Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 7/1 tsamba 18-22
  • Mabanja, Tamandani Mulungu Monga Mbali ya Mpingo Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabanja, Tamandani Mulungu Monga Mbali ya Mpingo Wake
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuumba Mtima
  • Kukonzekera Misonkhano ya Mpingo
  • Kukonzekera Utumiki Wakumunda kwa Banja
  • Pitirizani Kuwaphunzitsa Njira ya Yehova
  • Mitu ya Mabanja—Khalanibe ndi Ndandanda Yabwino Yochitira Zinthu Zauzimu
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Mphatso Yothandiza kwa Mabanja
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 7/1 tsamba 18-22

Mabanja, Tamandani Mulungu Monga Mbali ya Mpingo Wake

“M’masonkhano ndidzalemekeza Yehova.”​—SALMO 26:12.

1. Kuphatikiza pa kuphunzira ndi kupemphera kunyumba, kodi mbali ina yofunika ya kulambira koona ndi iti?

KULAMBIRA Yehova sikuphatikizapo kupemphera ndi kuphunzira Baibulo kunyumba kokha komanso zochita zina monga mbali ya mpingo wa Mulungu. Aisrayeli akale analamulidwa ‘kusonkhanitsa anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono,’ kuti aphunzire chilamulo cha Mulungu kotero kuti akayende m’njira yake. (Deuteronomo 31:12; Yoswa 8:35) Onse okalamba komanso ‘anyamata ndi anamwali’ analimbikitsidwa kutenga mbali m’kutamanda dzina la Yehova. (Salmo 148:12, 13) Makonzedwe ofananawo akugwiranso ntchito mumpingo wachikristu. M’Nyumba za Ufumu padziko lonse lapansi, amuna, akazi, ndi ana momasuka amatengamo mbali m’zochitika zimene zimaloŵetsamo omvetsera, ndipo ambiri amasangalala kwambiri pochita zimenezi.​—Ahebri 10:23-25.

2. (a) Kodi ndi chifukwa chiyani kukonzekera kuli chinthu chofunika kwambiri pothandiza ana kusangalala ndi misonkhano? (b) Kodi ndi chitsanzo chayani chimene chili chofunika?

2 Zoonadi, ndi kovuta kuthandiza ana kukhala ndi chizoloŵezi chabwino cha zochita zampingo. Ngati ana ena amene amafika pamisonkhano ndi makolo awo amaoneka kuti sasangalala nayo, kodi vuto lingakhale chiyani? Zoonadi, ana ambiri amakhala tcheru kwa nthaŵi yochepa ndipo zinthu sizikhalira kuwatopetsa. Kukonzekera kungathandize kuthetsa vuto limeneli. Popanda kukonzekera, misonkhano singakhale yatanthauzo lililonse kwa ana. (Miyambo 15:23) Popanda kukonzekera, kudzakhala kovuta kuti iwo apite patsogolo mwauzimu kumene kumadzetsa chikhutiro. (1 Timoteo 4:12, 15) Kodi tingachite chiyani? Choyamba, makolo afunika kudzifunsa ngati iwowo amakonzekera misonkhano. Chitsanzo chawo n’chisonkhezero champhamvu. (Luka 6:40) Kulinganiza bwino phunziro labanja kulinso kofunika kwambiri.

Kuumba Mtima

3. Paphunziro labanja, kodi ndi chifukwa chiyani muyenera kuyesetsa mwapadera kuti muumbe mitima, ndipo kodi zimenezi zimafunanji?

3 Nthaŵi ya phunziro labanja iyenera kukhala nthaŵi osati chabe yodzaza chidziŵitso m’mitu komanso iyenera kukhala nthaŵi youmba mitima. Izi zimafuna kuti muzizindikira mavuto amene anthu a m’banja lanu akukumana nawo ndi kusonyeza chisamaliro chachikondi kwa aliyense m’banjamo. Yehova ‘amayesa mtima.’​—1 Mbiri 29:17.

4. (a) Kodi kukhala “wosoŵa nzeru” kumatanthauzanji? (b) Kodi ‘kulandira nzeru’ kumaphatikizapo chiyani?

4 Kodi Yehova amapezanji pamene ayesa mitima ya ana athu? Ambiri anganene kuti amakonda Mulungu, ndipo zimenezi ndi zoyamikirika. Komabe, mwana kapena munthu amene akuphunzira kumene za Yehova sadziŵa njira zochuluka za Yehova. Chifukwa chakuti ndi mwana, iye angakhale “wosoŵa nzeru,” monga momwe Baibulo limanenera. Mwinamwake si zolinga zake zonse zimene zili zoipa, koma pamatenga nthaŵi kuti munthu apangitse mtima wake kukhala mumkhalidwe umene umasangalatsadi Mulungu. Izi zimaphatikizapo kuchititsa maganizo ako, zokhumba zako, zokonda zako, malingaliro ako, ndi zolinga zako m’moyo kukhala zogwirizana ndi zimene Mulungu amavomereza, kufika pamene zimenezi zingakhale zotheka kwa anthu opanda ungwiro. Pamene munthu aumba umunthu wake wamkati moteromo m’njira yaumulungu, ndiye kuti iye ‘akulandira nzeru.’​—Miyambo 9:4; 19:8.

5, 6. Kodi makolo angawathandize bwanji ana awo ‘kulandira nzeru’?

5 Kodi makolo angathandize ana awo ‘kulandira nzeru’? Zoonadi, palibe munthu amene angapatse munthu mnzake mtima wabwino. Aliyense wa ife anapatsidwa ufulu wakudzisankhira, ndipo zambiri zimadalira pa zimene ifeyo timalingalira. Komabe mwa kuzindikira, makolo nthaŵi zambiri angachititse mwana wawo kunena zakukhosi kwake, akumazindikira zimene zili mumtima mwake ndiponso mbali zimene akufunika thandizo. Gwiritsani ntchito mafunso onga akuti ‘Kodi ukumva bwanji ndi zimenezi?’ ndi ‘Kodi ukufuna utachita chiyani kwenikweni?’ Ndiyeno, mvetserani modekha. Musachite zinthu mopsa mtima. (Miyambo 20:5) Ndi kofunika kukhala wachifundo, womvetsetsa, ndi wachikondi ngati mukufuna kuwafika pamtima.

6 Kuti mulimbikitse malingaliro abwino, nthaŵi ndi nthaŵi kambiranani za chipatso cha mzimu​—mbali yake iliyonse​—ndipo nonse pamodzi monga banja yesetsani kuchikulitsa. (Agalatiya 5:22, 23) Kulitsani chikondi pa Yehova ndi Yesu Kristu, osati chabe mwakungonena kuti tiyenera kuwakonda koma kulongosola zifukwa zake tiyenera kuwakonda ndiponso mmene tingasonyezere chikondi chimenecho. (2 Akorinto 5:14, 15) Limbitsani chikhumbo chochita zimene zili zabwino mwa kulingalira za mapindu amene adzakhalapo. Kulitsani chikhumbo chokana maganizo oipa, nkhani zachabe, ndi khalidwe loipa mwa kukambirana kuipa kwa zinthu zimenezo. (Amosi 5:15; 3 Yohane 11) Sonyezani mmene maganizo, zolankhula, ndi khalidwe​—kaya zabwino kapena zoipa​—zingakhudzire unansi wa munthu ndi Yehova.

7. Kodi ndi chiyani chimene tingachite pothandiza ana kulimbana ndi mavuto ndi kusankha zochita m’njira imene idzawapangitsa kukhalabe oyandikana ndi Yehova?

7 Pamene mwana ali ndi vuto kapena akufunika kupanga chosankha chachikulu, tingamufunse kuti: ‘Kodi ukuganiza kuti Yehova amaziona bwanji zimenezi? Kodi ukudziŵa chiyani chokhudza Yehova chimene chikukupangitsa kunena zimenezi? Kodi wapemphera kwa iye za zimenezi?’ Mwa kuyamba mwamsanga monga momwe mungathere, thandizani ana anu kukhala ndi moyo umene nthaŵi zonse umayesetsa moona mtima kuzindikira chifuno cha Mulungu ndiyeno ndi kuchichita. Pamene afika pokhala ndi unansi wathithithi ndi Yehova, iwo adzasangalala kuyenda m’njira zake. (Salmo 119:34, 35) Zimenezi zidzawapangitsa kuyamikira mwayi woyanjana ndi mpingo wa Mulungu woona.

Kukonzekera Misonkhano ya Mpingo

8. (a) Kodi ndi chiyani chimene chingatithandize kuti phunziro lathu labanja liziphatikizapo nkhani iliyonse yofunika kuisamalira? (b) Kodi phunziro limeneli ndi lofunika bwanji?

8 Pali nkhani zambiri zimene timafunika kuzisamalira panthaŵi ya phunziro labanja. Kodi zonsezo mungazikwanitse bwanji panthaŵiyo? Ndi kosatheka kuchita zonse panthaŵi imodzi. Koma mudzaona kuti zimathandiza mukakhala ndi mpambo wa zofunika kuchita. (Miyambo 21:5) Upendeni nthaŵi ndi nthaŵi, ndipo onani zimene zikufunika kuzisamalira mwapadera. Khalani wachidwi ndi mmene aliyense m’banjamo akupitira patsogolo. Makonzedwe ameneŵa a phunziro labanja ali mbali yofunika ya maphunziro achikristu, otikonzekeretsa kukhala ndi moyo tsopano ndiponso moyo wosatha umene ukubwera.​—1 Timoteo 4:8.

9. Kodi ndi zolinga ziti zokhudza kukonzekera misonkhano zimene tingagwirirepo ntchito pang’onopang’ono panthaŵi ya maphunziro athu abanja?

9 Kodi phunziro lanu labanja limaphatikizapo kukonzekera misonkhano ya mpingo? Pali zinthu zambiri zimene mungamagwirirepo ntchito mwapang’onopang’ono pamene mukuphunzira pamodzi. Zina mwa zimenezi zingatenge milungu ingapo, zina miyezi, zina mwina ngakhale zaka kuti muzikwanitse. Lingalirani zolinga izi: (1) aliyense m’banjamo kukhala wokonzeka kukayankha pamisonkhano ya mpingo; (2) aliyense ayenera kuyesetsa kuti aziyankha m’mawu akeake; (3) kuphatikiza malemba m’mayankho; ndi (4) kupenda nkhaniyo ndi cholinga chofuna kuona mmene munthuwe ungaigwiritse ntchito. Zonsezi zingathandize munthu kupanga choonadi kukhala chakechake.​—Salmo 25:4, 5.

10. (a) Kodi tingasamalire motani uliwonse wa misonkhano yathu ya mpingo? (b) Kodi ndi chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

10 Ngakhale ngati nthaŵi zambiri phunziro lanu labanja limakhala pa phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu umenewo, musanyalanyaze kufunika kwakuti munthu aliyense payekha kapena banja lonse pamodzi lizikonzekera Phunziro la Buku la Mpingo, Sukulu ya Utumiki Wateokalase, ndi Msonkhano wa Utumiki. Zimenezinso ndi mbali zofunika za pologalamu yotiphunzitsa kuyenda m’njira ya Yehova. Mwa nthaŵi ndi nthaŵi mungathe kumakonzekera misonkhano pamodzi monga banja. Mwa kuchitira zinthu pamodzi, mudzawongolera maluso anu akuphunzira. Chotsatira chake, mudzapeza mapindu ochuluka pamisonkhano yeniyeniyo. Mwa zinthu zina, kambiranani mapindu a kukonzekera misonkhano imeneyi nthaŵi zonse ndi kufunika koika nthaŵi yeniyeni yochitira zimenezi.​—Aefeso 5:15-17.

11, 12. Kodi kukonzekera kuimba pampingo kudzatipindulitsa motani, ndipo kodi zimenezi tingazichite motani?

11 Pa Misonkhano Yachigawo ya “Njira ya Moyo ya Mulungu,” tinalimbikitsidwa kukonzekera mbali inanso ya misonkhano yathu​—kuimba nyimbo. Kodi mwatsatira zimenezi? Kuchita zimenezi kungathandize kukhomereza choonadi cha Baibulo m’maganizo ndi m’mitima mwathu ndipo panthaŵi yofananayo kungakulitse kusangalala kwathu ndi misonkhano ya mpingo.

12 Kukonzekera kumene kumaphatikizapo kuŵerenga ndi kukambirana matanthauzo a mawu ena amene ali m’nyimbo zondandalikitsidwa kungatithandize kuti tiziimba mochokera pansi pamtima. Mu Israyeli wakale, zida zoimbira zinali kugwiritsidwa ntchito kwambiri polambira. (1 Mbiri 25:1; Salmo 28:7) Kodi alipo wina m’banja lanu amene amagwiritsa ntchito chida choimbira? Bwanji osagwiritsa ntchito chida chimenecho pochita pulakatesi imodzi mwa nyimbo za Ufumu za mlungu umenewo, ndiyeno imbani nyimboyo monga banja. Njira ina ndiyo kugwiritsa ntchito makaseti ojambulidwa a nyimbozo. M’mayiko ena abale athu amaimba bwino kwambiri ndi pakamwa pokha opanda zida zoimbira. Pamene akuyenda panjira kaya akugwira ntchito zawo m’munda, kaŵirikaŵiri amakonda kuimba nyimbo zimene zidzaimbidwa pa misonkhano ya mpingo mlungu umenewo.​—Aefeso 5:19.

Kukonzekera Utumiki Wakumunda kwa Banja

13, 14. Kodi ndi chifukwa chiyani kukambirana kwa banja kumene kumakonzekeretsa mitima yathu kaamba ka utumiki wakumunda kuli kofunika kwambiri?

13 Kuchitira umboni kwa ena za Yehova ndi chifuno chake ndi mbali yofunika ya moyo wathu. (Yesaya 43:10-12; Mateyu 24:14) Kaya ndife ana kapena achikulire, timasangalala kwambiri ndi ntchito imeneyi ndipo timapeza mapindu ochuluka ngati takonzekera. Kodi zimenezi tingazichite motani m’banja?

14 Mofanana ndi nkhani zonse zokhudza kulambira kwathu, ndi kofunika kukonzekeretsa mitima yathu. Tifunika kukambirana osati kokha zimene tikukachita komanso chifukwa chake tikukachita zimenezo. M’masiku a Mfumu Yehosafati, anthu analangizidwa m’chilamulo cha Mulungu, koma Baibulo limatiuza kuti iwo “sadakonzere mitima yawo.” Zimenezi zinawapangitsa kukhala osatetezeka ku zinthu zimene zikanawapatutsa pa kulambira koona. (2 Mbiri 20:33; 21:11) Cholinga chathu sichakuti tizitha chabe kupereka lipoti la maola amene tathera mu utumiki wakumunda, komanso sichakungogaŵira mabuku. Utumiki wathu uyenera kukhala chisonyezero cha chikondi chathu pa Yehova ndiponso pa anthu amene akufuna mwayi wosankha moyo. (Ahebri 13:15) Ndiyo ntchito imene ife tili “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akorinto 3:9) Ndi mwayi waukulu bwanji! Pamene tikuchita utumiki, timatero mogwirizana ndi angelo oyera. (Chivumbulutso 14:6, 7) Ndi nthaŵi inanso yabwino iti imene ingakhalepo yokulitsira kuyamikira zimenezi kuposa pamene banja likukambirana, kaya ndi paphunziro lathu la mlungu ndi mlungu kapena pokambirana lemba logwirizana ndi zimenezi kuchokera mu Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku!

15. Kodi ndi nthaŵi iti imene tingakonzekere utumiki wakumunda monga banja?

15 Kodi inu nthaŵi ndi nthaŵi mumagwiritsa ntchito nthaŵi ya phunziro lanu labanja kuthandiza anthu a m’banja lanu kukonzekera utumiki wakumunda wa mlunguwo? Kuchita zimenezi kungakhale kopindulitsa kwambiri. (2 Timoteo 2:15) Zingathandize kuti utumiki wawo ukhale watanthauzo ndi waphindu. Nthaŵi zina, mungapatule nthaŵi yonse ya phunziro kuti mukonzekere zimenezi. Kaŵirikaŵiri, mungamakambirane mbali zina za utumiki wakumunda kwa kanthaŵi kochepa mukamaliza phunziro labanja kapena nthaŵi ina mkati mwa mlunguwo.

16. Fotokozani phindu la sitepe lililonse lotchulidwa m’ndime ino.

16 Mungakhale ndi masitepe angapo oti muzikonzekera monga banja, masitepe onga aŵa: (1) Kukonzekera ulaliki woyesereredwa bwino kwambiri komanso lemba loti likaŵerengedwe ngati mpata ukalola. (2) Ngati ndi kotheka, onetsetsani kuti aliyense ali ndi chikwama chakechake cha mu utumiki wakumunda, Baibulo, notibuku, cholembera kapena pensulo, mathirakiti, ndi mabuku ena omwe ali mumkhalidwe wabwino. Chikwama cha mu utumiki sichiyenera kuchita kukhala chamtengo wapatali, koma chiyenera kukhala chaudongo. (3) Kambiranani malo amene mungachite umboni wamwamwayi ndi mmene mungauchitire. Mbali iliyonse ya malangizo ameneŵa itsatireni komanso nthaŵi imene mumayendera limodzi mu utumiki wakumunda. Perekani malingaliro othandiza, koma musapereke uphungu pa mfundo zochuluka.

17, 18. (a) Kodi ndi kukonzekera monga banja kotani kumene kungathandize kuti utumiki wathu wakumunda ukhale waphindu kwambiri? (b) Kodi ndi mbali iti ya kukonzekera kumeneku imene ingamachitidwe mlungu uliwonse?

17 Mbali yaikulu ya ntchito imene Yesu Kristu anapatsa otsatira ake ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Kupanga ophunzira kumafuna zambiri kuposa chabe kulalikira. Kumafuna kuphunzitsa. Kodi phunziro lanu labanja lingakuthandizeni motani kukwanitsa kuchita zimenezi?

18 Monga banja, kambiranani anthu amene kungakhale bwino kuwafikiranso paulendo wobwereza. Ena a iwo angakhale atatenga mabuku; ena mwina anangomvetsera. Mungakhale mutakumana nawo pantchito ya kunyumba ndi nyumba kapena pochita umboni wamwamwayi kumsika kapena kusukulu. Lolani kuti Mawu a Mulungu akutsogolereni. (Salmo 25:9; Ezekieli 9:4) Sankhani aliyense wa inu amene akufuna kumuchezera mlungu umenewo. Kodi mukakamba chiyani? Kukambirana kwa banja kungathandize aliyense m’banjamo kukonzekera. Dziŵani malemba enieni amene mudzakambirana ndi anthu ochita chidwi ndiponso mfundo zoyenera za mu bolosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena mu buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Musayese kulongosola zinthu zambirimbiri pa ulendo umodzi. Musiyireni funso mwininyumba limene mudzayankhe paulendo wanu wotsatira. Bwanji osakonza kuti zikhale mbali ya zochita za mlungu uliwonse za banja lanu kulinganiza maulendo obwereza amene aliyense adzapanga, nthaŵi imene adzachita zimenezo, ndi zimene akuyembekeza kukakwaniritsa. Kuchita zimenezi kungathandize kuti utumiki wakumunda wa banja lonselo ukhale wopindulitsa kwambiri.

Pitirizani Kuwaphunzitsa Njira ya Yehova

19. Kuti anthu a m’banja lanu apitirize kuyenda m’njira ya Yehova, kodi iwo afunika kumatani, ndipo kodi ndi chiyani chimene chimapangitsa zimenezi?

19 Kukhala mutu wabanja m’dziko loipali si chinthu chapafupi. Satana ndi ziŵanda zake akuyesetsa kuwononga mkhalidwe wauzimu wa atumiki a Yehova. (1 Petro 5:8) Ndiponso, lerolino makolo mukukumana ndi mavuto ambiri, makamaka inu makolo amene mulibe mnzanu wamuukwati. Ndi kovuta kupeza nthaŵi yochita zinthu zonse zimene mumafuna kuchita. Koma n’koyenera kuyesetsa, ngakhale ngati mutamagwiritsa ntchito lingaliro limodzi lokha panthaŵi imodzi, ndipo pang’onopang’ono kudzawongolera pologalamu yanu ya phunziro labanja. Kuona anthu amene mumakhala nawo pamodzi akuyenda mokhulupirika m’njira ya Yehova, ndi mphotho yosangalatsa kwambiri. Kuti ayende bwinobwino m’njira ya Yehova, anthu a m’banja lanu afunika kumasangalala popezeka pamisonkhano yampingo ndi pochita utumiki wakumunda. Kuti zimenezi zitheke, kukonzekera kumafunika​—kukonzekera kumene kumaumba mtima ndi kukonzekeretsa aliyense kutengamo mbali mwatanthauzo.

20. Kodi ndi chiyani chimene chingathandize makolo ambiri kukhala ndi chimwemwe chonga chotchulidwa pa 3 Yohane 4?

20 Ponena za anthu amene anawathandiza mwauzimu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti ali kuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4) Maphunziro abanja amene amachititsidwa m’maganizo muli zolinga zenizeni ndiponso mitu ya mabanja imene imachita zinthu mwachifundo ndi mothandiza pa zofunika zilizonse za anthu a m’banja lawo angathandize kwambiri kuti banjalo likhale ndi chimwemwe choterocho. Mwa kukulitsa kuyamikira njira ya moyo ya Mulungu, makolo amathandiza banja lawo kusangalala ndi njira ya moyo yabwino kwambiri.​—Salmo 19:7-11.

Kodi Mungalongosole?

◻ Kodi ndi chifukwa chiyani kukonzekera misonkhano kuli kofunika kwambiri kwa ana athu?

◻ Kodi makolo angawathandize motani ana awo ‘kulandira nzeru’?

◻ Kodi phunziro lathu labanja lingathandize motani kukonzekera misonkhano yonse?

◻ Kodi kukonzekera utumiki wakumunda monga banja kungatithandize motani kukhala ogwira mtima kwambiri?

[Chithunzi patsamba 20]

Phunziro lanu labanja lingaphatikizepo kukonzekera misonkhano ya mpingo

[Chithunzi patsamba 21]

Ndi kopindulitsa kuchita pulakatesi kukaimba pamisonkhano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena