Misonkhano Yatanthauzo Yokonzekera Utumiki Wakumunda
1 Pa Luka 10:1-11, tili ndi cholembedwa cha msonkhano umene Yesu anachita ndi ophunzira 70 ogaŵiridwa chatsopano kuwathandiza kukonzekera kaamba ka utumiki wakumunda. Iye anapereka malangizo achindunji kuwathandiza kukhala olinganizika, kukonzekera zimene akanena, ndi kuchita ndi mikhalidwe yovuta. Tingaphunzire mwa kusanthula nkhani imeneyi.
2 Mwachionekere ophunzira onse 70 analipo pa msonkhano umenewo ndi Yesu. Nthaŵi yochuluka imawonongedwa pa misonkhano yokonzekera utumiki ngati anthu ena abwera mochedwa mwa chizoloŵezi. Kufika kwawo mochedwa kaŵirikaŵiri kumachititsa kulinganizanso magulu limodzi ndi magawo ogaŵiridwa. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimachititsa gulu lonse kuchedwa. Tonsefe tingachite mbali yathu mwa kufika panthaŵi yake ndi kukhala okonzekera kupita ku gawo mofulumira.
3 Yesu anapatsa gululo nkhani yokambitsirana yakutiyakuti yoigwiritsira ntchito, yotchedwa, “Ufumu wa Mulungu.” (Luka 10:9) Tagaŵiridwa kulalikira uthenga umodzimodziwo, ndipo nthaŵi zambiri timayamikira malingaliro ena othandiza onena za zimene tinganene. Wochititsa angasonye ku buku la Kukambitsirana, limene limapereka mawu oyamba osiyanasiyana oposa 40 ndi ndime za Malemba oyenerera amene angagwiritsiridwe ntchito pa mikhalidwe yambiri yosiyanasiyana. Kapendedwe kachidule ka ulaliki umodzi kapena aŵiri kangatithandize kukhala ndi chinachake m’maganizo choti tinene, kutitheketsa kulankhula ndi chidaliro chachikulu pa makomo.
4 Yesu sanangouza ophunzira ake zimene akanena koma anawauza mmene akazinenera. (Luka 10:5, 6) Zitsanzo zoperekedwa pa programu ya Msonkhano Wautumiki zimatisonyeza mmene tingalankhulire mogwira mtima. Wochititsa angapende zimene zinanenedwa pa msonkhano womalizira ndi kupereka malingaliro a mmene zingagwiritsidwire ntchito mu utumiki tsikulo. Chitsanzo chachidule chokonzekeredwa cha ulaliki wa Malemba chingatithandize kusonkhanitsa malingaliro athu ndi kuwalankhula.
5 Yesu analangizanso ophunzira ake ponena za khalidwe lawo laumwini. (Luka 10:7, 8) Mofananamo wochititsa angatipatse chitsogozo chachindunji kutithandiza kupeŵa chilichonse chimene chingacheutse ntchito yathu. Iye angatichenjeze ponena za kuunjikana m’mphambano za makwalala kapena kutaya nthaŵi kutsutsana ndi otsutsa. Iye angatikumbutse kufunika kwa kusunga zolembedwa zolongosoka za kunyumba ndi nyumba. Makolo angafunikire chikumbutso ponena za kuyang’anira mosamalitsa ana awo.
6 Ophunzira 70 amenewo anagwirizana ndi malangizo a Yesu ndipo pambuyo pake “anabwera mokondwera.” (Luka 10:17) Ngati tivomereza chitsogozo chimene timalandira pa misonkhano yokonzekera utumiki, nafenso tingayembekezere kuwonjezera chimwemwe chathu m’kulalikira uthenga wa Ufumu.—Mac. 13:48, 49, 52.