaonetsetsa kuti ‘tikukolola monga mwa chifundo.’ Ngati tiyendabe “m’njira ya chiweruzo,” tidzapitiriza kulandira malangizo m’chilungamo pansi pa ulamuliro wa Ufumu. (Yesaya 40:14) Pamene nthaŵi ikupyola, mosakayikira tidzazindikira bwino kwambiri kuti Yehova ndiye wokonda chilungamo ndi chiweruzo.—Salmo 33:4, 5.
[Chithunzi patsamba 23]
Msamariya wachifundo anasonyeza chiweruzo cha Yehova
[Chithunzi patsamba 23]
Yesu anachitira chifundo anthu odwala, amene anali ngati mabango ophwanyika