‘Timalalikira Mawuwo’
1 Mogwirizana ndi malongosoledwe a Baibulo a “masiku otsiriza,” anthu ochuluka lerolino ali chabe ndi “maonekedwe a chipembedzo.” (2 Tim. 3:1, 5) Zili choncho chifukwa chakuti atsogoleri achipembedzo alephera kupereka chitsogozo chenicheni chauzimu ku nkhosa zawo. Atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu sakuchirikiza Baibulo. Iwo amakonda kumangobwereza ziphunzitso zopanda pake za afilosofi ndi akatswiri a zaumulungu kapena kulankhula nkhani za makhalidwe a anthu ndi zandale m’malo molalikira Mawu a Mulungu. Atsogoleri achipembedzo ambiri samalikhulupirira Baibulo. Amaliona kukhala lachikale, motero amakonda kuphunzitsa mwachinyengo nthanthi ya chisinthiko m’malo mwa chiphunzitso cha Baibulo cha Mlengi Wamkulu. Atsogoleri achipembedzo ochuluka samatchula nkomwe dzina laumwini la Mulungu, ndipo amangopenya osanena kalikonse pamene dzinalo likuchotsedwa m’mabaibulo amakono.
2 Monga momwe zinalili kwa atsogoleri achipembedzo a m’tsiku la Yesu, atsogoleri achipembedzo a lerolino akuphunzitsa pachabe. (Mat. 15:8, 9) Ndendende ndi mawu onenedweratu ndi mneneri Amosi. Pali “njala, . . si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Anthu amafunikira chakudya chauzimu cha Mawu a Mulungu koposa chinthu china chilichonse.
3 Mmene Tingakhutiritsire Zosoŵa za Anthu Zauzimu: Paulo analimbikitsa Timoteo kumamatira ku ‘malembo opatulika, okhoza kupatsa [munthu] nzeru kufikira chipulumutso,’ ndipo anamsonkhezera ‘kulalikira mawu’ kwa ena. (2 Tim. 3:14, 15; 4:2) Monga Mboni za Yehova, tiyenera kumamatira ku chiphunzitso cha Baibulo pamene tikulalikira, kutsanzira Chitsanzo chathu, Yesu, yemwe anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.” (Yoh. 7:16) Timagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu monga maziko a chiphunzitso chathu chifukwa chakuti timazindikira kuti ali ndi nzeru yaumulungu, ndipo tikufuna kuti anthu adziŵe magwero a chidziŵitso chimene timagaŵana nawo.—1 Akor. 2:4-7.
4 Anthu ayenera choyamba kumva choonadi m’Baibulo kuti aphunzire za Yehova ndi kuti amkhulupirire. Paulo analemba mwanzeru kuti: “Adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:14) Mwa kulalikira Mawu a Mulungu, timathandiza ena kupeza chikhulupiriro mwa chidziŵitso cholongosoka. Chidziŵitso choterocho chikhoza kusintha moyo kukhala wabwinopo ndipo chimaterodi. Mngelezi wolemba mabuku Charles Dickens, analemba za Baibulo kuti: “Ndilo buku labwino kuposa onse amene anakhalapo kapena amene adzakhalapo m’dziko, chifukwa limakuphunzitsani maphunziro abwino koposa amene angatsogolere munthu aliyense woyesayesa kukhala woona ndi wokhulupirika.”
5 Aja omwe ali ndi njala ya choonadi chauzimu amazindikira kuti chimachirikizidwa ndi ukumu wa Mawu a Mulungu. Kalelo mu 1913, Frederick W. Franz, pamene anali wophunzira wachichepere pakoleji, anapatsidwa kabuku ka mutu wakuti Where Are the Dead? (Kodi Akufa Ali Kuti?) Ataŵerenga ndi chidwi chachikulu yankho la Baibulo pa funso limeneli, anati: “Ichi ndicho choonadi.” Mamiliyoni ofunafuna choonadi alingalira mofananamo. Tipitirizetu kulalikira Mawuwo mwakhama ndi mwachangu ndi kusangalala pomamva ena akunena kuti: “Ichi ndicho choonadi.”