Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda
1 Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova ndicho chiŵiya chachikulu cha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” chotipatsiramo chakudya chauzimu “panthaŵi yake.” (Mat. 24:45) Mkulu amene amachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ali ndi udindo wofunika kwambiri monga mphunzitsi wodziŵa amene amapereka chitsanzo chabwino pamoyo wachikristu.—Aroma 12:7; Yak. 3:1.
2 Kuti aphunzitse mogwira mtima, wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ayenera kukonzekera zolimba mlungu uliwonse. Amatero mwapemphero ndi mosamalitsa. Amayesayesa kutifika pamtima ndi nkhani yomwe tikuphunzira kusonyeza kuti ali ndi chidwi ndi anthu m’mpingo. Amasumika malingaliro pamfundo zazikulu m’phunzirolo ndipo amatithandiza kuona mmene zikugwirizanira ndi mutu wa nkhaniyo.
3 Amakonzekera mosamalitsa, zimene zimaphatikizapo kuŵerenga malemba pasadakhale kuti aone mmene akugwirira ntchito. Amaika Mawu a Mulungu patsogolo mwa kulimbikitsa mpingo kugwiritsa ntchito bwino Baibulo pamene akuphunzira. Ngati anthu oyankha sakutchula mfundo yofunika kapena ngati sakusonyeza mmene lemba lalikulu pandimepo likugwirira ntchito, iye amafunsa funso lolunjika lowonjezera kuti chidziŵitsocho chitulutsidwe. Mwa njirayi, amatithandiza kudziŵa zenizeni ndi kudziŵanso mmene tingagwiritsire ntchito zimene tikuphunzira pamoyo wathu.
4 Wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda nthaŵi zonse amayesa kupititsa patsogolo luso lake la kuphunzitsa. Salankhulapo kwambiri, koma amalimbikitsa ifeyo kuti tiziyankha—m’mawu athuathu, mwachidule, ndi molunjika. Nthaŵi zina angamatikumbutse kuti munthu woyamba kuyankha pandime ayenera kuyankha funso losindikizidwalo mwachidule ndi molunjika. Mayankho owonjezereka a omvetsera angakhudze mmene lemba likugwirira ntchito, ndemanga zochirikiza mfundoyo, kapena mmene nkhaniyo tingaigwiritsire ntchito. Mwa kulimbikitsa kukonzekera kwa umwini ndi kwa banja, wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda amasonkhezera chikhumbo cha aliyense chofuna kuyankhapo.
5 Monga ‘ophunzitsidwa ndi Yehova,’ timayamikira “mphatso mwa amuna,” monga ngati ochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda, amene ‘amachititsa . . . m’chiphunzitso.’—Yes. 54:13; Aef. 4:8, 11, NW; 1 Tim. 5:17.