Mmene Tingachitire Machaŵi
1 Kukhala ndi zochita zochuluka mu utumiki wa Yehova kumatitanganitsa! (1 Akor. 15:58) Timadziŵa za kufunika kwa kuphunzira aliyense payekha ndiponso monga banja, kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kukonzekera misonkhano yampingo ndi kupezekapo, ndi kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda nthaŵi zonse. Oyang’anira ali ndi mathayo a kuŵeta, ndipo amasamalira mathayo enanso a mumpingo. Ena angakhale ndi mathayo olemera a m’banja kapena mathayo osiyanasiyana kwa ena. Kuti zonse ziyende bwino, aliyense afunika kulingalira bwino ndi kulinganiza bwino zinthu zaumwini.
2 Ikani Zofunika Patsogolo: Chipambano pa ‘kuchita machaŵi’ chimadalira pa kuzindikira ndi kulingalira bwino kwathu. (Aef. 5:15, 16) Tiyenera kuzindikira zimene zili “zinthu zofunika kwambiri” ndi kuziika pamwamba pa mpambo wathu wa zinthu zofunika. (Afil. 1:10, NW) Okwatirana ena aŵiri anafotokoza banja lawo lotsatira teokrase motere: “Tinadzaza moyo wathu ndi choonadi . . . Choonadi si mbali ya moyo wathu, ndicho moyo wathu. Zinthu zina zilizonse zimazikidwa pa icho.” Kuika kulambira ndi kutumikira Yehova patsogolo m’moyo wa munthu nkofunika.
3 Dziŵani Zinthu Zotayitsa Nthaŵi: Muli maola 168 mu mlungu umodzi, ndipo tiyenera kugwiritsira ntchito mwanzeru nthaŵi yathu imene tili nayo. Kuti tikhale ndi nthaŵi yokwanira kaamba ka ntchito za teokrase, tiyenera kudziŵa zinthu zotayitsa nthaŵi ndi kuzichepetsa. Kufufuza kwina kunavumbula kuti pa mlungu umodzi, wachikulire wamba ku United States amathera maola oposa 30 pa kupenyerera TV! Kwa ena, nthaŵi yochuluka imathera pa kuŵerenga mabuku akudziko. Ena angapeze kuti amathera nthaŵi yochuluka kwambiri ku macheza, pa zinthu za pamtima, pa kusanguluka, kapena pa zochita zinazake za pakompyuta. Mwinamwake tingafunikire kusanthula ndandanda yathu ya tsiku ndi tsiku mosamalitsa kuti tione mmene tingagwiritsire ntchito bwino nthaŵi yathu. Kuchita mwanzeru kumafuna kuti tiike malire pa ukulu wa nthaŵi imene timathera pa zinthu zosafunika.
4 Khalani ndi Ndandanda Yabwino: Kaya mikhalidwe yathu yaumwini ikhale yotani, aliyense wa ife angachite machaŵi pa kulondola zinthu zauzimu. Ena apeza kuti kudzuka mwamsanga tsiku lililonse kumawathandiza kuchita zambiri. Ngati timatha nthaŵi yaikulu paulendo wa kuntchito kapena podikira ena, tingagwiritsire ntchito ina ya nthaŵi imeneyo kuŵerenga Baibulo, kukonzekera misonkhano, kapena kumvetsera nkhani zokonzedwa ndi Sosaite pa makaseti. Mabanja amapindula kwambiri mwa kupatula nthaŵi yakutiyakuti yokhazikitsidwa bwino yochitira phunziro pamodzi. Ngati wapabanja aliyense samachedwa pobwera ku phunziro la banja, zimachititsa aliyense kukhala ndi nthaŵi yowonjezereka.
5 Pamene tsiku lililonse lipita, timazindikira mowonjezereka kuti “yafupika nthaŵi [yotsala, NW].” (1 Akor. 7:29) Moyo wathu umadalira pa mmene timagwiritsira ntchito nthaŵi yofunika yotsalayi. Tidzadalitsidwa ngati tichita nayo machaŵi kotero kuti tisunge zinthu za Ufumu pamalo oyamba!—Mat. 6:33.