Gwiritsirani Ntchito Bwino Nthaŵi Yanu
1 Yehova amasamala nthaŵi. Amafuna kuti nafenso tisamale nthaŵi. Mwa gulu lake iye amatithandiza kukhala osamala nthaŵi. Nthaŵi zonse timalimbikitsidwa ‘kuchuluka mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Mwa njira imeneyi, tingakhale ogwira mtima kwambiri mu utumiki wa Yehova.
2 Tonsefe tili ndi nthaŵi yofanana mlungu uliwonse—maola 168. Kodi timaigwiritsira ntchito bwino motani nthaŵi yathu? Kodi timasonyeza kuti tikudziŵadi nthaŵi imene tafikapo malinga ndi kaonedwe ka Yehova? Kodi tikucheukitsidwa ndi zochita zosafunikira?
3 Kuli kofunika kuti ife tikhale adongosolo. Ambiri amayesa kukhala ndi mpambo wa zofunika zoyamba. Chinthu chilichonse chimaikidwa pa mpambowo malinga ndi kufunika kwake. Kodi tingachite motani zimenezo? Baibulo limati munthu ayenera ‘kuona zabwino m’ntchito zake zonse.’ (Mlal. 3:13) Ntchito zina zimatulutsa zipatso zabwino kuposa zina. Talingalirani zipatso zimene ntchito iliyonse idzatulutsa. Kodi kumaliza ntchitoyo kudzadzetsa mapindu aakulu? Kodi ‘mudzaona zabwino’ pa ntchito yanu? Ngati simudzatero, mwina siili ntchito yofunika kwambiri choyamba.
4 Mu Utumiki Wathu: Timayamikira kwambiri pamene ena afika panthaŵi yake pamisonkhano yokonzekera utumiki, kumvetsera mosamalitsa malangizo, ndi kupita mwamsanga m’gawo. Ndi bwino kutanganitsidwa ndi kulalikira m’malo moyembekezera. Mwachionekere Paulo anazindikira kwambiri kufunika kwa dongosolo labwino pamene analemba kuti: “Zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.”—1 Akor. 14:40.
5 Pamene tili mu utumiki wakumunda, tingatayire nthaŵi yofunika pakupuma. Komabe, tingapume pang’ono titagwira ntchito mu utumiki kwa maola angapo. Kapena pamene machedwe akunja sali bwino, kupuma kungatitsitsimule ndi kutithandiza kupitiriza. Komabe, ambiri amakonda kutanganitsidwa ndi kulalikira kwa anthu nalepa kucheza ndi abale pa kupuma mkati mwa nthaŵi yoikidwa pambali kaamba ka utumiki. Kusapambanitsa nkofunika.
6 “Chumba . . . chidziŵa nyengo yake” ya kusamuka, ndipo “nyerere . . . zitengeratu zakudya zawo m’malimwe” kuti zikonzekere nthaŵi yachisanu, limatero Baibulo. (Yer. 8:7; Miy. 6:6-8) Chimenecho ndicho chinsinsi cha kugwiritsira ntchito bwino nthaŵi. Nafenso tiyenera ‘kudziŵa nyengo yathu.’ Popanda kuumirira kwambiri, tiyenera kusamala nthaŵi. Sitifunikira kudziŵa chabe zimene tiyenera kuchita komanso pamene zifunikira kuchitidwa. Tiyenera kukhala ndi chizoloŵezi cha kukonzekera pasadakhale, tikumalola mpata wa kuchedwa kumene kungakhalepo. Tiyeneranso kukonzekera kuchepetsa zochita zina kuti tipatule nthaŵi ya zinthu zina zofunika kwambiri, zonga ngati kukonzekera misonkhano yathu, utumiki wakumunda, ndi zochita zina zateokrase.
7 Tikufuna kukhala ngati Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, amene amatiphunzitsa kuti “kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake.” (Mlal. 3:1) Mwa kugwiritsira ntchito bwino nthaŵi yathu, ‘tingakwaniritse utumiki wathu.’—2 Tim. 4:5.