Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/1 tsamba 14-19
  • Chuma Chathu m’Zotengera Zadothi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chuma Chathu m’Zotengera Zadothi
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuumbidwa mu Israyeli Wakale
  • Kuumba Mtundu Wauzimu
  • Kuumba Israyeli wa Mulungu Lerolino
  • “Taonani! Khamu Lalikulu”
  • Woumba Wamkulu ndi Ntchito Yake
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Mzimu wa Moyo Wochokera kwa Mulungu Unawalowera”
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Uyang’aniro Wateokrase m’Nthaŵi ya Akristu
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Tiziyamikira Kuti Yehova Amatiumba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/1 tsamba 14-19

Chuma Chathu m’Zotengera Zadothi

“Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.”​—2 AKORINTO 4:7.

1. Kodi chitsanzo cha Yesu chiyenera kutilimbikitsa motani?

PAMENE anali kuumbidwa ndi Yehova pano padziko lapansi, Yesu anadzionera mmene mtundu wa anthu ulili wofooka. Chitsanzo chake cha kukhala wokhulupirika chiyeneradi kutilimbikitsa! Mtumwi wina anati: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Mwa kugonjera ku kuumbidwa koteroko, Yesu anapambana dziko. Iye analimbikitsanso atumwi ake kuti akhale olakika. (Machitidwe 4:13, 31; 9:27, 28; 14:3; 19:8) Ndipo anaperekatu chilimbikitso champhamvu m’mawu ake omalizira a nkhani yomaliza imene anawakambira! Iye anati: “Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.”​—Yohane 16:33.

2. Mosiyana ndi khungu la dzikoli, kodi ife tili ndi chiwalitsiro chotani?

2 Mofananamo, atasiyanitsa khungu lochititsidwa ndi “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano” ndi “chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero,” mtumwi Paulo ponena za utumiki wathu wamtengo wapatali anati: “Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife; ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osawonongeka.” (2 Akorinto 4:4, 7-9) Ngakhale kuti ndife “zotengera zadothi” zofooka, Mulungu watiumba ndi mzimu wake kuti tilake kotheratu dziko la Satana.​—Aroma 8:35-39; 1 Akorinto 15:57.

Kuumbidwa mu Israyeli Wakale

3. Kodi Yesaya anafotokoza motani kuumbidwa kwa mtundu wachiyuda?

3 Yehova samangoumba anthu okha komanso mitundu yathunthu. Mwachitsanzo, pamene Israyeli wakale anagonjera ku kuumba kwa Yehova, anali kupeza bwino. Koma potsirizira pake anaumitsa mtima wake nakhala wosamvera. Chotsatirapo chake chinali chakuti Mlengi wa Israyeli anabweretsa “tsoka” pa Israyeliyo. (Yesaya 45:9) M’zaka za zana la chisanu ndi chitatu B.C.E., Yesaya analankhula ndi Yehova ponena za kuchimwa kwakukulu kwa Israyeli, nati: “Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu. . . . Zinthu zathu zonse zokondweretsa zapasuka.” (Yesaya 64:8-11) Israyeli anali ataumbidwa kukhala chotengera chimene chinali kuyenerera chiwonongeko chokha basi.

4. Kodi Yeremiya anachita fanizo lotani?

4 Zaka zana limodzi pambuyo pake, pamene tsiku lowaŵerengera mlandu linali kuyandikira, Yehova anauza Yeremiya kuti atenge nsupa ya dothi ndi kutsagana ndi akuluakulu ena a Yerusalemu kupita ku Chigwa cha Hinomu, namulangiza kuti: “Uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe, nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu aŵa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso.”​—Yeremiya 19:10, 11.

5. Kodi chiweruzo cha Yehova pa Israyeli chinali chachikulu motani?

5 Mu 607 B.C.E., Nebukadinezara anasakaza Yerusalemu pamodzi ndi kachisi wake ndipo anatenga Ayuda amene anapulumuka ukapolo napita nawo ku Babulo. Koma atatha zaka 70 ali mu ukapolo, Ayuda olapa anabwereranso kwawo ndi kukamanganso Yerusalemu ndi kachisi wake. (Yeremiya 25:11) Komabe, pomafika m’zaka za zana loyamba C.E., mtunduwo unali utamusiyanso Woumba Wamkuluyo, ndipo pamapeto pake unafikira pochitadi upandu waukulu wa kupha Mwana wake wa Mulungu. Mu 70 C.E., Mulungu anagwiritsa ntchito Ulamuliro wa Dziko Lonse wa Aroma ngati wakupha wake posesa dongosolo la zinthu lachiyuda, napera Yerusalemu ndi kachisi wake. Mtundu wa Israyeli sunali kudzaumbidwanso ndi dzanja la Yehova monga chinthu ‘chopatulika ndi chokongola.’a

Kuumba Mtundu Wauzimu

6, 7. (a) Kodi Paulo anafotokoza motani kuumbidwa kwa Israyeli wauzimu? (b) Kodi chiŵerengero chonse cha “zotengera zachifundo” ndi chotani, ndipo chinapangidwa motani?

6 Ayuda amene analandira Yesu anaumbidwa monga maziko a mtundu watsopano, “Israyeli wa Mulungu” wauzimu. (Agalatiya 6:16) Motero mawu a Paulo aŵa alidi oyenerera: “Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi? . . . Ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziŵitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko? ndi kuti Iye akadziŵitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero.”​—Aroma 9:21-23.

7 Kenako Yesu woukitsidwayo anadziŵikitsa kuti “zotengera zachifundo” zimenezi zidzakwanira 144,000. (Chivumbulutso 7:4; 14:1) Popeza kuti Israyeli wakuthupi analephera kupereka chiŵerengero chonse chimenecho, Yehova anasonyeza chifundo chake kwa anthu amitundu. (Aroma 11:25, 26) Mpingo wachikristu watsopanowo unakula mofulumira. M’zaka 30 zokha uthenga wabwino unali ‘kulalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Zimenezi zinafuna kuti pakhale uyang’aniro wabwino pa mipingo yambirimbiriyo yomwe inali yomwazikanamwazikana.

8. Ndani amene anapanga bungwe lolamulira loyambirira, ndipo kodi bungweli linakula motani?

8 Yesu anakonza atumwi 12 kuti akhale bungwe lolamulira loyambirira, nawaphunzitsa pamodzi ndi ena za utumiki. (Luka 8:1; 9:1, 2; 10:1, 2) Pa Pentekoste wa 33 C.E., mpingo wachikristu unakhazikitsidwa, ndipo patapita nthaŵi bungwe lake lolamulira linakulitsidwa kuti liphatikizepo ‘atumwi ndi akulu ku Yerusalemu.’ Kukuoneka kuti kwa nthaŵi yaitali mbale wake wa Yesu Yakobo, ngakhale kuti sanali mtumwi, anali tcheyamani. (Machitidwe 12:17; 15:2, 6, 13; 21:18) Malinga ndi kunena kwa wolemba mbiri Eusebius, atumwi ndiwo amene makamaka anali kuzunzidwa ndipo anamwazikana n’kukakhala m’madera ena. Amene anali kupanga bungwe lolamuliralo anasinthidwa mogwirizana ndi kumwazikako.

9. Kodi ndi zinthu zomvetsa chisoni ziti zimene Yesu ananeneratu kuti zidzachitika?

9 Chakumapeto kwa zaka za zana loyamba, ‘mdani, Mdyerekezi,’ anayamba ‘kufesa namsongole’ pakati pa oloŵa a “Ufumu wa Kumwamba” amene ali ngati tirigu. Yesu ananeneratu kuti zinthu zomvetsa chisoni zimenezi zidzaloledwa kuchitika mpaka panthaŵi yakututa pa “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Ndiyeno, kachiŵirinso, “olungamawo adzawalitsa monga dzuŵa, mu Ufumu wa Atate wawo.” (Mateyu 13:24, 25, 37-43) Kodi zimenezo zikachitika liti?

Kuumba Israyeli wa Mulungu Lerolino

10, 11. (a) Kodi kuumbidwa kwa Israyeli wa Mulungu kwa makono kunayamba motani? (b) Kodi ndi ziphunzitso zosiyana ziti zimene zinapezeka m’Dziko Lachikristu ndi pakati pa Ophunzira Baibulo akhama?

10 Mu 1870, Charles Taze Russell anapanga gulu lophunzira Baibulo ku Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A. Mu 1879 anayamba kufalitsa kamodzi pa mwezi magazini imene lerolino ikudziŵika kuti Nsanja ya Olonda. Ophunzira Baibulo ameneŵa, monga momwe anadzatchedwera, posapita nthaŵi anazindikira kuti Dziko Lachikristu linali litatenga ziphunzitso zachikunja zosakhala za m’malemba, monga ngati kusafa kwa mzimu, moto wa helo, puligatoliyo, mulungu wa Utatu, ndi kubatiza makanda.

11 Komabe, chofunika kwambiri chinali chakuti anthu okonda choonadi cha Baibulo ameneŵa anabwezeretsa ziphunzitso zazikulu za Baibulo, monga ngati kuomboledwa kupyolera mwa nsembe yadipo ya Yesu ndi kuukitsidwira ku moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso lamtendere mu Ufumu wa Mulungu. Koposa zonse, anagogomezera kuti posachedwapa kudzatsimikiziridwa kuti Yehova Mulungu ndiye Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse. Ophunzira Baibulowo anakhulupirira kuti Pemphero la Ambuye linali pafupi kuyankhidwa lakuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Anali kuumbidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu kukhala gulu la padziko lonse la Akristu okonda mtendere.

12. Kodi ndi motani mmene Ophunzira Baibulo anafikira pozindikira deti lofunika kwambiri?

12 Kuphunzira mozama Danieli chaputala 4 pamodzi ndi maulosi ena kunakhutiritsa maganizo Ophunzira Baibulowo kuti kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu ya Umesiya kunali pafupi. Anazindikira kuti 1914 idzakhala chaka chimene “nthaŵi zawo za anthu akunja” zidzatha. (Luka 21:24; Ezekieli 21:26, 27) Ophunzira Baibulo anafutukula ntchito yawo mofulumira, napanga makalasi a Baibulo (kenako anadzatchedwa kuti mipingo) mu United States monse. Pamene zaka za zana la 19 zinali kutha, ntchito yawo yophunzitsa Baibulo inafika ku Ulaya ndi Australasia. Panali kufunika kolinganiza zinthu bwino.

13. Kodi Ophunzira Baibulo anachitanji kuti azidziŵika mwalamulo, ndipo kodi ndi utumiki wabwino wotani umene pulezidenti woyamba wa Sosaite anachita?

13 Kuti Ophunzira Baibulowo azidziŵika mwalamulo, Zion’s Watch Tower Tract Society inalembetsedwa mu 1884 ku United States, ndipo likulu lake linali ku Pittsburgh, Pennsylvania. Otsogolera ake anatumikira monga Bungwe Lolamulira, loyang’anira kulalikira Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Pulezidenti woyamba wa Sosaiteyo, Charles T. Russell, analemba mavoliyumu asanu ndi limodzi a buku lotchedwa Studies in the Scriptures ndipo anapanga maulendo ochuluka okalalikira. Anaperekanso ndalama zambiri zimene anapeza asanayambe kuphunzira Baibulo ku ntchito yaufumu ya padziko lonseyo. Mu 1916, pamene Nkhondo Yaikulu inali mkati ku Ulaya, Mbale Russell wotopayo anamwalira paulendo wolalikira. Anali atapereka zake zonse kuti afutukule ntchito yochitira umboni Ufumu wa Mulungu.

14. Kodi ndi motani mmene J. F. Rutherford ‘anamenyera nkhondo yabwino’? (2 Timoteo 4:7, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono)

14 Joseph F. Rutherford, amene kwa nthaŵi yochepa anali woweruza ku Missouri, anakhala pulezidenti wotsatira. Chifukwa cha kuchirikiza kwake choonadi cha Baibulo mosaopa, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anagwirizana ndi anthu andale pa ‘kupanga vuto mogwiritsa ntchito lamulo.’ Pa June 21, 1918, Mbale Rutherford pamodzi ndi atsogoleri ena asanu ndi aŵiri a Ophunzira Baibulo anaponyedwa m’ndende, atapatsidwa ziweruzo zochuluka panthaŵi imodzi zoti akhale m’ndende zaka 10 kapena 20. Ophunzira Baibulowo analimbana ndi vutolo. (Salmo 94:20, NW; Afilipi 1:7) Atachita apilo anawatulutsa pa March 26, 1919, ndipo kenaka anawauza kuti analibe mlandu pa nkhani yabodza ya kupandutsa anthu.b Zimenezi zinawaumba kukhala ochirikiza choonadi amphamvu. Ndi chithandizo cha Yehova, anagwiritsa ntchito njira iliyonse kuti apambane nkhondo yauzimu yolalikira uthenga wabwino mosasamala kanthu za chitsutso cha Babulo Wamkulu. Nkhondo imeneyo ikupitirizabe mpaka chaka chino cha 1999.​—Yerekezerani ndi Mateyu, chaputala 23; Yohane 8:38-47.

15. Kodi n’chifukwa chiyani chaka cha 1931 chili chofunika m’mbiri?

15 Mu ma 1920 ndi ma 1930, Israyeli wa Mulungu wodzozedwayo anapitiriza kuumbidwa motsogozedwa ndi Woumba Wamkuluyo. Kuwala kwaulosi kuchokera m’Malemba kunali kuunika, kukumapereka ulemu kwa Yehova ndi kusumikitsa malingaliro a anthu pa Ufumu wa Umesiya wa Yesu. Mu 1931 Ophunzira Baibulo anali osangalala kulandira dzina latsopano lakuti Mboni za Yehova.​—Yesaya 43:10-12; Mateyu 6:9, 10; 24:14.

16 ndi bokosi patsamba 19. Kodi ndi liti pamene chiŵerengero chonse cha 144,000 chinakwana, ndipo kodi pali umboni wotani wa zimenezi?

16 Mu ma 1930 chiŵerengero cha awo “oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika,” a 144,000, chinaoneka kukhala chitakwanira. (Chivumbulutso 17:14; onani bokosi patsamba 19.) Sitikudziŵa kuti ndi anthu angati odzozedwa amene anasonkhanitsidwa m’zaka za zana loyamba ndiponso pakati pa “namsongole” m’kati mwa mazana a zaka za mdima a mpatuko waukulu wa Dziko Lachikristu. Koma mu 1935 panali chiwonkhetso cha ofalitsa 52,465, mwa chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 56,153 padziko lonse, amene anasonyeza kuti ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba mwa kudya zizindikiro za pa Chikumbutso. Kodi anthu ochuluka amene anali kudzasonkhanitsidwabewo anali kudzayembekezeranji?

“Taonani! Khamu Lalikulu”

17. Kodi ndi chochitika chosaiwalika chotani chimene chinachitika mu 1935?

17 Pamsonkhano womwe unachitika ku Washington, D.C., U.S.A., kuyambira pa May 30 kufika pa June 3, 1935, Mbale Rutherford anakamba nkhani imene inasintha zinthu yokhala ndi mutu wakuti “Gulu Lalikulu.”c Gulu limeneli, limene “palibe munthu anakhoza kuliŵerenga,” lidzaoneka pamene kusindikiza chizindikiro cha a 144,000 a Israyeli wauzimu kufika kumapeto. Aŵanso adzakhala ndi chikhulupiriro m’mphamvu ya kuombola ya ‘mwazi wa Mwanawankhosa,’ Yesu, ndi kumapereka utumiki wopatulika m’makonzedwe a kachisi wolambirira wa Yehova. Monga gulu, iwo ‘adzatuluka m’chisautso chachikulu’ amoyo, kuti akalandire dziko lapansi la Paradaiso mmene ‘simudzakhalanso imfa.’ Kwa zaka zingapo msonkhano umenewo usanachitike, gulu limeneli linali kunenedwa kuti ndi a Yonadabu.​—Chivumbulutso 7:9-17; 21:4; Yeremiya 35:10.

18. Kodi ndi motani mmene chaka cha 1938 chinalili chofunika kwambiri?

18 Chaka cha 1938 chinali chofunika kwambiri pa kuzindikiritsa bwino lomwe magulu aŵiri ameneŵa. Makope a March 15 ndi April 1, 1938, a Nsanja ya Olonda a Chingelezi analongosola nkhani yophunzira ya mbali ziŵiri yakuti “Nkhosa Zake” ndipo inasonyeza bwino lomwe malo a otsalira odzozedwa ndi a mabwenzi awo, a khamu lalikulu. Ndiyeno makope a June 1 ndi June 15 anali ndi nkhani zophunzira zonena za “Gulu,” zochokera pa Yesaya 60:17. Mipingo yonse inafunsidwa kupempha Bungwe Lolamulira kuti liike atumiki a m’mipingo yomweyo, motero kuyambitsa makonzedwe a teokalase abwino, okhazikitsidwa ndi Mulungu. Mipingo inachitadi zimenezi.

19 ndi mawu a mtsinde. Kodi ndi mfundo ziti zimene zikutsimikizira kuti chiitano chachisawawa cha “nkhosa zina” chapitirizabe kwa zaka zoposa 60 tsopano?

19 Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 1939 inapereka lipoti lakuti: “Atsatiri odzozedwa a Kristu Yesu amene tsopano ali padziko lapansi ndi ochepa, ndipo chiŵerengero chawo sichidzawonjezereka. M’Malemba iwoŵa akutchedwa ‘otsalira’ a mbadwa za Ziyoni, gulu la Mulungu. (Chiv. 12:17) Ambuye tsopano akusonkhanitsa ‘nkhosa zake zina,’ zimene zidzapanga ‘gulu lalikulu’. (Yohane 10:16) Awo amene tsopano lino akusonkhanitsidwa ndi mabwenzi awo a otsalira, akugwira ntchito limodzi ndi otsalirawo. Kuchokera panthaŵi ino kumka m’tsogolo, awo amene akupanga ‘nkhosa zina’ adzachuluka mpaka ‘gulu lalikulu’ limeneli litasonkhanitsidwa.” Otsalira odzozedwa anali ataumbidwa kuti asonkhanitse khamu lalikululi. Ameneŵanso ayenera kuumbidwa tsopano.d

20. Kodi gulu lakhala likusintha motani kuyambira mu 1942?

20 Mu January 1942, pamene Nkhondo Yadziko II inali pachimake, Joseph Rutherford anamwalira ndipo Nathan Knorr anakhala pulezidenti m’malo mwake. Pulezidenti wachitatu wa Sosaite amakumbukiridwa kwambiri chifukwa choyambitsa masukulu a teokalase m’mipingo ndiponso Sukulu ya Gileadi yophunzitsa amishonale. Pamsonkhano wapachaka wa Sosaite mu 1944, iye analengeza kuti mpambo wa mfundo zoyendetsera Sosaite anali kuukonzanso kuti anthu okhala mamembala ake azikhala anthu auzimu osati kutengera zinthu zakuthupi zimene munthu amapereka. M’zaka 30 zotsatira, chiŵerengero cha anthu ogwira ntchito m’munda padziko lonse chinawonjezeka kuchoka pa 156,299 kufika pa 2,179,256. Mu 1971-75 panali kufunika kwakuti gulu lisinthe mowonjezereka. Munthu amene anali pulezidenti sanalinso kudzayang’anira yekha ntchito yonse ya Ufumu padziko lonse. Bungwe Lolamulira, limene mamembala ake amasinthanasinthana utcheyamani, linakulitsidwa kuti likhale ndi mamembala odzozedwa 18, amene pafupifupi theka la iwo tsopano anamaliza ntchito yawo ya padziko lapansi.

21. Kodi n’chiyani chimene chayeneretsa a kagulu kankhosa kulandira Ufumu?

21 Ena otsalawo a kagulu ka nkhosa aumbidwa pokumana ndi ziyeso kwa zaka zambiri. Ndi olimbadi mtima, pokhala atalandira mosaphonya ‘umboni wa mzimu.’ Yesu anawauza kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.”​—Aroma 8:16, 17; Luka 12:32; 22:28-30.

22, 23. Kodi a kagulu ka nkhosa ndi a nkhosa zina akuumbidwa motani?

22 Pamene chiŵerengero cha otsalira odzozedwa ndi mzimu amene ali padziko lapansi chatsika, abale ofikapo a khamu lalikulu apatsidwa uyang’aniro wauzimu pafupifupi m’mipingo yonse padziko lonse. Ndipo pamene Mboni zodzozedwa zokalamba zomalizira zitsiriza ntchito yawo ya padziko lapansi, oyang’anira a sa·rimʹ a nkhosa zina adzakhala ataphunzitsidwa bwino kuti azikagwira ntchito za uyang’aniro monga ngati kagulu ka akalonga padziko lapansi.​—Ezekieli 44:3; Yesaya 32:1.

23 A kagulu ka nkhosa pamodzi ndi a nkhosa zina akupitiriza kuumbidwa kukhala zotengera zaulemu. (Yohane 10:14-16) Kaya chiyembekezo chathu ndi cha “kumwamba kwatsopano” kapena cha “dziko lapansi latsopano,” tiyenitu tilabadire ndi mtima wonse chiitano cha Yehova chakuti: “Khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu [wakumwamba] wosangalala, ndi anthu ake okondwa.” (Yesaya 65:17, 18) Tiyenitu ife anthu ofooka tizitumikira modzichepetsa nthaŵi zonse, tikumaumbidwa ndi “ukulu woposa wamphamvu”​—mphamvu ya Mulungu ya mzimu woyera!​—2 Akorinto 4:7; Yohane 16:13.

[Mawu a M’munsi]

a Dziko Lachikristu lopanduka, lomwe linachitiridwa chitsanzo ndi Israyeli wakale, lichenjezedwetu za chiweruzo cha Yehova chofananacho.​—1 Petro 4:17, 18.

b Judge Manton, wa Roma Katolika amene anakaniza kutulutsa Ophunzira Baibulo pabelo, anadzamangidwa ndi iyeyo kenako, atapezeka kuti analandira ziphuphu.

c New World Translation of the Christian Greek Scriptures, yofalitsidwa mu 1950, imagwiritsa ntchito mawu akuti “khamu lalikulu” monga matembenuzidwe abwino a liwu louziridwa lachigiriki.

d Mu 1938 anthu onse amene anafika pa Chikumbutso padziko lonse anali 73,420, ndipo anthu 39,225​—53 peresenti ya onse amene analipo​—anadya zizindikiro. Pofika 1998 chiŵerengero cha ofikapo chinakula kufika pa 13,896,312, pamene anthu 8,756 chabe ndiwo amene anadya, avareji ya wosakwanira pa munthu mmodzi ku mipingo 10 iliyonse.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Pogonjera ku kuumba kwa Atate wake, kodi ndi motani mmene Yesu analili Wotipatsa Chitsanzo?

◻ Kodi ndi kuumbidwa kotani kumene kunachitika mu Israyeli wakale?

◻ Kodi ndi motani mmene “Israyeli wa Mulungu” wakhala akuumbidwira kufika tsopano?

◻ Kodi “nkhosa zina” zakhala zikuumbidwa pa cholinga chotani?

[Bokosi patsamba 18]

Kuumbidwa Kwinanso m’Dziko Lachikristu

Kuchokera ku Athens, Greece, Associated Press inatumiza lipoti lotsatirali ponena za mkulu wa Tchalitchi cha Greek Orthodox amene anasankhidwa posachedwapa: “Akuyenera kukhala mthenga wa mtendere. Koma mtsogoleri wa Tchalitchi cha Greek Orthodox akumveka ngati kazembe amene akukonzekera nkhondo.

“‘Ngati kuli kofunika, ife tili okonzeka kukhetsa mwazi ndi kudzipereka nsembe. Monga tchalitchi, ife timapempherera mtendere . . . Koma timadalitsa zida zopatulika nthaŵi ikafuna kuti titero,’ anatero Archbishop Christodoulos posachedwapa pa tsiku loyera la Kutengeredwa Kumwamba kwa Namwali, limene lilinso tsiku lokumbukira asilikali a Greece.”

[Bokosi patsamba 19]

“Palibe Kuwonjezeka!”

Pamwambo womaliza maphunziro a Gileadi mu 1970, Frederick Franz, amene panthaŵiyo anali wachiŵiri kwa pulezidenti wa Watch Tower Society, anauza ophunzira kuti ndi kotheka kuti iwo, amene onse anali a nkhosa zina okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi, angakabatize munthu wina amene anganene kuti ndi wotsalira wa odzozedwa. Kodi zimenezi zingachitike? Eya, iye anati Yohane Mbatizi anali wa nkhosa zina koma anabatiza Yesu ndi atumwi ena. Ndiyeno anapitirira kufunsa ngati padakali chiitano chakuti enanso a otsalira asonkhanitsidwe. Iye anati: “Ayi, palibe kuwonjezeka! Chiitano chimenecho chinatha kale m’mbuyomo mu ma 1931-35! Palibe amene akuwonjezeka. Nanga ena ochepa amene ayanjana ndi gulu posachedwapa amene amadya zizindikiro za pa Chikumbutso ndi ndani? Ngati ali otsalira, iwo ndi oloŵa m’malo! Iwo sakuwonjezeka ku gulu la odzozedwa, koma akuloŵa m’malo amene ataya chikhulupiriro.”

[Chithunzi patsamba 15]

Timayamikiratu kwambiri chuma chathu cha utumiki!

[Chithunzi patsamba 16]

Israyeli wakale anakhala chotengera chimene chinali kuyenerera chiwonongeko chokha basi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena