Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/96 tsamba 6
  • Thandizani Ena Kupeza Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Ena Kupeza Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • “Moyo Wosatha ndi Uwu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Chidziŵitso Chonena za Mulungu Woona Chimatsogolera ku Moyo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • “Chikhulupiriro Chidza ndi Mbiri”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 3/96 tsamba 6

Thandizani Ena Kupeza Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo

1 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti chili ‘chifuniro cha Mulungu kuti anthu amtundu uliwonse ayenera kufika pa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi.’ (1 Tim. 2:4, NW) Kodi tingathandize ena motani kupeza chidziŵitso chimenecho? Njira imodzi njakupanga maulendo obwereza kwa anthu amene chikondwerero chawo chadzutsidwa ndi buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life. Buku limeneli limafotokoza choonadi cha Baibulo m’mawu omveka, osavuta, ndi osankhidwa bwino. Mwa kuliphunzira, anthu amtundu uliwonse adzatsogoleredwa ku moyo. Kodi nchiyani chimene tinganene chimene chidzalimbikitsa ena kuliphunzira limodzi nafe?

2 Kwa aja amene anasonyeza chidwi pa Baibulo monga chitsogozo chothandiza, mungabwerereko kukawapempha kuphunzira nawo, mwinamwake mukumati:

◼ “Pamene ndinali pano, tinakambitsirana za chifukwa chake tingakhulupirire Baibulo monga magwero a chitsogozo chothandiza. Chifukwa cha kuuziridwa kwake ndi Mulungu, Baibulo lilinso magwero otsimikizirika a chitonthozo ndi chiyembekezo, monga momwedi mmodzi wa atumwi a Kristu ananenera. [Ŵerengani Aroma 15:4.] Pamapeto a kukambitsirana kwathu koyamba, ndinafunsa funso lakuti, Kodi tingapindule motani ife enife ndi chidziŵitso chimene chili m’Baibulo? Ŵerengani ndime 18 patsamba 11 m’buku la Knowledge. Tchulani kuti Mboni za Yehova zikuchititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi mamiliyoni asanu padziko lonse, zikumathandiza anthu kulikonse kupeza chidziŵitso chotsogolera ku moyo wosatha. Sonyezani mwachidule mmene phunziro limachitidwira, mukumagwiritsira ntchito ndime zisanu zoyamba m’mutu 1.

3 Ngati poyamba munakambitsirana za nkhani ya pemphero ndi munthu wina, mungayese kafikidwe aka poyesayesa kuyambitsa phunziro:

◼ “Ndikhulupirira kuti munasangalala ndi chidziŵitso chonena za pemphero chimene tinakambitsirana m’buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life. Ndinalonjeza kuti ndidzabweranso ndi kudzakambitsirana nanu za awo amene amapemphera kwa Mulungu, mmene nawonso angamvetsere kwa iye. Taonani zimene zalongosoledwa patsamba 158. [Ŵerengani ndime 18.] Motero, mwa kuphunzira Baibulo ife eni, timamvetsera zimene Mulungu amatiuza. Kuchita zimenezo kumatikokera pafupi ndi iye ndipo kumatithandiza kulimbana ndi mavuto atsiku ndi tsiku amene timapempherera. Ndingakonde kuphunzira nanu Baibulo.” Ngati munthuyo akufuna, yambirani pa mutu woyamba wa buku la Knowledge.

4 Ngati munagwiritsira ntchito kafikidwe kachindunji kuti muyambe phunziro, munganene motere pogwirizanitsa ndi makambitsirano oyamba:

◼ “Ndayesa kuima pano kachiŵirinso chifukwa chakuti ndafuna kukuuzani zambiri ponena za programu yathu yaulere ya phunziro la Baibulo. Ndinakusiyirani buku longa ili la Knowledge That Leads to Everlasting Life, limene lili buku lothandiza kuphunzira limene timagwiritsira ntchito. Onani mmene limatilimbikitsira kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu. [Ŵerengani ndime 23 patsamba 22.] Chonde ngati mungatenge buku lanu, mwina tingapitirize kuphunzira kuchokera pamene tinasiyira panthaŵi ija.” Ngati phunziro linali lisanayambidwe paulendo woyamba, munganene kuti: “Mwinamwake ino ingakhale nthaŵi yabwino yakuti ndikusonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo.” Mutakambitsirana ndime zingapo, linganizani nthaŵi yotsimikizirika ya kudzafikanso kaamba ka phunziro lotsatira.

5 Kugwiritsira ntchito mogwira mtima buku la Knowledge kudzatikhozetsa kuwanditsa chidziŵitso cholongosoka kaamba ka dalitso la ena. (Miy. 15:7) Chidziŵitso chimenecho chidzakondweretsa awo amene mtima wawo uli wabwino, chidzawapatsa chikondwerero, ndipo chidzakhala chisonkhezero champhamvu kwa iwo cha kuchita mogwirizana ndi chilungamo cha Yehova, potsirizira pake chowatsogolera ku moyo wosatha.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena