“Moyo Wosatha ndi Uwu”
1 Mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 17:3 ayenera kuonedwa mwamphamvu. Iye anatanthauza zimene ananena—kuloŵetsa chidziŵitso cha Mulungu ndi Kristu ndiko moyo wosatha! Koma kodi ndi mwa kupeza kwathu chidziŵitso cha Yehova ndi Yesu kokha kumene tidzafupidwa nako moyo wamuyaya? Ayi. Aisrayeli anadziŵa kuti Yehova anali Mulungu wawo, koma moyo wawo sunasonyeze chikhulupiriro chimenecho. Chotero, anataya chiyanjo chake. (Hos. 4:1, 2, 6) Lerolino anthu mamiliyoni ambiri ‘angakhale ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso.’ (Aroma 10:2) Afunikira kufika pa kudziŵa Yehova, “Mulungu woona yekha,” ndi kuphunzira mmene angamtumikirire moyenera. Ndi cholinga chimenecho, m’November tidzagaŵira bukulo Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kodi mudzagwiritsira ntchito kafikidwe kotani pogaŵira buku la Chidziŵitso? Nawa malingaliro ena amene angakuthandizeni.
2 Popeza kuti lingaliro la kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi lili latsopano kwa anthu ochuluka, mawu oyamba awa angawakope mtima:
◼ “Tikufunsa anansi athu funso. Ngati munali mutapemphedwa kuti mukhale ndi moyo kosatha m’dziko longa ili, kodi mukanavomera? [Sonyezani chithunzi cha pa masamba 4-5 m’buku la Chidziŵitso. Yembekezerani yankho.] Umenewu ungakhaledi mkhalidwe wanu wachimwemwe m’moyo. Koma kodi muganiza kuti muyenera kuchitanji kuti mudzaone zimenezi zitachitika kwa inu? [Yembekezerani yankho.] Onani zimene zikufunika kuzichita malinga ndi kunena kwa Yohane 17:3. [Ŵerengani.] Buku limeneli likuthandiza ambiri kupeza mtundu wapadera umenewu wa chidziŵitso. Kodi mungakonde kukhala ndi buku lanulanu loti muziŵerenga? [Yembekezerani yankho.] Paulendo wanga wotsatira, tidzakambitsirana za chifukwa chake kuli koyenera kukhulupirira kuti tingapeze moyo wosatha padziko lapansi pompano.”
3 Pamene mubwerera kwa aja amene munakambitsirana nawo Yohane 17:3, mungapitirize motere:
◼ “Paulendo wanga wathawo, ndinakuŵerengerani mawu a Yesu okondweretsa opezeka pa Yohane 17:3, pamene anatsimikizira kuti kudziŵa Mulungu ndi iye ndiko moyo wosatha. Koma anthu ambiri amakhulupirira kuti moyo wabwino kwambiri ungapezedwe kumwamba kokha. Kodi mukulingalira motani pa zimenezo? [Yembekezerani yankho.] Ngati buku limene ndinakusiyirani lija lili pafupi, ndingakonde kukusonyezani mavesi ena a m’Baibulo amene amasonyeza kuti Paradaiso adzabwezeretsedwa padziko lapansi. [Kambitsiranani ndime 11-16 pa masamba 9-10 m’buku la Chidziŵitso.] Paulendo wanga wotsatira, ndidzafuna kukusonyezani chifukwa chake mungakhulupirire malonjezo ameneŵa amene akupezeka m’Baibulo. Pakali pano, mwina mungaŵerenge mutu 2 m’buku lanu.”
4 Nawu ulaliki umene mungafune kugwiritsira ntchito kwa anthu amene ali achipembedzo:
◼ “Takhala tikulankhula ndi anansi athu ponena za chifukwa chake pali zipembedzo zambiri zosiyanasiyana m’dziko. M’Zambia mokha muno muli zipembedzo 96, ndipo m’dziko lonse muli zoposa 10,000. Komabe, pali Baibulo limodzi lokha. M’lingaliro lanu, kodi nchifukwa ninji pali msokonezo umenewu wa zipembedzo? [Yembekezerani yankho. Tsegulani buku la Chidziŵitso pa mutu 5, ndi kuŵerenga ndime 1.] Mudzalandira mayankho okhutiritsa a mafunso amenewo mwa kuŵerenga mutu uwu. Ndingakonde kukusiyirani bukuli ngati mukufuna kulipenda.” Ngati alilandira, pangani makonzedwe otsimikizirika a kubwererako, ndi kunena kuti: “Pamene ndidzabweranso, mwina tidzakambitsirana za kuti kaya ngati zipembedzo zonse zangokhala njira zosiyanasiyana zopita kumalo amodzi.”
5 Pamene mubwerera kukapitiriza makambitsirano onena za chifukwa chake pali zipembedzo zochuluka, munganene kuti:
◼ “Panthaŵi ija imene ndinalankhula nanu, ndinadzutsa funso lakuti kaya zipembedzo zonse zangokhala njira zosiyanasiyana zopita kumalo amodzi. Kodi mukuganiza bwanji pamenepo? [Yembekezerani yankho.] Ndikufuna kukusonyezani m’buku limene ndinakusiyirani lija zimene Yesu ananena pankhaniyo. [Tsegulani pa mutu 5 m’buku la Chidziŵitso, ndipo ŵerengani ndime 6-7, kuphatikizapo Mateyu 7:21-23.] Mungadabwe chifukwa chake kuli kofunika kwambiri kudziŵa bwinobwino chifuniro cha Mulungu. Mudzapeza kuti ndime zotsatira nzopatsa chidziŵitso kwambiri. Chonde ŵerengani zotsalazo m’mutu umenewu. Pamene ndidzabweranso, ndidzakonda kukusonyezani kufunika kwa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo.”
6 Kaŵirikaŵiri kafikidwe kachindunji kamakhala kachipambano poyambitsa maphunziro a Baibulo. Nali lingaliro la mawu oyamba limene lili patsamba 13 m’buku la “Kukambitsirana”:
◼ “Ndafika kudzakusonyezani kosi yaulere ya phunziro la Baibulo lapanyumba. Ngati ndingathe, ndingakonde kutenga mphindi zochepa kusonyeza mmene anthu m’maiko okwanira 200 amaphunzirira Baibulo monga timagulu tabanja. Tingagwiritsire ntchito uliwonse wa mitu yokambitsirana imeneyi. [Sonyezani mpambo wa zamkati wa m’buku la Chidziŵitso.] Kodi ndi uti umene umakukondweretsani mwapadera?” Yembekezerani kuti munthuyo asankhe. Tsegulani pa mutu umene wasankha, ndi kuyamba phunziro pa ndime yoyamba.
7 Naka kafikidwe kenanso kachipambano kamene mungayese kuyambitsira maphunziro:
◼ “Ndimachititsa maphunziro a Baibulo aulere ndipo ndili ndi nthaŵi mu ndandanda yanga ya ophunzira owonjezereka. Buku ili lothandizira kuphunzira Baibulo ndi limene timagwiritsira ntchito. [Sonyezani buku la Chidziwitso.] Kosi imeneyi imangotenga miyezi yoŵerengeka yokha ndipo imapereka mayankho pa mafunso onga akuti: Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika? Kodi nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa? Kodi nchiyani chimene chimachitika kwa okondedwa athu akufa? Ndipo ndi motani mmene tingayandikirire kwa Mulungu? Ndiyeno funsani kuti, “Kodi ndingakusonyezeni kuphunzira kwake?” Ngati akana phunzirolo, gaŵirani buku la Chidziŵitso ndi kulinganiza kudzabweranso.
8 Ha, ndi chuma cha mtengo wapatali chotani nanga chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Kristu kwa onse amene ali nacho! Kuchiloŵetsa ndikodi moyo wosatha m’mikhalidwe yangwiro. Tiyenitu tigwiritsire ntchito mpata uliwonse mu November kuuza ena za chidziŵitso chotsogolera ku moyo wosatha.