Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Mutu wa pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera wachaka chautumiki chatsopano uli ndi maziko enieni a m’Malemba: “Gonjerani Mulungu—Kanizani Mdyerekezi.” (Yak. 4:7) Ndi langizotu lamphamvu m’nthaŵi zovuta zino! Kumvera Mulungu kumatiika paudani ndi Satana. Pulogalamuyi idzatithandiza momwe tingalimbire mtima kukana njira za Mdyerekezi zowononga chikhulupiriro. Kodi china mwa chuma chauzimu chimene tikamve kumsonkhano umenewu n’chiti?
Woyang’anira dera adzasonyeza momwe “Kugonjera Mulungu Monga Anthu Okhala m’Banja” kumalimbitsira mabanja kupirira mavuto a dzikoli. Pa tsikuli nkhani yoyamba ya mlendo yamutu wakuti, “Tanthauzo la Kukaniza Mdyerekezi,” idzafotokoza chifukwa chake tifunika kulimba mtima kukana zolinga za Satana zofuna kuwononga uzimu wathu ndiponso mmene tingachitire zimenezi. Nkhani ziŵiri ndi zokhudza kwambiri achinyamata, amene ayeneranso kuchenjera ndi misampha ya Mdyerekezi. Akristu ambiri amene panopo ali achikulire anakana kutsatira zofuna za dziko ali achinyamata. Tikasangalala kumva zina mwa zimene akumana nazo.
Anthu onse afunika kugonjera olamulira. Choncho, nkhani yomaliza ya mlendo idzagogomezera mbali zinayi zimene tikufunika kusonyeza kugonjera Mulungu: (1) kwa akuluakulu a boma, (2) mu mpingo, (3) pantchito yolembedwa, ndiponso (4) m’banja. Ndi pulogalamu yothandizadi kwambiri!
Amene akufuna kubatizidwa patsiku la msonkhano wapadera limeneli auze woyang’anira wotsogolera mwamsanga. Tonse tiike chizindikiro pakalendala yathu pa tsiku la msonkhanowu ndipo tikonzekere kudzakhalapo papulogalamu yonse. Madalitso amene timalandira sadzatha ngati tigonjera Yehova kwamuyaya.