Misonkhano Yautumiki ya May
Mlungu Woyambira May 6
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Pendani “Kutamanda Yehova m’Kuimba Kogwirizana!”
Mph. 15: “Khalani a Mtima Wonse!” Mafunso ndi mayankho. Malinga ndi nthaŵi, kambitsiranani “Zinthu Zokambitsirana Monga Banja” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1982, tsamba 27.
Mph. 20: “Lankhulani Choonadi kwa Mnzanu.” Mafunso ndi mayankho. Pendani maulaliki osonyezedwa. Limbikitsani atsopano kugaŵanamo mu kugaŵira magazini, kugwiritsira ntchito maulaliki achidule poyamba. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zimene zikuphatikizapo kufotokoza ndemanga ya patsamba 2 ya Nsanja ya Olonda. Chonde onani nkhani yakuti “Konzekerani Ntchito ya Kugaŵira Sabusikrispishoni mu April” mu Utumiki Wathu Waufumu wa February.
Nyimbo Na. 148 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 13
Mph. 7: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 18: “Sitinakhalepo ndi Zabwino Zotere Mwauzimu!” Mafunso ndi mayankho. Khalani ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu, kuphatikizapo wachichepere, kuti atchule ena a madalitso awo. Malizani mwa kusonyeza mmene chiyamikiro chowonjezereka chimatisonkhezera kukhala achangu mu utumiki wopatulika.
Mph. 20: Chitirani Zinthu Pamodzi Monga Banja. Pocheza atate alankhula ndi banja lawo za kufunika kwa kuchitira zinthu pamodzi, yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya September 1, 1993, masamba 16-19. Gogomezerani phunziro la banja ndi ntchito ya kulalikira. Sonyezani mmene mabanja amakono akugaŵanikirana chifukwa chakuti nthaŵi yaikulu samakhala pamodzi ndipo saali ogwirizana konse. Kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kugaŵanamo mu utumiki pamodzi kuli dalitso m’banja lachikristu. Gogomezerani kuti atate afunika kulinganiza bwino zinthu zimenezi ndi kuti amayi afunika kugwirizana nazo. Ana ayenera kukondwera ndi ntchito zauzimu, kugwirira ntchito pafupi ndi makolo awo. Banja lidzakhala logwirizana ndipo lidzalimbitsidwa kuti lilimbane ndi zisonkhezero zomawonjezereka za kuchita zinthu zakudziko.
Nyimbo Na. 193 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 20
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Limbikitsani onse kugaŵanamo mu kugaŵira magazini.
Mph. 15: “Pitirizanibe Kulankhula Choonadi.” Gogomezerani kufunika kwa kupanga maulendo obwereza, ndi chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro. Gaŵirani sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri zachidule.
Mph. 20: Zosoŵa zapamalopo kapena kambani nkhani pa mutu wakuti: “Ngati Muli ndi Mangawa a Misonkho, Perekani Misonkho,” ya mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1994, masamba 26-28.
Nyimbo Na. 28 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 27
Mph. 5: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: Kugaŵira Knowledge That Leads to Everlasting Life mu June. Woyang’anira utumiki choyamba afotokoza chifukwa chimene buku la Knowledge linafalitsidwira. Ndiyeno apenda zina za mfundo zake zazikulu ndi ofalitsa okhoza aŵiri kapena atatu. Bukuli limayankha mafunso ponena za mtsogolo mwathu, kuvutika kwa anthu, Ufumu wa Mulungu, khalidwe laumulungu, moyo wa banja, ndi mapindu a pemphero. Aŵiri osiyana a m’kaguluko achita chitsanzo kusonyeza mafikidwe amene angagwiritsiridwe ntchito kuyambitsa phunziro kaya paulendo woyamba kapena paulendo wobwereza. Ndiyeno woyang’anira utumiki afotokoza mfundo zotsatirapozi. Pali kufunika kwa kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri opita patsogolo panthaŵi yaifupi. Bukuli linalinganizidwira makamaka chifuno chimenecho. Limapereka choonadi m’njira yabwino ndi yomveka. Mafunso a ndime iliyonse, ndi amenenso ali kumapeto kwa mutu uliwonse, amatithandiza kusumika maganizo pa mfundo zazikulu. Bukuli limaphatikizapo mayankho a mafunso ofunsidwa kwa odzipatulira chatsopano amene akufuna kubatizidwa. Limbikitsani onse kugwira ntchito ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro mu June.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Ŵerengani ndi kukambitsirana ndi omvetsera.
Mph. 15: “Kodi Muli ndi Zochita Zambiri?” Mafunso ndi mayankho. Malinga ndi nthaŵi, phatikizanipo ndemanga zochokera mu Galamukani! wa June 8, 1990, masamba 29-31. Khalani ndi wofalitsa mmodzi kapena aŵiri kuti asimbe mwachidule zimene achita kuti akwaniritse zochita zateokrase zambiri.
Nyimbo Na. 155 ndi pemphero lomaliza.