Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/11 tsamba 3-6
  • Mphatso Yothandiza kwa Mabanja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphatso Yothandiza kwa Mabanja
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kulambira kwa Pabanja Kuzikhala Kosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Mabanja Achikhristu Ayenera ‘Kukhala Okonzeka’
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Mabanja, Tamandani Mulungu Monga Mbali ya Mpingo Wake
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 1/11 tsamba 3-6

Mphatso Yothandiza kwa Mabanja

1. Kodi kusunga Sabata mlungu uliwonse kunkathandiza bwanji mabanja a Aisiraeli?

1 Kusunga Sabata inali mphatso yachikondi yochokera kwa Yehova yomwe inkapindulitsa mabanja. Pa tsikuli Aisiraeli ankapuma ntchito zawo za tsiku ndi tsiku ndipo ankakhala ndi nthawi yoganizira za ubwenzi wawo ndi Yehova komanso kuganizira zabwino zimene ankawachitira. Makolo ankakhalanso ndi mwayi wokhomereza Chilamulo m’mitima mwa ana awo. (Deut. 6:6, 7) Sabata linkapatsa mpata anthu a Yehova mlungu uliwonse woti aziganizira kwambiri zinthu zokhudza kulambira.

2. Kodi Sabata limatiphunzitsa chiyani za Yehova?

2 Masiku ano Yehova safuna kuti mabanja azisunga Sabata. Komabe, lamulo limeneli limatiphunzitsa kuti Mulungu wathu amafunitsitsa kuti anthu ake azipindula chifukwa chokhala naye pa ubwenzi wabwino. (Yes. 48:17, 18) Njira imodzi imene Yehova amasonyezera chikondi chake masiku ano ndi mwa kutipatsa mwayi wokhala ndi tsiku lochita Kulambira kwa Pabanja.

3. Kodi cholinga cha Kulambira kwa Pabanja ndi chiyani?

3 Kodi Cholinga cha Kulambira kwa Pabanja N’chiyani? Kuyambira mu January 2009, Phunziro la Baibulo la Mpingo linayamba kuchitika limodzi ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu komanso Msonkhano wa Utumiki. Chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kusintha kumeneku n’chakuti mabanja azikhala ndi nthawi yapadera mlungu uliwonse yochita Kulambira kwa Pabanja kuti azilimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova monga banja. Banja lililonse linalimbikitsidwa kuti ngati n’zotheka liziphunzira Baibulo nthawi imene poyamba ankachita phunziro la buku. Iwo anafunika kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi kuti azikambirana nkhani za m’Baibulo mofatsa ndiponso kuti aziphunzira nkhani zogwirizana ndi zosowa za banjalo.

4. Kodi tizichita Kulambira kwa Pabanja kwa ola limodzi lokha? Fotokozani.

4 Kuti tikapezeke pa Phunziro la Buku la Mpingo tinkafunika nthawi yokwanira yoti tiyende komanso tikonzekere bwino. Kwa ambirife, tinkafunika nthawi yochuluka kuposa ola limodzi kuti tikapezeke pa phunziro limeneli. Koma chifukwa cha kusintha kwa nthawi ya misonkhanoyi, tsopano timagwiritsa ntchito nthawi imeneyi kulambira Yehova monga banja. Choncho, Kulambira kwa Pabanja kwathu kusamachite kukhala ola limodzi ndendende. Tiyenera kuganizira zosowa komanso zimene banja lathu lingakwanitse kuchita kenako n’kusankha kuti Kulambira kwa Pabanja kwathu kuzitenga nthawi yaitali bwanji, kuti tikwaniritse cholinga cha Kulambira kwa Pabanja.

5. Kodi nthawi yonse ya Kulambira kwa Pabanja izingothera pokambirana monga banja? Fotokozani.

5 Kodi Nthawi Yonse ya Kulambira kwa Pabanja Izingothera Pokambirana Monga Banja? Anthu okwatirana komanso mabanja amene ali ndi ana amalimbikitsana akamakambirana nkhani za m’Malemba. (Aroma 1:12) Onse m’banjamo amayamba kukondana. Choncho, kukambirana mfundo za m’malemba ndi kofunika kwambiri pa Kulambira kwa Pabanja. Komabe, aliyense m’banjamo akhoza kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi pophunzira Baibulo payekha. Mwachitsanzo, pambuyo poti amaliza kukambirana monga banja, onse akhoza kukhalabe pamodzi koma aliyense akupitiriza kuphunzira payekha, mwina angamapitirize kukonzekera misonkhano kapena kuwerenga magazini. Mabanja ena amasankha kusayatsa TV chigawo chonse cha tsiku chimene amachita Kulambira kwa Pabanja.

6. Kodi zokambiranazo zizichitika motani?

6 Kodi Zokambiranazo Zizichitika Motani? Sikuti nthawi zonse kukambiranako kuzikhala kwa mafunso ndi mayankho. Mabanja ambiri amakhala ndi ndondomeko yofanana ndi imene timakhala nayo kumisonkhano kuti Kulambira kwa Pabanja kwawo kuzikhala kosangalatsa komanso kochititsa chidwi. Amagawa zokambiranazo m’mbali zosiyanasiyana komanso amaziphunzira m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, angawerenge Baibulo pamodzi, kukonzekera misonkhano ina ndi kuyerekeza zimene angakachite mu utumiki. Tsamba 6 lili ndi zina zimene mungachite.

7. Kodi makolo ayenera kuyesetsa kuti zokambiranazo zizikhala zotani?

7 Kodi Makolo Ayenera Kukhala ndi Cholinga Choti Mzimu wa Zokambiranazo Uzikhala Wotani? Banja lanu likhoza kumaphunzira bwino ngati phunzirolo likuchitika mwachikondi komanso m’njira yokhala ngati mukucheza. Nthawi zina mukhoza kuchitira phunziro lanu panja ngati nyengo ili bwino. Mukhoza kumakhala ndi kanthawi kopuma kaye pang’ono ngati pakufunikira kutero. Mabanja ena amakonza zokhala ndi zosangalatsa zina akamaliza phunzirolo. Makolo ayenera kupewa kugwiritsa ntchito mpata umenewu kudzudzula kapena kupereka chilango kwa ana. Komabe, ngati adziwa zoti pabanjapo pali chizolowezi kapena vuto linalake, akhoza kugwiritsa ntchito nthawi ina ya phunzirolo kuti akambirane njira yothetsera vutolo. Ngakhale zili choncho, ngati pali nkhani ina yachinsinsi yokhudza mwana wina, ndi bwino kukambirana naye payekha nthawi ina mkati mwa mlunguwo kuti musamuchititse manyazi pamaso pa abale ake. Kulambira kwa Pabanja sikuyenera kukhala kosasangalatsa kapena kotopetsa, koma kuyenera kusonyeza kuti Mulungu amene timamulambira ndi wachimwemwe.—1 Tim. 1:11.

8, 9. Kodi mitu ya mabanja iyenera kukonzekera motani?

8 Kodi Mwamuna, Yemwe Ndi Mutu wa Banja, Angakonzekere Motani? Banja lingamapindule kwambiri ngati mutu wa banjalo amakonzekereratu tsiku la Kulambira kwa Pabanja lisanafike. Mlungu uliwonse iye ayenera kukonzekera zimene angakambirane ndi banja lake komanso njira yabwino imene angatsatire pokambirana mfundozo. (Miy. 21:5) Mwamuna ayenera kukambirana ndi mkazi wake posankha nkhani zimenezi. (Miy. 15:22) Inu amene ndi mitu ya mabanja mungachitenso bwino nthawi zina kufunsa ana anu kuti mumve zimene akuona kuti n’zofunika kukambirana. Kuwapatsa mpata umenewu kungakuthandizeni kuzindikira zimene amakonda komanso zomwe zimawadetsa nkhawa.

9 Nthawi zambiri mwamuna sangachite kufunikira kuthera nthawi yambiri akukonzekera phunziroli. N’kutheka kuti banja lingamasangalale kumachita zinthu zina zake mlungu uliwonse, ndipo mutu wa banja sungafunikire kuti mlungu uliwonse uzisintha pulogalamu yonseyo kuti isiyane ndi ya mlungu watha. Zingamakhale zophweka kukonzekera akangomaliza pulogalamu iliyonse chifukwa pa nthawiyi amakhala asanaiwale zosowa zauzimu za banja lake. Mitu ina ya mabanja imalemba mndandanda wa mfundo zodzakambirana mlungu wotsatira n’kuzimata pamalo oti aliyense m’banjamo atha kuziona, monga pachitseko kapena mmunsi mwa kalendala. Zimenezi zimapangitsa banjalo kukhala ndi chidwi komanso kulithandiza kukhala ndi mpata wokwanira wokonzekera ngati pakufunikira kutero.

10. Kodi amene amakhala okha angagwiritse ntchito bwanji nthawi ya Kulambira kwa Pabanja?

10 Bwanji Ngati Ndimakhala Ndekha Kapena Amene Ndimakhala Nawo si Mboni? Anthu amene amakhala okha angagwiritse ntchito nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kuti aziphunzira Baibulo paokha. Kuphunzira kwabwino kuyenera kuphatikizapo kuwerenga Baibulo, kukonzekera misonkhano, ndiponso kuwerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ofalitsa ena amawonjezeraponso kufufuza nkhani zina ndi zina paokha. Nthawi zina angafune kuitana wofalitsa wina kapena banja lina kuti likhale nawo pokambirana mfundo za m’Malemba.

11, 12. Kodi ubwino wochita Kulambira kwa Pabanja kokhazikika ndi wotani?

11 Kodi Ubwino Wochita Kulambira kwa Banja Nthawi Zonse Ndi Wotani? Anthu amene amachita kulambira koona ndi mtima wonse amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Nawonso mabanja amene amalambirira limodzi amakhala ogwirizana kwambiri. Pofotokoza madalitso amene apeza, banja lina linalemba kuti: “Timachita upainiya monga banja ndipo tilibe ana, choncho timayembekezera mwachidwi tsiku limene timachita Kulambira kwa Pabanja. Nthawi imeneyi yalimbitsa ubwenzi wathu monga banja komanso ndi Atate wathu wakumwamba. Masiku ano tikangodzuka m’mawa wa tsiku limene timachita kulambira kwa pabanja, timauzana kuti ‘Paja lero timachita Kulambira kwa Pabanja.’”

12 Dongosolo lokhala ndi tsiku lochita Kulambira kwa Pabanja limathandizanso mabanja amene amakhala otanganidwa. Mayi wina amene amalera ana aamuna awiri yekha komanso amachita upainiya wokhazikika analemba kuti: “M’mbuyomu, phunziro lathu la banja silinkayenda bwino. Linali losakhazikika chifukwa ndinkakhala wotopa. Ndinkalephera kupeza njira yabwino yochitira phunziroli. Choncho ndalemba kalatayi ndi cholinga chokuthokozani chifukwa chokhazikitsa dongosolo la Kulambira kwa Pabanja. Takwanitsa kukhala ndi phunziro la banja lokhazikika ndipo tapindula kwambiri ndi zimenezi.”

13. Kodi banja lingatani kuti lizipindula kwambiri ndi Kulambira kwa Pabanja?

13 Mofanana ndi Sabata, Kulambira kwa Pabanja ndi mphatso yochokera kwa Atate wathu wakumwamba yothandiza mabanja. (Yak. 1:17) Mabanja achiisiraeli amene ankasunga Sabata mokhulupirika ndi amene ankapindula mwauzimu. Nafenso mabanja athu angapindule kwambiri ngati timagwiritsa bwino ntchito mwayi wochita Kulambira kwa Pabanja. (2 Akor. 9:6; Agal. 6:7, 8; Akol. 3:23, 24) Tikamagwiritsa bwino ntchito mwayi umenewu, banja lathu lidzanena mawu amene wamasalimo ananena akuti: “Koma kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.”—Sal. 73:28.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kulambira kwa Pabanja sikuyenera kukhala kosasangalatsa kapena kotopetsa, koma kuyenera kusonyeza kuti Mulungu amene timamulambira ndi wachimwemwe

[Bokosi patsamba 6]

SUNGANI

Njira Zina Zochitira Kulambira kwa Pabanja

Baibulo:

• Werengani limodzi chigawo cha kuwerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu. Ngati nkhaniyo yalembedwa mosonyeza kuti anthuwo akukambirana, mungagawane mbali kuti mmodzi aziwerenga mbali ya wofotokoza, ndipo ena aziwerenga mawu a anthu osiyanasiyana amene ali munkhaniyo

• Chitani sewero la zimene mwawerenga m’Baibulo

• Gawirani aliyense mbali yoti awerenge m’Baibulo tsiku la Kulambira kwa Pabanja lisanafike ndipo alembe funso limodzi kapena awiri pa zimene wawerengazo. Kenako mungadzafufuze mayankho a funso limene aliyense anapeza

• Mlungu uliwonse lembani vesi la m’Baibulo pakakhadi ndipo yesani kuloweza ndi kufotokoza zimene lembalo likunena. Lembani makhadi ambiri ndipo muziwaonanso mlungu uliwonse kuti mudziwe malemba amene mukutha kuwakumbukira

• Mvetserani tepi kapena CD ya Baibulo ndipo muzitsatira m’Baibulo lanu

Misonkhano:

• Konzekerani limodzi chigawo cha misonkhano ya mlungu umenewo

• Konzekerani nyimbo za Ufumu zimene mukaimbe kumisonkhano mlungu wotsatira

• Ngati wina ali ndi nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kapena chitsanzo mu Msonkhano wa Utumiki, kambiranani mmene angakakambire kapena muuzeni kuti ayesezere pamaso pa banja lonse

Zosowa za Banjalo:

• Kambiranani mfundo za m’buku la Zimene Achinyamata Amafunsa kapena Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

• Yesezerani mmene ana angayankhire nkhani inayake imene ikhoza kuchitika kusukulu kwawo

• Auzeni ana kuti akhale ngati makolo ndipo inuyo mukhale ngati ana. Anawo afufuze nkhani inayake kenako akambirane nanu

Utumiki:

• Yesezerani zimene mukanene mu utumiki Loweruka ndi Lamlungu

• Kambiranani zolinga zimene banjalo likhoza kukhala nazo n’cholinga choti lidzachite nawo utumiki mokwanira nthawi ya Chikumbutso kapena ya tchuti

• M’patseni aliyense mwayi woti afufuze kwa mphindi zingapo mmene angayankhire funso linalake limene anthu angafunse mu utumiki, kenako yesezerani

Zinthu Zina Zimene Mungachite:

• Werengerani limodzi nkhani ya m’magazini atsopano

• Aliyense awerengeretu nkhani imene yamuchititsa chidwi m’magazini atsopano ndipo kenako adzafotokozere banja lonse pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja

• Nthawi zina mungaitane wofalitsa kapena banja lina kuti mudzachitire limodzi Kulambira kwa Pabanja ndiponso mwina mungadzakhale ndi mwayi wowafunsa zina ndi zina

• Onerani ndi kukambirana vidiyo ya Sosaite

• Kambiranani limodzi nkhani ya “Zimene Achinyamata Amafunsa” kapena “Zoti Banja Likambirane” kuchokera m’magazini ya Galamukani!

• Kambiranani limodzi “Phunzitsani Ana Anu” kapena “Zoti Achinyamata Achite” kuchokera m’magazini ya Nsanja ya Olonda

• Werengani ndi kukambirana nkhani zina za mu Yearbook yatsopano kapena mabuku amene angotuluka kumene pa msonkhano wachigawo

• Mukabwera kumsonkhano wachigawo, wadera kapena wapadera, kambiranani mfundo zikuluzikulu zimene mwaphunzira

• Onani zinthu zam’chilengedwe zimene Yehova analenga ndipo kambiranani zimene mukuphunzirapo ponena za Yehova

• Fufuzani ndi kukambirana zinthu monga zitsanzo zabwino za anthu a m’Baibulo, mapu kapena matchati

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena