Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/02 tsamba 1
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo a Banja Atanthauzo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo a Banja Atanthauzo
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Phunziro la Banja Losangalatsa
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kukwaniritsa Udindo wa Kusamalira Banja
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 2/02 tsamba 1

Kuchititsa Maphunziro a Baibulo a Banja Atanthauzo

1 Kuphunzitsa ana awo choonadi ndi ntchito ina yofunika kwambiri imene makolo amagwira. Ndi udindo umene Yehova anawapatsa. (Deut. 6:6, 7) Kuti ana ayende moongoka m’dziko loipali, amafunika kuwalangiza ndi kuwatsogolera. Amafunika kuphunzira kukonda Yehova ndi choonadi ndiponso kutsimikiza mtima kuyendera nacho limodzi. Nsanja ya Olonda ya August 1, 1988, patsamba 11, inati: ‘Mosasamala kanthu za udindo uliwonse umene muli nawo kapena mavuto amene mumakumana nawo, kucheza ndi ana anu n’kofunika kukhala patsogolo pa zonse. Nthaŵi imene mumacheza ndi ana anu idzakuthandizani kukhomereza zinthu zauzimu zimene zidzatchinjiriza mitima ya ana anu ndi kuwaika panjira yabwino.’

2 Kuti mabanja atsatire malangizo a m’Mawu a Mulungu, ayenera kukhala ndi nthaŵi ya phunziro la banja nthaŵi zonse. Mitu yabanja ifunika kusamalira choyamba moyo wauzimu wa mabanja awo. Ngati makolo alephera kusamalira bwino zosoŵa zauzimu za banja lawo pakalipano, ndithudi adzapeza mavuto aakulu m’tsogolo.

3 Zinthu Zophunzira Ndiponso Njira Zophunzirira: Kodi aziphunzira chiyani? Mutu wa banja ndi umene ungadziŵe bwino kwambiri zosoŵa za pabanja. Angafunse ena m’banjamo zimene akuganiza kuti n’zopindulitsa ndipo agwiritse ntchito malingalirowo. Kulolera kudzapangitsa phunziro labanja kukhala lothandiza ndi lolimbikitsa. Mabanja ambiri amasankha kukonzekera Nsanja ya Olonda paphunziro lawo la mlungu ndi mlungu. Komabe, nthaŵi zina ndi bwino kukambirana nkhani zapadera zokhudza mavuto amene ana amakumana nawo kusukulu. Mungakambirane molimbikitsa nkhani zimene zafalitsidwa zokhudza zibwenzi, zochitika zina za kusukulu, za maseŵero, ndi zizoloŵezi zoipa. N’kofunika kuti mutu wabanja uzipendanso nthaŵi zonse nkhani zimene banja likufunikira ndiponso momwe angawafikire pa mtima ndi zimenezo.—Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1971, masamba 364-5.

4 Kodi phunziro lizichitika motani? Apangitseni onse kukhala omasuka koma nonse mukuchita zinthu mwaulemu. Peŵani kungolankhula zimene zalembedwazo kapena kupangitsa anthu ena kukhala omangika pa phunzirolo. Funsani mafunso owonjezereka, ndipo gwiritsani ntchito mafanizo kuti alimbikitse ena kuganiza ndiponso kuti onse aloŵetsedwe m’makambiranowo. Mungagwiritse ntchito zinthu monga mapu ndi matchati kuti mukometsere nkhaniyo. Ana aang’ono akangoyamba kulankhula azitenga nawo mbali m’makambiranowo. Mungawafunse mafunso ophweka osalira mayankho aatali. Musagwiritsire ntchito nthaŵi ya phunziro kukhala yodzudzulira ana. Mmalo mwake, athokozeni ndi kuyamikira kuyesetsa kwawo, ndipo limbikirani kuwauza zinthu zauzimu.

5 Kodi mungatsimikizire motani kuti mukuwafika pamtima ana anu? Limbikitsani onse kuyankha m’mawu awo. Gwiritsirani ntchito mwanzeru mafunso ofuna mayankho awoawo kuti mudziŵe zimene zili m’mitima yawo. Mungafunse kuti: “Kodi ana asukulu amalingalira zotani pa nkhani imeneyi? Kodi mumakayikira mfundo imeneyi?” Samalani, musapse mtima ndi zimene ana anena poyankha mafunso onena malingaliro awo. Ngati mupsa mtima, ana anu aziopa kutulutsa zakukhosi momasuka. Apatseni mpata wolankhula. Kudziŵa kuti mumawakonda ndi kudera nkhaŵa mavuto awo kudzathandiza ntchito yanu yophunzitsa kukhala yophweka kwambiri.—Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1986, masamba 23-5.

6 Kumbukirani kuti cholinga chachikulu cha phunziro lanu labanja ndicho kukhomereza mwa ana maganizo a Yehova osati kuloŵeza zokayankha pamsonkhano wampingo. (Aef. 3:17-19) Izi zikutanthauza kuti aziyesetsa kumvetsetsa zimene akuphunzira. Uzani banjalo zifukwa zake afunika kuchita zimene Mulungu amafuna ndiponso chifukwa chake zimenezi zili njira yabwino kwambiri kuposa ina iliyonse imene angatsatire pamoyo wawo.

7 Phunziro la Baibulo lokhazikika la banja n’lofunika pokulitsa moyo wauzimu wabanja. Limaphunzitsa ndi kuthandiza ana kuthana ndi zovuta m’moyo. Makolo, ndinu amene mungathandize bwino ana anu. Chitani ntchitoyi imene Mulungu anakupatsani. Ndithudi Yehova adzakudalitsani ngati muyesetsa nthaŵi zonse kuchititsa phunziro la Baibulo labanja latanthauzo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena