Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/15 tsamba 9-12
  • Mabanja Aakulu Ogwirizana Potumikira Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabanja Aakulu Ogwirizana Potumikira Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mabanja Aakulu Lerolino
  • Makolo Ayenera Kukhala Anthu Auzimu
  • Kugwirizana Ngati Timu
  • Kulankhulana Kwabwino, Zolinga Zofanana
  • Kudalira Yehova
  • Musaleme!
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Makolo—Kodi Ana Anu Akukula Mwauzimu?
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kukwaniritsa Udindo wa Kusamalira Banja
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/15 tsamba 9-12

Mabanja Aakulu Ogwirizana Potumikira Mulungu

“Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova,” analemba motero wamasalmo. “Chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake.”​—Salmo 127:3-5.

INDE, ana angakhaledi dalitso lochokera kwa Yehova. Ndipo monga momwe katswiri woponya mivi amakhutira podziŵa kulunjikitsa mivi ili m’phodo lake, makolonso amasangalala pamene alunjikitsa ana awo panjira ya kumoyo wosatha.​—Mateyu 7:14.

Kalekale, panali mabanja ochuluka pakati pa anthu a Mulungu amene ‘anadzaza mapodo’ awo ndi ana ambiri. Mwachitsanzo, taganizani za zaka zawo za ukapolo mu Igupto: “Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nawo.” (Eksodo 1:7) Kuyerekeza chiŵerengero cha Aisrayeli amene analoŵa m’dziko la Igupto ndi cha amene anatuluka kumaonetsa kuti panali mabanja okhala ndi ana khumi. Mabanja ambiri anali aakulu chomwecho.

Patapita zaka zambirimbiri, Yesu anakulira m’banja limene ambiri lero angaganize kuti n’lalikulu kwambiri. Yesu anali woyamba, koma Yosefe ndi Mariya analinso ndi ana ena aamuna anayi komanso aakazi. (Mateyu 13:54-56) Kukhala kwawo ndi ana ambiri kungakhale chifukwa chimene Mariya ndi Yosefe anayambira ulendo wobwerera kwawo kuchokera ku Yerusalemu popanda kuzindikira kuti Yesu panalibe pagulupo.​—Luka 2:42-46.

Mabanja Aakulu Lerolino

Lerolino, Akristu ambiri amasankha kuchepetsa mabanja awo pazifukwa zauzimu, zachuma, zakakhalidwe, ndi zinanso. Ngakhale zili choncho, m’madera ena mabanja aakulu adakali chizoloŵezi. Malinga ndi The State of the World’s Children 1997, dera limene amabereka ana ambiri ndi chigawo cha Afirika cha kummwera kwa Sahara. Kumeneko, akazi ambiri amakhala ndi ana asanu ndi mmodzi.

Kwa makolo achikristu amene mabanja awo n’ngaakulu, n’kovuta kulera anawo kuti azikonda Yehova, koma ambiri akuchita zimenezo. Kuti zitheke, banja lifunikira kukhala logwirizana pa kulambira koyera. Mawu a mtumwi Paulo ku mpingo wa Korinto amagwiranso ntchito m’mabanja achikristu lerolino. Analemba kuti: “Koma ndikudandaulirani inu, abale, . . . kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mumtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.” (1 Akorinto 1:10) Kodi umodzi umenewo ungakhalepo motani?

Makolo Ayenera Kukhala Anthu Auzimu

Chofunika kwambiri n’chakuti makolo ayenera kukhala odzipereka kwambiri kwa Mulungu. Tamverani zimene Mose anauza Aisrayeli: “Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi; ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”​—Deuteronomo 6:4-7.

Onani kuti Mose ananena kuti malamulo a Mulungu anafunikira kukhala ‘pamitima’ ya makolowo. Pokhapokha zitatero m’pamene makolowo akafuna kuphunzitsa ana awo malangizo auzimu nthaŵi zonse. Inde, pamene makolo ali olimba mwauzimu, amafunitsitsa kuphunzitsa ana awo zinthu zauzimu.

Kuti ukhale wauzimu ndi wokonda Yehova ndi mtima wako wonse, ufunikira nthaŵi zonse kuŵerenga Mawu a Mulungu, kuwasinkhasinkha, ndi kuwatsata. Wamasalmo analemba kuti amene akonda chilamulo cha Yehova ndi kuchiŵerenga ‘usana ndi usiku akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake panyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.’​—Salmo 1:2, 3.

Monga momwe mtengo umabalira zipatso zabwino akamautsirira nthaŵi zonse, mabanjanso amene amadya mwauzimu amabala zipatso zaumulungu zotamanda Yehova. Mwachitsanzo, pali banja la a Uwadiegwu, amene akhala ku West Africa. Ngakhale kuti a Uwadiegwuwo ndi akazi awo ali ndi ana asanu ndi atatu, iwo ndi akazi awo ali apainiya okhazikika, kapena kuti atumiki anthaŵi zonse a Mboni za Yehova. Iwo anati: “Takhala tikuphunzira Baibulo nthaŵi zonse monga banja zaka zoposa 20. Taphunzitsa ana Mawu a Mulungu kuyambira pamene anali akhanda, osati chabe paphunziro lathu la banja komanso mu utumiki ndi panthaŵi zina. Ana athu onse amalengeza uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo wamng’ono pa onse, amene ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi, ndiye yekha amene sanabatizidwebe.”

Kugwirizana Ngati Timu

“Nzeru imangitsa nyumba,” limatero Baibulo. (Miyambo 24:3) M’banja, nzeru yoteroyo imapangitsa onse kugwirizana ngati timu. “Kaputeni” wa timu la banja ndi atate; ndiwo mutu woikidwa ndi Mulungu panyumbapo. (1 Akorinto 11:3) Mtumwi Paulo anafotokoza mouziridwa kukula kwake kwa udindo wa umutu pamene analemba kuti: “Ngati wina sadzisungiratu [pa zakuthupi ndi zauzimu zomwe] mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”​—1 Timoteo 5:8.

Mogwirizana ndi uphungu umenewu wa m’Mawu a Mulungu, amuna achikristu ayenera kusamalira mkhalidwe wauzimu wa akazi awo. Ngati akazi alemetsedwa ndi ntchito zapanyumba, mkhalidwe wawo wauzimu umawonongeka. M’dziko lina mu Afirika, Mkristu wobatizidwa chatsopano anadandaulira akulu mumpingo kuti mkazi wake sakonda zinthu zauzimu. Akulu anamuuza kuti iye afunikira kumathandizana ndi mkazi wake. Choncho mwamunayo anayamba kuthandizana ntchito zapanyumba ndi mkazi wake. Anam’thandizanso kuphunzira kuŵerenga ndi kuwonjeza chidziŵitso chake cha Baibulo. Mkaziyo analabadira, ndipo panopa banja lonse n’logwirizana kutumikira Mulungu.

Atate afunikanso kusamala za mkhalidwe wauzimu wa ana awo. Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Pamene makolo alabadira langizoli lakuti asakwiyitse ana awo, limodzinso ndi la kuwaphunzitsa, anawo amaona kuti ali m’timu ya banja. Chotero, anawo akhoza kumathandizana ndi kulimbikitsana kuti akwanitse zolinga zauzimu.

Kugwirizana monga timu kumafunanso kupatsa ana maudindo auzimu pamene angaŵasamalire. Atate wina, mkulu wachikristu wa ana 11, amadzuka mmamaŵa ndi kuphunzira ndi ana ake angapo asanapite kuntchito. Ana aakulu atabatizidwa, amasinthana kuthandiza ang’ono awo aamuna ndi aakazi, kuphatikizapo kuwaphunzitsa Baibulo. Atateyo amayang’anira ntchitoyo ndi kuwayamikira. Ana asanu ndi mmodzi ndi obatizidwa, ndipo enawo akulimbikira kuti apeze cholinga chomwecho.

Kulankhulana Kwabwino, Zolinga Zofanana

Chofunika kuti banja ligwirizane ndicho kulankhulana kwachikondi ndi kukhala ndi zolinga zofanana zauzimu. Gordon, mkulu wachikristu amene akhala ku Nigeria, ndi atate wa ana asanu ndi aŵiri oyambira pa zaka 11 mpaka 27. Asanu ndi mmodzi ndi apainiya, monganso makolo. Wotsirizira, amene anabatizidwa posachedwapa, mokhazikika amachita ntchito yopanga ophunzira limodzi ndi banja. Ana aakulu aŵiri aamuna ndi atumiki otumikira mumpingo.

Gordon ankachititsa yekha maphunziro a Baibulo ndi aliyense wa ana akewo. Ndiponso, banjalo lili ndi pologalamu yatsatanetsatane yophunzira Baibulo. Mmaŵa uliwonse amakumana kupenda lemba la Baibulo kenako kukonzekera misonkhano ya mpingo.

Chimodzi cha zolinga za aliyense m’banja ndicho kuŵerenga nkhani zonse za m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!. Posachedwapa, anawonjeza kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku pa pologalamu yawoyo. Chifukwa chosimba zimene aŵerenga, banjali limalimbikitsana kupitiriza chizoloŵezicho.

Phunziro la Baibulo la banja la mlungu ndi mlungu n’lokhazikika bwino moti safunikira kukumbutsana​—aliyense amaliyembekezera. Zaka zonsezi, zophunziridwa, kaphunziridwe, ndi utali wa nthaŵi ya phunziro la banja zasinthasintha malinga ndi misinkhu ya ana ndi zosoŵa zawo. Banjali layandikana kwambiri ndi atumiki ena okhulupirika a Mulungu, ndipo zimenezi zawapindulitsa anawo.

Pokhala banja, amachitira zinthu pamodzi ndipo amakhala ndi nthaŵi yosangalala. Kamodzi pamlungu, amakhala ndi “madzulo a banja,” pamene amakhala ndi zilapi, nthabwala zabwino, kuliza piyano, nthano, ndi kusangalala kwachisawawa. Nthaŵi zina, amapita kunyanja ndi malo ena osangalatsa.

Kudalira Yehova

Zili pamwambazi sizikuchepetsa vuto lolera mabanja aakulu. “N’zovuta kwambiri kukhala atate wabwino kwa ana asanu ndi atatu,” anatero Mkristu wina. “Amafuna chakudya chenicheni ndiponso chauzimu chochuluka; ndiyenera kugwira ntchito kwambiri kuti ndipeze ndalama zokwanira kuwasamalira. Ana ena n’ngachinyamata, ndipo onse asanu ndi atatuwo ali pasukulu. Ndikudziŵa kuti chiphunzitso chauzimu n’chofunika kwambiri, koma ana anga ena n’ngaliuma komanso osamvera. Amandikwiyitsa, koma ndidziŵa kuti nthaŵi zina inenso ndimachita zinthu zokwiyitsa mtima wa Yehova, ndipo iye amandikhululukira. Chotero ndiyenera kupitiriza kuwalanga moleza mtima ana anga kufikira atazindikira kulakwa kwawo.

“Ndimayesa kutsata chitsanzo cha Yehova pakuti iye amaleza nafe mtima chifukwa afuna kuti tonse tilape. Ndimaphunzira ndi banja langa, ndipo ana anga ena akufuna kubatizidwa. Sindidalira nyonga yanga kuti zimenezi zitheke; mphamvu zanga sizingachite zambiri. Ndimayesa nthaŵi zonse kuyandikana kwambiri ndi Yehova m’pemphero ndi kutsata mwambi umene umati: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.’ Yehova adzandithandiza kuchita ntchito yophunzitsa ana anga.”​—Miyambo 3:5, 6.

Musaleme!

Nthaŵi zina ntchito yophunzitsa ana ingaoneke ngati ena sakuiyamikira, koma inu musasiye! Limbikirani! Ngati ana anu salabadira kapena sayamikira zoyesayesa zanu panopo, angadzatero m’kupita kwa nthaŵi. Kumatenga nthaŵi kuti mwana akule kukhala Mkristu wobala zipatso za mzimu.​—Agalatiya 5:22, 23.

Monica, amene akhala ku Kenya, ali mmodzi wa ana khumi. Iyeyo anati: “Makolo anatiphunzitsa choonadi cha Baibulo kuyambira ukhanda wathu. Atate ankaphunzira nafe mabuku achikristu mlungu uliwonse. Chifukwa cha ntchito yawo, phunzirolo linkachitika masiku osiyanasiyana. Nthaŵi zina, poweruka ku ntchito, ankatipeza tikuseŵera panja ndipo ankatiuza kuti patapita mphindi zisanu, tonse tiloŵe m’nyumba kukaphunzira Baibulo. Titamaliza phunziro lathu la Baibulo, ankatilimbikitsa kufunsa mafunso kapena kukambirana zothetsa nzeru zilizonse.

“Iwo ankaonetsetsa kuti tikuyanjana ndi ana oopa Mulungu. Nthaŵi ndi nthaŵi atate ankapita kusukulu kwathu kukafunsa aphunzitsi za khalidwe lathu. Paulendo wina anawauza kuti achimwene anga aakulu atatu anali atamenyana ndi anyamata ena ndi kuti nthaŵi zina ankachita chipongwe. Atate anawalanga chifukwa cha kusamvera kwawo, komanso anakhala nawo pansi kuwafotokozera mwa Malemba chifukwa chake anafunikira kukhala ndi khalidwe loopa Mulungu.

“Makolo anatisonyeza mapindu ake a kufika pamisonkhano mwa kukonzekera misonkhanoyo limodzi nafe. Tinaphunzitsidwa kukhala atumiki mwa kuchita pulakatisi kunyumba. Kuyambira ukhanda, tinkapita nawo makolowo ku utumiki wakumunda.

“Lero, achimwene anga aakulu aŵiri ali apainiya apadera, mchemwali wanga ndi mpainiya wokhazikika, ndipo winanso, wokwatiwa komanso wokhala ndi banja, ndi Mboni yokangalika. Achemwali anga aang’ono aŵiri, wazaka 18 ndi wazaka 16, ndi ofalitsa obatizidwa. Anyamata aang’ono aŵiri akuphunzitsidwa. Ndakhala ndikutumikira paofesi ya nthambi ya Kenya ya Mboni za Yehova zaka zitatu. Ndimawakonda makolo anga ndipo ndimawayamikira chifukwa ndi anthu auzimu; anatiikira chitsanzo chabwino.”

Kaya muli ndi ana angati, musasiye kuwathandiza panjira ya kumoyo wosatha. Pamene Yehova adalitsa khama lanu, mudzanenanso mawu onenedwa ndi mtumwi Yohane za ana ake auzimu: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.”​—3 Yohane 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena