Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/96 tsamba 3
  • Kodi Muli ndi Zochita Zambiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muli ndi Zochita Zambiri?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • “Tiyeninso Tichotse Cholemera Chirichonse”
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mmene Tingachitire Machaŵi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Kodi Mungakondwere ndi Zochita Zambiri?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Ntchito Imakulepheretsani Kulalikira?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 5/96 tsamba 3

Kodi Muli ndi Zochita Zambiri?

1 Paulo analimbikitsa kuti tikhale “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse.” (1 Akor. 15:58) Tikulimbikitsidwa kumakhala ndi ndandanda yatsiku ndi tsiku ya phunziro laumwini, kugaŵanamo mu utumiki mokhazikika, kupezeka pamisonkhano mokhulupirika, ndi kusamalira ntchito za mpingo mwakhama. Kuwonjezera pa zimenezo, tiyenera kuthandiza ena amene akufuna thandizo. Pokhala ndi zambiri zochita, nthaŵi zina tingamve kukhala othedwa mphamvu, tikumalingalira kuti tiyenera kufunafuna njira zochepetsera ntchito zathu.

2 Pali mikhalidwe ina imene ingachititse kuchotsapo kapena kuchepetsako zinthu zina kukhala kwanzeru ndi koyenera. Anthu ena amalingalira kuti afunika kuchita zilizonse zimene ena awapempha kuchita. Kusalinganiza zinthu pamkhalidwewu kungachititse kupanikizika ndi kupsinjika maganizo zimene zingakhale zowonongadi.

3 Linganizani Zinthu: Mfungulo ya kulinganiza zinthu ndiyo kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo wa ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.’ (Afil. 1:10, NW) Zimenezo zimangotanthauza kuti tisumike maganizo pa zinthu zimene zilidi nkanthu ndiyeno, ngati nthaŵi ndi mikhalidwe ilola, kusamalira zinthu zosafunika kwenikweni. Mathayo a banja mosakayikira ali pamwamba pa zinthu zofunika. Mathayo ena akuntchito ayenera kuchitidwa. Komabe, Yesu anaphunzitsa kuti zosankha zathu zoyambirira ziyenera kuzikidwa pa pulinsipulo lakuti tikufuna Ufumu choyamba. Tiyenera choyamba kuchita zinthu zimene zidzatilola kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kwa Yehova.—Mat. 5:3; 6:33.

4 Pomakumbukira zimenezi, tidzatsimikizira kuti pandandanda yathu yokhala ndi zambiri tichotsepo zofuna zaumwini zosafunikira, zochitika zosangulutsa zopambanitsa, ndi kudzipereka kwa ena kosafunikira. Pokonza zochita zathu za mlungu uliwonse, tidzapatula nthaŵi ya phunziro laumwini lokwanira, kutengamo mbali moyenerera mu utumiki, kupezeka pamisonkhano, ndi zinthu zina zilizonse zogwirizana kwambiri ndi kulambira kwathu. Nthaŵi yotsalayo ingagaŵidwe pakati pa zofuna zina, kudalira pa mmene zimatithandizira kufikira chonulirapo chathu chachikulu cha kukhala Akristu achikatikati amene amaika Ufumu patsogolo.

5 Ngakhale titachita zimenezo, tingaonebe katundu wathu kukhala wolemera kwambiri. Ngati zili tero, tiyenera kuyankha chiitano cha Yesu chakuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mat. 11:28) Ndiponso yang’anani kwa Yehova, amene “tsiku ndi tsiku atisenzera katundu” ndi kulimbitsa wolefuka. Akulonjeza kuti sadzalekerera wolungama agwedezeke. (Sal. 55:22; 68:19; Yes. 40:29) Tingakhale otsimikizira kuti mapemphero athu adzayankhidwa, kutitheketsa kulimbikira m’moyo wachangu wa zochita za teokrase.

6 Pamene kuli kwakuti tili otsimikizira kukhala otanganitsidwa kulondola zinthu za Ufumu zoyenerera, tingasangalale kudziŵa kuti kuchititsa kwathu sikuli chabe mwa Ambuye.—1 Akor. 15:58.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena