Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/04 tsamba 4
  • Penyani Bwino Mmene Mumagwiritsira Ntchito Nthaŵi Yanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Penyani Bwino Mmene Mumagwiritsira Ntchito Nthaŵi Yanu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndizichita Masewera a Pakompyuta?
    Galamukani!—2008
  • Mmene Tingachitire Machaŵi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Kodi Ndiyenera Kuchita Maseŵero Apakompyuta Kapena Apavidiyo?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Ndiyenera Kuchita Masewera a Pakompyuta?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 1/04 tsamba 4

Penyani Bwino Mmene Mumagwiritsira Ntchito Nthaŵi Yanu

1. Kodi anthu kulikonse ali ndi vuto lanji masiku ano?

1 Masiku ano pamene kuli zipangizo zambiri zopulumutsira nthaŵi ndi zochepetsa ntchito, anthu ambiri amapezeka kuti ali ndi zochita zambiri koma ali ndi nthaŵi yochepa yochitira zinthuzo. Kodi zimakuvutani kupitirizabe kuchita zinthu zauzimu bwinobwino? Kodi mumafuna mutakhala ndi nthaŵi yambiri yochitira utumiki? Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthaŵi yathu?—Sal. 90:12; Afil. 1:9-11.

2, 3. Kodi zinthu zimene timachita masiku onse pa moyo wathu zingatibweretsere vuto lanji, nanga aliyense wa ife angadzipende bwanji?

2 Dziŵani Zotayitsa Nthaŵi: Tonsefe tiyenera kupenda nthaŵi ndi nthaŵi mmene timagwiritsira ntchito nthaŵi yathu. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” (Aef. 5:15, 16) Zinthu zimene timachita masiku onse pa moyo wathu, monga ntchito yolembedwa, kupita kumsika, kudya, kuyeretsa pakhomo, maulendo, kupita kusukulu, ndi kugona, zili ndi nthaŵi yake. Tingagwiritsenso ntchito nthaŵi ina pa kusangalala. Komabe, zimavuta kugaŵa bwinobwino nthaŵi yochitira chilichonse cha zimenezi. Ngakhale zili choncho, tifunikabe kuyesetsa ndithu. Kodi tingachite motani?

3 Mlungu umodzi uli ndi maola 168, ndipo tifunikira kugwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi imene tili nayo. Kuti tikhale ndi nthaŵi yokwanira yochitira zinthu zauzimu, tifunikira kudziŵa ndi kuchepetsa zinthu zotayitsa nthaŵi. Ena amatayira nthaŵi yochuluka kuonera mavidiyo, TV ndi kuŵerenga mabuku akudziko. Enanso mwina amathera nthaŵi yambirimbiri akucheza ndi anzawo, kuchita zimene amakonda, kusangalala, kapena ali kubizinezi inayake. Kuti tigwiritse ntchito bwino nthaŵi yathu, tifunikira kupenda zimene timachita patsiku. Kuchita zinthu mwanzeru kumafuna kuti tiike malire pa nthaŵi yomwe timagwiritsa ntchito pa zinthu zosafunika kwenikweni.—1 Akor. 7:29, 31.

4. Kodi tonsefe tingasinthe motani zina n’zina, ndipo n’chifukwa chiyani?

4 Kugwiritsa Ntchito Nthaŵi Mwanzeru: Yesu anati: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:33) Mwachidziŵikire, zinthu za Ufumu ziyenera kukhala zoyamba pankhani yogwiritsa ntchito nthaŵi yathu. Tikanati tigaŵe nthaŵi yathu muja timachitira pokonza bajeti ya ndalama zathu, nthaŵi imene tingapatule kuti ikhale ya misonkhano yachikristu, phunziro la Baibulo labanja, ndi ntchito zina zauzimu monga utumiki wa kumunda ndi phunziro laumwini, sitingaigwiritse ntchito pa zinthu zina. Tikamagaŵa nthaŵi yathu, tiyenera kuikaponso zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Payenera kukhala nthaŵi yopita kuntchito kuti tithandizike ifeyo ndiponso banja lathu. M’pofunikanso kukhala ndi nthaŵi ya kudya ndi kugona, komanso yosamalira zosoŵa za banja. Mwa zinthu zoyambirira pa ndandanda ya akulu ndi atumiki otumikira, payenera kukhala nthaŵi yokonzekera ndi kusamalira maudindo awo auzimu. Bwanji osakonza ndandanda ngati imeneyi, ndi kuona ngati mwa zinthu zoyambirira pali zinthu zosafunikira kwenikweni kukhalapo?

5. Kodi tingapatule bwanji nthaŵi yochitira zinthu zauzimu, ndipo kuchita zimenezi kuli ndi phindu lanji?

5 Mwina mungafunike kuchita zimenezi ngati pali mbali zimene mukufunika kusintha. Kodi mungapatule nthaŵi yokwana theka la ola tsiku lililonse pa zinthu zosafunika zimene mumachita? Imeneyi ndi pafupifupi nthaŵi imene mungafunike tsiku lililonse kuti muŵerenge Baibulo lonse m’chaka chimodzi. Zimenezi n’zopindulitsa kwambiri mwauzimu. (Sal. 19:7-11; 119:97-100) Khalani ndi nthaŵi yeniyeni yoŵerenga Baibulo, yokonzekera misonkhano, ndiponso ya utumiki wa kumunda. (1 Akor. 15:58) Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuchepetsa zinthu zokutayitsani nthaŵi, ndipo zidzakuthandizani ‘kudziŵitsa chifuniro cha Ambuye n’chiyani.’—Aef. 5:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena