Sitinakhalepo ndi Zabwino Zotere Mwauzimu!
1 Anthu ambiri akuyembekezera tsiku pamene anganene kuti, “Sitinakhalepo ndi zabwino zotere!” Malinga ndi kuganiza kwawo, tsiku limenelo lidzabwera pamene adzakhala ndi chuma chochuluka, chimene chidzawalola ‘kupumula, kudya, kumwa ndi kukondwera.’ (Luka 12:19) Mosiyana ndi zimenezo, tsopano lino tikhoza kunena kuti m’lingaliro lauzimu, sitikusoŵa kanthu kabwino kalikonse. (Sal. 34:10) Kodi zimenezo nzotheka motani?
2 Miyambo 10:22 imanena kuti “madalitso a Yehova alemeretsa.” Ife amene tili ndi chiyanjo cha Mulungu chotere tinganenedi kuti Mulungu “atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” (1 Tim. 6:17) Zimenezi zimatipangitsa kukhala anthu olemera koposa padziko lapansi!
3 Kuŵerenga Madalitso Athu: Oŵerengeka a ife tili ndi chuma chakuthupi chochuluka. Komabe, ndife odala chifukwa chakuti sitimadera nkhaŵa mopambanitsa ponena za zofunika zathu za tsiku ndi tsiku. Yehova amadziŵa zinthu zimene timafuna, ndipo akulonjeza kutipatsa zimenezo. (Mat. 6:31-33) Chitsimikizo chake chimatipatsa mtendere wa maganizo umene ulidi wosagulika.
4 Komabe, madalitso athu auzimu, ngaakulupo. Moyo wathu umadalira pa chakudya chauzimu chochokera kwa Yehova. (Mat. 4:4) Awo amene amayang’ana ku magwero akudziko kaamba ka chakudya chauzimu amakhala ndi njala pamene kuli kwakuti ife tili kudya ndi kumwa ndi kukhuta. (Yes. 65:13) “Kapolo wokhulupirika” amatisonya ku magwero osatha a chidziŵitso chimene chimatsogolera ku moyo wosatha.—Mat. 24:45; Yoh. 17:3.
5 Ubale wathu wamtengo wapatali wapadziko lonse umatipatsa mayanjano abwino a abale ndi alongo achikondi amene amakhala kumbali zonse za dziko lapansi. (Yoh. 13:35) Mpingo wakwathu ndiwo malo amtendere obisalako, kumene tingapeze chitonthozo ndi chitsitsimulo. Akulu amalindirira moyo wathu, kutithandiza kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana. (Aheb. 13:17) Kuyandikana ndi abale athu kumatichititsa kulimbikitsana, kumene kumatipatsa nyonga kuti tilimbikire.—Aroma 1:11, 12.
6 Ntchito yathu ilinso dalitso. Ntchito zambiri zolembedwa nzotopetsa ndi zosakhutiritsa. Kugaŵana uthenga wabwino kumadzetsa chisangalalo kwa ena ndi chimwemwe kwa ifeyo. (Mac. 20:35) Timathadi kuona zabwino kaamba ka kugwiritsa ntchito kwathu konse.—Mlal. 2:24.
7 Koposa zonse, tili ndi chiyembekezo chodabwitsa chamtsogolo. (Aroma 12:12) Tikuyang’ana kutsogolo ku dziko latsopano langwiro ndi lachilungamo, mmene tidzakhala ndi okondedwa athu m’chimwemwe ndi mtendere kosatha! Chiyembekezo chimenechi chili chuma chamtengo woposa chinthu chilichonse chimene dzikoli lingatipatse.—1 Tim. 6:19.
8 Kodi Chiyamikiro Chathu Tingachisonyeze Motani? Sitingabwezere Yehova zimene watichitira. Tingangosonyeza chiyamikiro chathu mwa (1) kumuyamikira tsiku ndi tsiku kaamba ka chisomo chake (Aef. 5:20), (2) kusonyeza chikondi chathu mwa kukhala omvera (1 Yoh. 5:3), (3) kuyeretsa dzina lake mwa kulalikira uthenga wabwino (Sal. 83:18), ndi (4) kuchirikiza mpingo wachikristu mwa kugwirizana kwathu kwa mtima wonse.—1 Tim. 3:15.
9 Tili ndi chifukwa chabwino chokhalira anthu achimwemwe koposa padziko lapansi. (Sal. 144:15b) Malingaliro athu, kakhalidwe, ndi utumiki zisonyezetu chisangalalo chimene tili nacho m’paradaiso wathu wauzimu. Sitinakhalepo ndi zabwino zotere!