Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/95 tsamba 1
  • Yehova Amapereka Mphamvu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amapereka Mphamvu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera Kosaleka?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Yehova Amapatsa Mphamvu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Pitirizanibe Kukhala M’gulu la Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Pitirizani Kuyenda Mopita Patsogolo M’njira ya Kachitidwe Yadongosolo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 6/95 tsamba 1

Yehova Amapereka Mphamvu

1 Monga anthu a Yehova, tapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino pamenenso tikusunga ‘mayendedwe okoma mwa amitundu.’ (1 Pet. 2:12; Mat. 24:14) Polingalira za nthaŵi zoŵaŵitsazi ndiponso za zofooka zathu, sitingathe konse kuchita ntchitoyi mwa ife tokha. (2 Tim. 3:1-5) Tili achimwemwe chotani nanga kuti tikhoza kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka thandizo!

2 Mtumwi Paulo anapirira mayesero ambiri. (2 Akor. 11:23-27) Kodi anakhoza bwanji kulimbana ndi ameneŵa ndi kumaliza ntchito yake? Yehova anampatsa “ukulu woposa wamphamvu.” (2 Akor. 4:7) Paulo anavomereza za thandizo la Mulungu limenelo pamene analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afil. 4:13) Yehova adzatithandiza mofananamo. Kodi tingapeze motani thandizo limeneli?

3 Mwa Kupemphera Kosaleka: Yesu anatilimbikitsa ‘kupitirizabe kupempha, kufuna, ndi kugogoda,’ popanda kuleka. (Luka 11:5-10, NW ) Khama lathu m’pemphero limasonyeza Yehova kuya kwa nkhaŵa yathu, ukulu wa chikhumbo chathu, ndi kuona mtima kwa cholinga chathu. (Sal. 55:17; 88:1, 13; Aroma 1:9-11) Paulo anazindikira kufunika kwa kuchita khama m’pemphero pamene anatilimbikitsa ‘kupemphera kosaleka.’ (1 Ates. 5:17) Pemphero lili imodzi ya njira zazikulu zimene tingapezere nazo thandizo la Yehova.

4 Mwa Kutsatira Chitsogozo cha Teokrase: “Teokrase” amatanthauza kuti “ulamuliro wochitidwa ndi Mulungu,” amene ali chikondi. Timapindula ndi ulamuliro wake mwa kuvomereza ukumu wake ndi kutsatira malangizo ake m’zosankha zazikulu ndi zazing’ono. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amaimira ulamuliro wa teokrase pa dziko lino lapansi. (Mat. 24:45-47) Kuchita mogwirizana ndi gulu limene “kapolo” ameneyo amagwiritsira ntchito nkofunika ngati titi tipeze dalitso la Yehova. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:17.) Yehova adzafupa kukhulupirika kwathu kwa iye ndi kufunitsitsa kwathu kumvera malamulo ake mwa kupereka mphamvu imene tikufuna panthaŵi yoyenerera.—Aheb. 4:16.

5 Mwa Kukhala Oyandikana ndi Abale Athu: Chikondi ndicho chizindikiro chodziŵikitsa ophunzira a Yesu. (Yoh. 13:34, 35) Pokhala ndi maumunthu osiyanasiyana ambiri, pakati pathu pangabuke kusamvana chifukwa cha kusiyana maganizo. Tifunikira kukhala achifundo, okhululukirana mwaufulu. (Aef. 4:32) Zimenezi zimatikhozetsa kukhalabe oyandikirana ndi abale athu okhulupirira ndi kukhala olimbikitsidwa ndi chipiriro chawo cha kuchirimika pa chiyeso. “Podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale [athu] ali m’dziko,” tili ndi nyonga yopatsidwa ndi Mulungu ya kulimbana ndi zitsenderezo zofananazo.—1 Pet. 5:9.

6 Mwa Kusunga Chizoloŵezi Chabwino cha Phunziro Laumwini: Kulimbitsa maganizo ndi mitima yathu mwauzimu kumatikhozetsa kulimbana ndi chiukiro cha Satana. (1 Pet. 5:8) Chizoloŵezi chabwino cha phunziro laumwini chidzawonjezera za mu nkhokwe yathu ya chidziŵitso chaumulungu. Tingathe kupezamo nyonga pamene tiyang’anizana ndi zovuta za tsiku lililonse. Paulo anagogomezera kuti “chidziŵitso cholongosoka” chimachita mbali yofunika pa kupezedwa kwa chipulumutso. (1 Tim. 2:3, 4, NW ) Kudya chakudya chauzimu nthaŵi zonse kuli kofunika.

7 Zogaŵira zonse zofunika pa kutithandiza kukhala olimba zili zopezeka mosavuta mumpingo Wachikristu. Chichirikizo cha mtima wonse cha ntchito zake chidzapereka yankho lotsimikizirika lakuti “[ti]dzayenda koma osalefuka.”—Yes. 40:29-31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena