“Khalani Akuyamika”
1 Ambiri a ife paubwana wathu anatiphunzitsa kunena “chonde” ndi “zikomo” pamene wina anatichitira chabwino kapena kutisonyeza chifundo. Paulo akutilangiza kuti ‘tikhale oyamika’ nthaŵi zonse, ndipo tiyenera kwenikweni kuthokoza Yehova. (Akol. 3:15, 16) Koma kodi ndi motani mmene tingasonyezere kuti Mlengi wathu Wamkulu timamyamikira? Ndipo tili ndi zifukwa zapadera zotani zomyamikira?
2 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Akor. 15:57) Nthaŵi ya Chikumbutso chaka chilichonse, timakumbutsidwa za chikondi chosayerekezeka chimene onse aŵiri Mulungu ndi Kristu anasonyeza pokonza dipo limene limatipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Popeza kuti pafupifupi tonsefe tataya okondedwa athu mu imfa, tikuyamikira chotani nanga lonjezo la Yesu la chiukiriro! Mitima yathu imasefukira ndi zithokozo pamene tilingalira za chiyembekezo cha kupulumuka mapeto a dongosolo lino osafa konse. (Yoh. 11:25, 26) Sitingathe kufotokoza mokwanira chiyamikiro cha madalitso onse osaneneka amene tidzalandirabe padzanja la Yehova m’Paradaiso wa padziko lapansi akudzayo. (Chiv. 21:4) Kodi aliyense angafunenso zifukwa zina zabwino ‘zokhalira woyamika’ kwa Mulungu?
3 Mosonyezera Chiyamiko kwa Mulungu: Nthaŵi zonse nkoyenera kufotokoza kuyamikira kwathu m’pemphero kwa Yehova kaamba ka ubwino wake. (Sal. 136:1-3) Timasonkhezeredwanso kusonyeza kumyamikira kwathu m’njira zina zabwino. Mwachitsanzo, ifeyo mosakayika tidzapezekapo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu pa Sande, March 23. Kuti tithandize kukwaniritsa zosoŵa zakuthupi za mpingo wathu ndi ntchito ya padziko lonse ‘timalemekeza Yehova ndi chuma chathu’ mosangalala. (Miy. 3:9) Akulu timawachirikizadi ndi kugwirizana nawo, choncho kusonyeza kuyamikira kwathu Yehova pa thandizo limene amapereka kudzera mwa iwo. (1 Ates. 5:12, 13) Tsiku lililonse, timayesetsa kukhalabe ndi khalidwe loongoka limene limalemekeza dzina la Mulungu. (1 Pet. 2:12) Yehova amakondwera nawo umboni wonsewu wa kuyamikira kwathu.—1 Ates. 5:18.
4 Chisonyezero Chathu Chabwino Koposa cha Kuyamikira: Kukhala ndi phande ndi mtima wonse m’ntchito yolalikira Ufumu, kulemekeza dzina la Yehova, kumthokoza m’pemphero, ndi kuchirikiza choonadi mokhulupirika ndi zina za zisonyezero zabwino koposa za kuyamikira kochokera mumtima kumene tingachite kwa Mlengi wathu kaamba ka zonse zimene watichitira. Yehova amasangalala kutiona tikumchitira utumiki wopatulika mochirikiza chifuniro chake chakuti ‘anthu onse apulumuke.’ (1 Tim. 2:3, 4) Ndiye chifukwa chake ofalitsa ambiri amene angathe kutero akulabadira pempho limene linatuluka mu Utumiki Wathu Waufumu wa February la kulembetsa upainiya wothandiza m’mwezi umodzi kapena yoposapo m’miyezi ya March, April, ndi May. Kuyesetsa mwapadera mu utumiki kuli njira yabwino ‘yokhalira oyamika’ kwa Mulungu. Kodi mudzatha kuloŵa nawo upainiya m’April? m’May?
5 Tapatsidwa chiyembekezo chotsimikizika cha kukhala ndi moyo kosatha. Pamene tidzachiona chitakwaniritsidwa, tidzakhalanso ndi zifukwa zina zambirimbiri tsiku ndi tsiku zopitirizira kuyamikira Yehova mosangalala.—Sal. 79:13.