Filipo—Mlaliki Wokangalika
MALEMBA ali ndi nkhani zambiri za amuna ndi akazi amene chikhulupiriro chawo n’chofunika kuchitsanzira. Mwachitsanzo, Filipo mmishonale wachikristu wa m’zaka za zana loyamba. Iye sanali mtumwi, komabe anagwiritsidwa ntchito mwamphamvu kufalitsa uthenga wa Ufumu. Inde, Filipo anadziŵika kukhala “mlaliki.” (Machitidwe 21:8) N’chifukwa chiyani Filipo anadziŵika ndi dzina limeneli? Ndipo tingaphunzirenji kuchokera kwa iye?
Filipo amapezeka m’nkhani za m’Baibulo kuyambira itangotha Pentekoste wa 33 C.E. Panthaŵiyo, Ayuda olankhula Chigiriki anayamba kudandaula za Ayuda olankhula Chihebri, akumanena kuti akazi amasiye awo anali kulambalalidwa pogaŵa chakudya cha tsiku ndi tsiku. Kuti athetse vutoli, atumwi anasankha ‘amuna oyang’anira asanu ndi aŵiri.’ Filipo anali mmodzi mwa amene anasankhidwa.—Machitidwe 6:1-6.
Amuna asanu ndi aŵiri ameneŵa anali “oyang’anira.” Baibulo la James Moffatt limati, iwo anali ndi “mbiri yabwino.” Inde, panthaŵi imene amasankhidwa, anali atadziŵika kale kukhala amuna auzimu okhala ndi luso la maganizo othandiza. Ndi mmene ziliri ndi aja otumikira monga oyang’anira achikristu lerolino. Amuna ameneŵa samasankhidwa mofulumira ayi. (1 Timoteo 5:22) Ayeneranso ‘kuti akunja awachitire umboni wabwino,’ komanso Akristu anzawo ayenera kuwadziŵa kukhala ofatsa ndi odziletsa.—1 Timoteo 3:2, 3, 7; Afilipi 4:5.
Mwachionekere, Filipo anagwira bwino ntchito yake ku Yerusalemu. Komabe, pasanapite nthaŵi, chizunzo chinayamba ndipo otsatira Kristu anabalalika. Monganso ena, Filipo anathaŵa mum’zindawo, komabe sanasiye kutumikira. Posakhalitsa, anali kalikiliki kulalikira m’gawo latsopano—Samariya.—Machitidwe 8:1-5.
Kutsegula Magawo Atsopano
Yesu analosera kuti ophunzira ake adzalalikira “m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Mwa kulalikira ku Samariya, Filipo anakwaniritsa nawo ulosi umenewu. Ayuda kwenikweni anali kuona Asamariya monga anthu opanda pake. Koma Filipo sanaweruziretu anthu ameneŵa, ndipo kupanda tsankho kwake kunadalitsidwa. Inde, Asamariya ambiri anabatizidwa, kuphatikizapo Simoni amene ankachita matsenga.—Machitidwe 8:6-13.
Nthaŵi ina, mngelo wa Yehova anauza Filipo kuti ayende m’njira yodutsa m’chipululu yochokera ku Yerusalemu kumka ku Gaza. Kumeneko Filipo anaona galeta m’takwera mdindo wa ku Aitiopiya amene anali kuŵerenga mokweza ulosi wa Yesaya. Filipo anayandikira galetalo ndi kuyamba kukambirana. Ngakhale kuti Mwaitiopiyayo anali wotembenukira kuchiyuda amene anali ndi chidziŵitso cha Mulungu ndi Malemba, iye modzichepetsa anavomereza kuti afunika chithandizo kuti amvetse zomwe anali kuŵerenga. Choncho, anaitana Filipo kukwera pa galetalo ndi kukhala naye. Umboni utaperekedwa, iwo anafika padziŵe la madzi. Mwaitiopiyayo anafunsa kuti: “Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” Filipo nthaŵi yomweyo anam’batiza iye, ndipo Mwaitiopiyayo ananyamuka kupitiriza ulendo wake mosangalala. Mosakayika, wophunzira watsopano ameneyu anakafalitsa uthenga wabwino kudziko lakwawo.—Machitidwe 8:26-39.
Kodi tingaphunzirenji kuchokera muutumiki wa Filipo kwa Asamariya ndi mdindo wa ku Aitiopiya? Sitiyenera kuganiza kuti anthu a kumayiko ena, mtundu, kapena chikhalidwe sangakhale ndi chidwi ndi uthenga wabwino. M’malo mwake, tiyenera kulalikira uthenga wa Ufumu kwa “anthu onse.” (1 Akorinto 9:19-23) Ngati ife eni tidzipereka kulalikira kwa onse, Yehova adzatigwiritsa ntchito ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse’ chiwonongeko cha dongosolo loipa lilipoli chisanafike.—Mateyu 28:19, 20.
Mwayi Woŵirikiza wa Filipo
Atalalikira kwa mdindo wa ku Aitiopiya, Filipo anachita umboni ku Azotu, “ndipo popitapita nalalikira Uthenga Wabwino m’midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kaisareya.” (Machitidwe 8:40) M’zaka za zana loyamba, mizinda iŵiri imeneyi ndiyo inali ndi anthu akunja ambiri. Paulendo wake wakumpoto ku Kaisareya, Filipo mosakayika analalikira kumalikulu achiyuda, monga ku Luda ndi Yopa. Mwina ndicho chifukwa chake ophunzira ena ankapezeka ku malo ameneŵa.—Machitidwe 9:32-43.
Filipo anadzatchulidwa komalizira patapita zaka pafupifupi 20. Kumapeto kwa ulendo wake wachitatu waumishonale, Paulo anaima ku Ptolemayi. “Ndipo m’maŵa mwake,” anatero Luka mnzake wapaulendo wa Paulo, ‘tinachoka, tinafika ku Kaisareya, ndipo tinaloŵa m’nyumba ya Filipo mlaliki.’ Panthaŵiyo, Filipo anali ndi “ana akazi anayi, anamwali, amene ananenera.”—Machitidwe 21:8, 9.
Panthaŵi imeneyo, n’kuti Filipo atakhazikika ku Kaisareya. Komabe sanachotse mtima wake pa umishonale, n’chifukwa chake Luka anamutcha “mlaliki.” Mawu ameneŵa kaŵirikaŵiri amatanthauza munthu amene amasiya nyumba yake ndi kupita kukalalikira uthenga wabwino ku magawo atsopano. Pokhala kuti Filipo anali ndi ana aakazi anayi amene amanenera, zimenezi zikutisonyeza kuti anawo ankatsatira kukangalika kwa bambo awo.
Masiku ano makolo achikristu ayenera kukumbukira kuti ana ndiwo ophunzira awo ofunika kwambiri. Ngakhale kuti makolo otere angasiye maudindo ena ateokalase chifukwa cha udindo wabanja, monga Filipo, iwo angatumikirebe Mulungu ndi mtima wonse ndi kupereka chitsanzo chabwino.—Aefeso 6:4.
Kucheza kwa Paulo ndi anzake kunapatsa banja la Filipo mwayi wabwino kuti asonyeze kuchereza alendo. Kunalidi nkhani zolimbikitsa! Mwinamwake inali nthaŵi imeneyi pamene Luka anadziŵa tsatanetsatane wa zimene Filipo ankachita, zimene anazilemba m’machaputala 6 ndi 8 a Machitidwe.
Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito Filipo kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Kukangalika kwa Filipo kunam’thandiza kufalitsa uthenga wabwino ku magawo atsopano ndiponso kulimbikitsa moyo wauzimu pa banja lake. Kodi mungakonde kusangalala ndi mwayi ndi madalitso ofananawo? Ngati mungakonde, tsanzirani mikhalidwe imene Filipo, mlalikiyo, anaonetsa.