Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/08 tsamba 1
  • “Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Khalani Oyamikira’
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Dzisonyezeni Inueni Kukhala Akuyamika”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Khalani Akuyamika”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Kodi Mumayamikira?
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 4/08 tsamba 1

“Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”

1 Yesu atachiritsa anthu akhate khumi, mmodzi yekha ndi amene anabwerera kudzamuthokoza. Yesu anati: “Amene ayeretsedwa si khumi kodi? Nanga ena asanu ndi anayi ali kuti?” (Luka 17:11-19) Timafunika kusonyeza kuti timayamikira mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro umene tapatsidwa ndi Atate wathu wowolowa manja ndi wachikondi, Yehova Mulungu.—Akol. 3:15; Yak. 1:17.

2 Kodi zina mwa zinthu zimene tiyenera kuyamikira ndi ziti? Timayamikira dipo, limene ndi mphatso yaikulu imene Mulungu anapereka kwa anthu. (Yoh. 3:16) Timayamikiranso Yehova chifukwa chotikokera kwa iye. (Yoh. 6:44) Chifukwa china chokhalira oyamikira ndi umodzi wathu wachikhristu. (Sal. 133:1-3) N’zachidziwikire kuti tingaganizirenso mphatso zina zambiri zochokera kwa Yehova. Sitifuna kukhala ngati Aisiraeli osayamika amene anaiwala zimene Yehova anawachitira.—Sal. 106:12, 13.

3 Sonyezani Kuyamikira: N’kutheka kuti anthu akhate khumi onse aja anayamikira zimene Yesu anawachitira, koma mmodzi yekha ndiye anasonyeza kuti akuyamikira. (Luka 17:15) Mofanana ndi zimenezi, timasonyeza kuyamikira tikamalalikira mwachangu. Ngati timayamikiradi zimene Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi watichitira, tingalimbikitsidwe kutsanzira chikondi ndi kuwolowa manja kwake mwa kuuza ena za iye. (Luka 6:45) Tikamauza ena za ‘zodabwitsa . . . ndi zolingirira [za Yehova] pa ife,’ timam’konda ndi kumuyamikira kwambiri.—Sal. 40:5.

4 Limbikitsani Ena Kukhala Oyamikira: Tiyenera kukhala tcheru kuti tithandize ana athu ndi anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti akhale oyamikira. Makolo ali ndi mipata yambiri yochitira zimenezi. Mwachitsanzo, angachite zimenezi pamene akusangalala ndi chilengedwe cha Yehova limodzi ndi ana awo. (Aroma 1:20) Tikamachititsa phunziro la Baibulo, mwina tingafunse wophunzira wathu kuti, “Kodi zimenezi zimatiuza chiyani za Yehova?” Wophunzirayo akayamba kuyamikira kwambiri, amayambanso kukonda kwambiri Mulungu ndipo amafunitsitsa kum’sangalatsa.

5 M’masiku otsiriza ano, anthu ambiri ndi osayamika. (2 Tim. 3:1, 2) Mosakayikira, Yehova amasangalala kwambiri kuona atumiki ake odzipereka akusonyeza kuyamikira mwa kugwira mwachangu ntchito yolalikira.—Yak. 1:22-25.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena