Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/00 tsamba 3-6
  • Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Chikhulupiriro Cholimba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Chikhulupiriro Cholimba
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula Motsimikiza
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Makolo, Thandizani Ana Anu Kupeza Nzeru Kuti Adzapulumuke
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Musamakayikire Kuti Zimene Mumakhulupirira Ndi Zoona
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 2/00 tsamba 3-6

Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Chikhulupiriro Cholimba

1 Kumayambiriro a zaka za zana loyamba, Yesu Kristu analamula otsatira ake kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mat. 24:14; 28:19, 20) Mboni za Yehova zasamalira kwambiri langizo limeneli moti kumapeto kwa zaka za zana la 20, ubale wathu wachikristu wawonjezeka kuposa ophunzira 5,900,000 m’mayiko 234. Sikukweza kwake mawu otamanda Atate wathu wakumwamba!

2 Tsopano taloŵa m’zaka za zana la 21. Mdani wathu mochenjera amayesetsa kudodometsa ntchito yathu yaikulu yolalikira Ufumu ndi yopanga ophunzira. Amagwiritsa ntchito mavuto a m’dongosolo lino la zinthu kufuna kusokoneza maganizo athu, kutithera nthaŵi yathu, ndiponso kutithera mphamvu zathu chifukwa cha nkhaŵa ndi zinthu zambiri zosafunika. M’malo molekera dongosolo ili kutiuza chimene chili chofunika m’moyo, timatsimikizira tokha mwa Mawu a Mulungu kuti chimene chili chofunika kwambiri ndicho kuchita chifuno cha Yehova. (Aroma 12:2) Zimenezo zikutanthauza kumvera langizo la m’Malemba la ‘kulalikira mawu panthaŵi yake, popanda nthaŵi yake ndi kwaniritsa utumiki wathu.’—2 Tim. 4:2, 5.

3 Khalani ndi Chikhulupiriro Cholimba: Akristu ayenera ‘kuima amphumphu ndi odzazidwa [“chikhulupiriro cholimba,” NW] m’chifuniro chonse cha Mulungu.’ (Akol. 4:12) Panopa liwu lakuti “chikhulupiriro” tanthauzo lake ndilo “malingaliro otsimikiza; kukhala okhutira.” Monga Akristu kodi tiyenera kukhutira kuti mawu aulosi a Mulungu ndi oona ndiponso kuti tsopano tili mkati mwenimweni mwa nthaŵi yamapeto. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha mtumwi Paulo, amene anati uthenga wabwino “uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupira.”—Aroma 1:16.

4 Mdyerekezi amagwiritsa ntchito amuna oipa ndi onyenga, osokeretsedwa, kuti asonkhezere ena ndi kuwasokeretsa. (2 Tim. 3:13) Pochenjezedweratu zimenezi, tiyesetse kulimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti tili ndi choonadi. M’malo molola nkhaŵa za moyo kufooketsa changu chathu, tiyenera kupitiriza kuika zinthu za Ufumu patsogolo. (Mat. 6:33, 34) Komanso sitikufuna kuiŵala za kufulumira kwa nthaŵi, kapena kumaganiza kuti mapeto a dongosolo lino ali kutali. Akuyandikira pafupi kwambiri. (1 Pet. 4:7) Ngakhale tione kuti m’madera ena anthu sakulabadira uthenga wabwino polingalira za umboni umene waperekedwa kale, ntchito yochenjeza iyenera kupitirira.—Ezek. 33:7-9.

5 Mafunso ofunika panthaŵi ino imene yatha kale ndi akuti: ‘Kodi ndimaona lamulo la Yesu lopanga ophunzira kukhala lofunika kwambiri? Polalikira uthenga wabwino, kodi ndimasonyeza chikhulupiriro cholimba chakuti Ufumu ndi weniweni? Kodi ndatsimikiza mtima kuchita nawo utumiki wopulumutsa miyoyo umenewu ku mlingo umene ndingathe?’ Podziŵa pamene tili m’nthaŵi ya mapeto, tiyenera kudzipenyerera tokha pa lamulo limene tinapatsidwa la kulalikira ndi kuphunzitsa. Pochita zimenezi tidzadzipulumutsa tokha ndi amene amatimvetsera. (1 Tim. 4:16) Kodi ndi motani mmene tonsefe tingalimbitsire chikhulupiriro chathu monga atumiki?

6 Tsanzirani Atesalonika: Mtumwi Paulo, pokumbukira ntchito yaikulu ya abale a ku Tesalonika, anati kwa iwo: ‘Uthenga wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu [“chikhulupiriro cholimba,” NW]; monga mudziŵa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu. Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, mmene mudalandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera.’ (1 Ates. 1:5, 6) Inde, Paulo anayamikira mpingo wa Atesalonika chifukwa chakuti unali kulalikira mwachangu komanso ndi chikhulupiriro cholimba mosasamala kanthu za masautso ambiri amene anali kukumana nawo. Kodi anatha bwanji kuchita zimenezi? Chimene chinawalimbikitsa makamaka chinali changu ndi chikhulupiriro chimene anaona kwa mtumwi Paulo ndi antchito anzake. Kodi zinawalimbikitsa bwanji?

7 Miyoyo ya Paulo ndi anzake amene amayenda naye inatsimikizira kuti mzimu wa Mulungu unali pa iwo ndi kuti anakhulupirira ndi mtima wonse zimene anali kulalikira. Asanafike ku Tesalonika, Paulo ndi Sila anachitidwa chipongwe ku Filipi. Popanda kuzengedwa mlandu, anamenyedwa, kuikidwa m’ndende, ndipo anawamanga m’matangadza. Koma mavuto ameneŵa sanafooketse changu chawo pa uthenga wabwino. Mwa thandizo la Mulungu anatuluka m’ndendemo, komanso woyang’anira ndende ndi banja lake anatembenuka, ndipo njira inatseguka yakuti abale ameneŵa apitirize mu utumiki wawo.—Mac. 16:19-34.

8 Mwa mphamvu ya mzimu wa Mulungu, Paulo anafika ku Tesalonika. Kumeneko anagwira ntchito mwamphamvu kuti apeze zofunika pamoyo wake kwinaku nadzipereka kwambiri kuphunzitsa Atesalonika choonadi. Sanaleke kulalikira uthenga wabwino pa mpata uliwonse. (1 Ates. 2:9) Kulalikira kwa Paulo ndi chikhulupiriro cholimba kunalimbikitsa kwambiri anthu akumeneko kwakuti ena mwa iwo analeka kulambira mafano nakhala atumiki a Mulungu woona, Yehova.—1 Ates. 1:8-10.

9 Chizunzo sichinalepheretse okhulupirira atsopanowo kulalikira uthenga wabwino. Mosonkhezeredwa ndi chikhulupiriro chawo chatsopanocho ndiponso kukhutira kwambiri kuti adzapeza madalitso ochuluka, Atesalonika anasonkhezereka kulalikira choonadi chimene anachilandira mokondwera. Mpingo umenewo unakhala wokangalika kwakuti uthenga wa chikhulupiriro ndi changu chawo unafalikira mbali zina za Makedoniya ngakhale m’Akaya. Choncho, pamene Paulo amalemba kalata kwa Atesalonika, ntchito zawo zabwinozo zinali kudziŵika kale bwino lomwe. (1 Ates. 1:7) N’chitsanzo chabwino bwanji!

10 Kusonkhezeredwa ndi Kukonda Mulungu ndi Anthu: Kodi m’motani mmene ifeyo lerolino tingakhalire ndi chikhulupiriro cholimba polalikira uthenga wabwino monga Atesalonika? Za iwo Paulo analemba kuti: ‘Tikukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita.’ (1 Ates. 1:3) N’zodziŵikiratu kuti anali kukonda kwambiri Yehova Mulungu ndi anthu amene anawalalikira. Chinali chikondi chomwecho chimene chinam’sonkhezera Paulo ndi anzake kupereka kwa Atesalonika ‘osati uthenga wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo [wawo].’—1 Ates. 2:8.

11 Mofananamo, kukonda kwathu kwambiri Yehova ndi anthu anzathu kumatisonkhezera kufuna kuchita nawo mokwanira ntchito yolalikira imene Mulungu watipatsa kuti tichite. Ndi chikondi chimenechi, timazindikira kuti kulengeza uthenga wabwino ndi ntchito yathu imene Mulungu watipatsa. Mwa kusinkhasinkha moyamikira zinthu zonse zimene Yehova watichitira kutitsogolera ku “moyo weniweniwo” kumatisonkhezera kuuza ena choonadi chosangalatsa chimodzimodzichi chomwe timakhulupirira ndi mtima wathu wonse.—1 Tim. 6:19.

12 Potangwanika m’ntchito yolalikira, chikondi chathu pa Yehova ndi anthu chidzapitirira kukula. Chikatero, tidzasonkhezereka kuchita zochuluka mu utumiki wa kukhomo ndi khomo ndiponso kuchita nawo mitundu ina yonse ya maulaliki amene alipo. Tidzagwiritsa ntchito mwayi wochitira umboni mwamwayi kwa achibale, anansi, ndi mabwenzi. Ngakhale anthu ambiri akane uthenga wabwino umene timawauza ndiponso ngakhale ena ayese kudodometsa ntchito yolengeza Ufumu, timakhala ndi chimwemwe mu mtima. Chifukwa chiyani? Chifukwa timadziŵa kuti tachita mbali yathu kuchitira umboni za Ufumu ndi kuthandiza anthu kupeza chipulumutso. Ndipo Yehova adzadalitsa khama lathu lofuna anthu owongoka mtima. Ngakhale pamene tili pamavuto a m’moyo ndiponso pamene Satana akufuna kutilanda chimwemwe chathu, timathabe kukhala olimba m’chikhulupiriro chathu ndiponso timakhalabe achangu pochitira ena umboni. Pamene tonse tichita mbali yathu, mipingo imakhala yolimba komanso yachangu monga umene unali ku Tesalonika.

13 Musasiye Poyesedwa: Chikhulupiriro n’chofunikanso pamene tikumana ndi ziyeso zosiyanasiyana. (1 Pet. 1:6, 7) Yesu anauza ophunzira ake momveka bwino kuti ngati am’tsatira iye, ‘anthu a mitundu yonse adzadana nawo.’ (Mat. 24:9) Paulo ndi Sila anakumana ndi zimenezi ku Filipi. Nkhani ya m’Machitidwe chaputala 16 imati Paulo ndi Sila anaikidwa m’chipinda cha mkati mwa ndende ndipo anawamanga m’matangadza. Nthaŵi zambiri, ndende yaikulu inali bwalo, ndipo m’mphepete mwake munali zipinda za ndende zoŵala komanso zoloŵa mpweya. Koma ndende ya mkatikati inali ya mdima ndiponso munali kufika mpweya wochepa kwambiri. Paulo ndi Sila anali m’ndende yoipa yamdima, yotentha, ndiponso yonunkha imeneyi. Tangolingalirani kupweteka kumene anali kumva ali m’matangadza kwa maola ambiri, misana yawo ili yomyuka komanso ikutuluka magazi chifukwa chokwapulidwa!

14 Mosasamala kanthu za ziyeso zimenezi, Paulo ndi Sila anakhulupirikabe. Anasonyeza kulimba mtima kumene kunawalimbikitsa kutumikira Yehova mosasamala kanthu za chiyeso. Chikhulupiriro chawo chikugogomezedwa m’vesi 25 la chaputala 16 pamene akuti Paulo ndi Sila “analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo.” Ndiponso, ngakhale anali m’ndende ya mkatikati, anakhulupiriradi kuti anali ndi chiyanjo cha Mulungu kwakuti anaimba mokweza mpaka andende ena kumamva! Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chofananacho lerolino pamene tikuyesedwa.

15 Ziyeso zimene Mdyerekezi amabweretsa pa ife n’zambiri zedi. Kwa ena zingakhale chizunzo cha m’banja. Abale athu ambiri ali m’milandu. Tingatsutsidwe ndi ampatuko. Pali mavuto osoŵa ndalama ndiponso nkhaŵa ya mmene tingapezere zofunika pamoyo. Achinyamata amakumana ndi chisonkhezero cha anzawo kusukulu. Kodi m’motani mmene tingapiririre ziyeso zimenezi bwinobwino? Kodi n’chiyani chimafunika kuti tisonyeze chikhulupiriro?

16 Choyamba komanso choposa zonse, tifunika kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova. Pamene Paulo ndi Sila anali m’ndende ya mkati, sanathere nthaŵi yawo kudandaula za mkhalidwe wawo kapena kudzimvera chisoni. Mofulumira anapita kwa Yehova m’pemphero ndiponso kum’tamanda moimba. Chifukwa chiyani? Chifukwa anali paubwenzi wolimba ndi Atate wawo wakumwamba. Anazindikira kuti anali kuvutika chifukwa cha chilungamo ndi kuti chipulumutso chawo chinali mwa Yehova.—Sal. 3:8.

17 Pamene tikumana ndi ziyeso lerolino, ifenso tiyenera kuyang’ana kwa Yehova. Paulo akutilimbikitsa ife monga Akristu kuti ‘zopempha zathu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yathu ndi maganizo athu mwa Kristu Yesu.’ (Afil. 4:6, 7) Ati kutonthoza kwake nanga kudziŵa kuti Yehova sadzatisiya tokha m’ziyeso! (Yes. 41:10) Amakhala ndi ife nthaŵi zonse malinga ngati tim’tumikira ndi chikhulupiriro chenicheni.—Sal. 46:7.

18 Chithandizo china chofunika posonyeza chikhulupiriro ndi kukhala wotanganidwa mu utumiki wa Yehova. (1 Akor. 15:58) Paulo ndi Sila anaponyedwa m’ndende chifukwa chakuti anali otanganidwa kulalikira uthenga wabwino. Kodi anasiya kulalikira chifukwa cha ziyeso zawo? Ayi, anapitiriza kulalikira ngakhale m’ndende mwenimwenimo, ndipo atatulutsidwa, anapita ku Tesalonika ndipo anapita ku sunagoge wa Ayuda ‘kukanena ndi iwo za m’Malembo.’ (Mac. 17:1-3) Pamene tili ndi malingaliro otsimikiza kwambiri kapena kukhulupirira Yehova ndi kukhutira kuti tili ndi choonadi, palibe chimene ‘chingakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.’—Aroma 8:35-39.

19 Zitsanzo Zamakono za Chikhulupiriro Cholimba: Pali zitsanzo zambiri zapadera m’tsiku lathu, za anthu amene asonyeza chikhulupiriro cholimba monga Paulo ndi Sila. Mlongo wina amene anapulumuka kumsasa wa Auschwitz anafotokoza za chikhulupiriro chosagwedera chimene abale ndi alongo athu kumeneko anasonyeza. Analongosola kuti: “Nthaŵi ina potifunsa, wapolisi anabwera kwa ine atakunga nkhonya. ‘Tichite nanu chiyani anthu inu?’ anakalipa motero. ‘Kukumangani, simudandaula. Kukutsekerani m’ndende, sizikukhudzani m’pang’onong’ono pomwe. Kupita nanu kumsasa wachibalo, simudandaula nazo. Kukuweruzani kuti muphedwa, mumangoti chilili zosakukhudzani. Tichite nanu chiyani?” Si mmene chikhulupiriro chathu chimalimbira kuona kukhulupirika kwa abale athu m’mikhalidwe yovuta ngati imeneyi! Nthaŵi zonse anayang’ana kwa Yehova kuti awathandize kupirira.

20 Ndithudi timakumbukira chikhulupiriro cha abale athu ambiri amene akumana ndi udani wa mafuko umene wafala m’zaka zinozi. Mosasamala kanthu kuti ali m’mikhalidwe yoopsa, abale amaudindo amaonetsetsa kuti abale ndi alongo awo akudyetsedwa mwauzimu. Onse akupitiriza mokhulupirika ali otsimikiza kuti ‘palibe chida chosulidwira iwo chidzapindula.’—Yes. 54:17.

21 Ambiri a abale ndi alongo athu amene ali ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira akusonyezanso chikhulupiriro cholimba ndi chipiriro. Mbale wina ku Guadeloupe anatsutsidwa kwambiri ndi mkazi wake wosakhulupirira. Kuti am’chititse ulesi ndi kum’siyitsa kupezeka pamisonkhano yachikristu, mkazi wakeyo sanali kukonza chakudya kapena kuchapa, kusita, ndi kusoka zovala za mwamuna wakeyo. Kwa nthaŵi yaitali, sanali kumulankhulitsa. Koma mwa kukhulupirika ndi mtima wonse potumikira Yehova komanso kum’pempha thandizo m’pemphero, mbale ameneyu anatha kupirira zonsezo. Kwa utali wotani? Pafupifupi zaka 20 zinapitapo kuti mkazi wake ayambe kusintha mtima wake pang’onopang’ono. Kenako, mwamunayo anasangalaladi chifukwa mkazi wakeyo analandira chiyembekezo cha Ufumu wa Mulungu.

22 Pomaliza, tisaiŵale chikhulupiriro cholimba cha abale ndi alongo athu achinyamata amene amapita kusukulu tsiku lililonse ndipo amalimbana ndi chisonkhezero cha anzawo ndi mavuto ena. Ponena za mavuto ofuna kufanana ndi ena pasukulu, mtsikana wina wa Mboni anati: “Pamene uli kusukulu, nthaŵi zonse aliyense amakulimbikitsa kukhala wopanduka pang’ono. Anyamata ndi atsikana amakulemekeza kwambiri ngati uchita zinthu zopulupudza.” Achinyamata athu amakumana ndi mavuto kwabasi! Ayenera kukhala otsimikiza maganizo ndi mtima kukana chiyeso.

23 Achinyamata athu ambiri akuchita bwino posunga umphumphu wawo mosasamala kanthu za ziyeso. Chitsanzo chimodzi ndi cha mlongo wachitsikana amene amakhala ku France. Tsiku lina atadya chakudya cha masana, anyamata ena anam’kakamiza kuti awapsompsone, koma anapemphera ndipo anakanitsitsa, chotero anyamatawo anam’siya. Kenako, mmodzi mwa anyamatawo anapitanso kwa mtsikana uja n’kumuuza kuti anasirira kulimba kwake mtima. Anam’lalikira mogwira mtima za Ufumu, ndi kumufotokozera miyezo yapamwamba imene Yehova waikira onse ofuna madalitso ake. M’kati mwa nthaŵi ya sukulu, anafotokozanso zikhulupiriro zake kwa kalasi yonse.

24 Tili ndi mwayi wapadera kwambiri kukhala pakati pa awo amene Yehova wafuna kuwagwiritsa ntchito kulankhula ndi chikhulupiriro cholimba za chifuno chake! (Akol. 4:12) Kuphatikiza apo, tili ndi mwayi wapadera kwambiri wosonyeza umphumphu wathu poukiridwa ndi Mdani wathu wonga mkango, Satana Mdyerekezi. (1 Pet. 5:8, 9) Tisaiŵale kuti Yehova akugwiritsa ntchito uthenga wa Ufumu pofuna kupulumutsa ife amene timalalikira ndiponso amene amatimvetsera. Zimene timasankha ndiponso moyo wathu watsiku ndi tsiku zitsimikizetu kuti timaika Ufumu patsogolo. Tiyeni tipitirize kulalikira uthenga wabwino ndi chikhulupiriro cholimba!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena