Mmene Banja Limachitira Zinthu Pamodzi Kuti Onse Azitengamo Mbali Mokwanira—Mu Utumiki
1 N’chiyaninso chingakhale chosangalatsa koposa kuona amuna ndi akazi awo, makolo ndi ana akugwira ntchito pamodzi mu utumiki wachikristu, akumatamanda dzina la Yehova poyera? (Sal. 148:12, 13) Mabanja onse ayenera kukhala ndi chizoloŵezi chabwino chotengamo mbali mu utumiki wakumunda nthaŵi zonse. Kodi banja lanu lili ndi tsiku pamlungu limene limapita mu utumiki wakumunda? Ngati ndi choncho, ndiye kuti aliyense amadziŵa bwino zimene ayenera kuchita kuti atengemo mbali mokwanira.—Miy. 21:5a.
2 Musanafike tsiku limene banja lanu limapita ku ulaliki, bwanji osakonzekera pamodzi maulaliki amene banja lanu likagwiritse ntchito? Nthaŵi yokonzekera ingakhale yothandiza kwambiri ndipo ingabweretse mzimu weniweni wogwirizana m’banja. N’kopindulitsadi pamene utumiki wakumunda uchitidwa ndi banja ndipo ngati onse m’banjamo akonzekera bwino!
3 Woyang’anira woyendayenda wina anapita ndi anthu onse a banja lina mu utumiki wa magazini. Pamene anali kupita kunyumba ndi nyumba ndi mmodzi mwa ana a akazi, mwanayo anafunsa woyang’anirayo kuti: “Kodi mudzayenda ndi ine kufikira nthaŵi yanji?” Ndiyeno anafotokoza kuti adzayenda ndi atate ake akamaliza kuyenda ndi woyang’anirayo. Zinali zoonekeratu kuti iye ndi atate ake anasangalala nawo utumiki. Ndithudi ndi mzimu wabwino kwambiri wochita zinthu monga banja!
4 Mabanja ena angakhoze kuchita upainiya pamodzi kwa mwezi umodzi pachaka. Kapena kungakhale kotheka kuti wina m’banjamo azichita upainiya wothandiza nthaŵi zonse kapena kulembetsa upainiya wokhazikika. Mwa kulinganiza zinthu bwino ndi kugwirizana, mwina onse m’banjamo angawonjezere mbali yawo mu utumiki, mwa kuchirikiza yemwe akuchita upainiyayo. Ndithudi banjalo lidzadalitsidwa ndi ntchito yowonjezereka imeneyi komanso ndi zokumana nazo za mu utumiki.—Mal. 3:10.
5 Kutengamo mbali mokwanira m’ntchito yolalikira kudzathandiza mabanja kukhala ogwirizana, achangu, obala zipatso, ndi osangalala mu utumiki wa Yehova!—Yerekezerani ndi Afilipi 2:1, 2.