Onetsani Mzimu wa Upainiya
1. Kodi mungaufotokoze motani mzimu wa upainiya?
1 Kaya panopa angathe kutumikira monga apainiya kapena ayi, ofalitsa Ufumu onse angathe kuonetsa mzimu wa upainiya. Iwo amafunitsitsa kumvera lamulo lakuti alalikire ndi kupanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20; Mac. 18:5) Amaganizira anthu ena, n’chifukwa chake amadzimana zina n’zina kuti akwaniritse utumiki wawo. (Mat. 9:36; Mac. 20:24) Atumiki a Yehova ndi ofunitsitsa kuchita zonse zimene angathe kuti athandize ena kuphunzira choonadi. (1 Akor. 9:19-23) Tiyeni tione chitsanzo cha mlaliki Filipo amene anaonetsa mzimu umenewu.
2. Kodi akulu ndi atumiki otumikira angatsanzire motani changu chimene Filipo anali nacho mu utumiki?
2 Kulalikira ndi Kuphunzitsa: Filipo anali ndi maudindo akuluakulu mu mpingo wa m’zaka 100 zoyambirira. (Mac. 6:1-6) Komanso anali mlaliki wachangu wa uthenga wabwino. (Mac. 8:40) Chimodzimodzinso masiku ano. Akulu ndi atumiki otumikira akhoza kuonetsa mzimu wa upainiya umenewu potsogolera mwachangu mu utumiki, kwinaku akusamalira maudindo awo ena mu mpingo. Mzimu umenewu umalimbikitsa mpingo kwambiri!—Aroma 12:11.
3. Kodi tingaonetse motani mzimu wa upainiya pamene takumana ndi ziyeso?
3 Stefano atamwalira, panali chizunzo chachikulu ndipo chinasokoneza kwambiri moyo wa ophunzira. Koma Filipo anapitirizabe kulalikira, ndipo anathandiza kwambiri kuti ntchito yolalikira iyambike pakati pa Asamariya. (Mac. 8:1, 4-6, 12, 14-17) Tingathe kutsanzira chitsanzo chimenechi mwa kupitirizabe kulalikira uthenga wabwino ngakhale pamene takumana ndi ziyeso ndiponso mwa kulalikira kwa onse amene timakumana nawo mopanda tsankho.—Yoh. 4:9.
4. Kodi Filipo anapereka chitsanzo chotani monga mphunzitsi?
4 Filipo anali ndi luso lophunzitsa Mawu a Mulungu, ndipo nkhani ya kutembenuka kwa mdindo wa ku Aitiopiya imasonyeza zimenezi. ( Mac. 8:26-38). Njira inanso imene tingaonetsere mzimu wa upainiya ndiyo kukulitsa luso lathu logwiritsa ntchito Baibulo ndi ‘kutanthauzira malembo.’ (Mac. 17:2, 3) Monga Filipo, timayesetsa kulalikira uthenga wabwino kulikonse kumene tingapezeko anthu ndiponso tikapeza mpata wabwino uliwonse.
5. Kodi n’chiyani chimene chingathandize makolo achikristu kulimbikitsa ana awo kukhala ndi mzimu wa upainiya?
5 Banja Ndiponso Mpingo: Zimene Filipo anali kuchita, mosakayikira zinawalimbikitsa kwambiri ana ake aakazi. (Mac. 21:9) Mofananamo, makolo amene amaika moyo wawo pa zinthu za Ufumu amalimbikitsa ana awo kuchitanso zomwezo. Pofika kumapeto kwa mlungu makolo amakhala atatopa. Komabe kholo limene limalalikira kwa ena mosangalala limaonetsa chitsanzo chabwino chosaiŵalika kwa mwana.—Miy. 22:6.
6. Kodi apainiya a mu mpingo mwathu tingawasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene akuchita?
6 Filipo analandiranso Paulo ndi Luka kunyumba kwake. Ameneŵa anali Akristu achangu amene anali kutumikira Yehova mwakhama. (Mac. 21:8, 10) Kodi ifeyo tingachite chiyani kuti tithandize atumiki achangu masiku ano ndi kuwasonyeza kuti timayamikira zimene akuchita? Tingathe kupita mu utumiki limodzi ndi apainiya kaya nthaŵi ya kum’maŵa kapena kumasana masiku amene anthu ambiri sapita mu utumiki. (Afil. 2:4) Tingathenso kuwaitana kunyumba kwathu kuti tidzacheze nawo. Choncho, mulimonse mmene tingathere, tiyeni tonse tiyesetse kuonetsa mzimu wa upainiya.