Pologalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Pologalamu ya tsiku la msonkhano wapadera imene idzayamba mu September 1999 ili ndi mutu wakuti: “Kusanthula Zakuya za Mulungu.” (1 Akor. 2:10) Ndi zinthu zofunika kwambiri ziti zimene tikaphunzire?
Pakufufuza kwawo chidziŵitso, anthu ambiri satsitsimulidwa ndi zimene amapeza. Baibulo limatipatsa mphamvu, monga mmene zikasonyezedwere ndi woyang’anira dera pankhani yake yakuti “Kusanthula Mawu a Mulungu Kumatsitsimula.” Mlendo adzagwirizanitsa kusanthula zakuya za Mulungu ndi kulalikira uthenga wabwino pamene akukamba nkhani yakuti “Kodi Mumaiona Motani Ntchito Yolalikira Ufumu?”
Ndi motani mmene makolo angathandizire ana awo kukumba mwakuya m’Mawu a Mulungu? Malingaliro othandiza adzaperekedwa pankhani yakuti “Khomerezani Mawu a Mulungu mwa Ana Anu.” Akristu achinyamata amalimbikitsidwa m’njira yabwino mwa kuyanjana ndi anthu achikulire mwauzimu mu mpingo. Zitsanzo za mmene amalimbikitsidwira zidzagogomezeredwa pankhani yakuti “Achinyamata Amene Amaphunzira kwa Achikulire.”
N’chifukwa chiyani tiyenera kusanthula mwakhama chuma chobisika chauzimu panthaŵi ino? Yehova ndi Wovumbula zinsinsi. Mlendo adzafotokoza zimene Yehova anavumbula m’nthaŵi zakale ndi zimene akuvumbula nthaŵi zamakono pankhani yake yakuti “Yehova Amavumbula Pang’onopang’ono Zinthu Zakuya.” Izi zidzalimbitsa chosankha chathu chopitirizabe “kusanthula zakuya za Mulungu.”
Konzekerani tsopano lino kukapezekapo. Awo amene akufuna kukasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova mwa kubatizidwa ayenera kuuza woyang’anira wotsogoza mofulumira. Chikhumbo chathu chofuna kusanthula mosamala kwambiri Mawu a Mulungu chidzalimbikitsidwa ndi zimene tikamve. Choncho osaphonya tsiku lapadera la malangizo auzimu limeneli!