Timalalikira Uthenga Wabwino
1 Si mwayi wake umene tili nawo kukhala onyamula “uthenga wabwino wa zinthu zabwino!” (Aroma 10:15) Tili ndi uthenga wotsitsimula woti tiuze anthu amene ali m’masautso ndi amene athedwa nzeru. Kodi tingawathandize motani kuzindikira kuti tikulalikira “uthenga wabwino wa zinthu zabwino”?—Yes. 52:7.
2 Konzekerani Uthenga Wogwira Mtima: Makambirano athu mu utumiki adzakhala ndi zotsatira zabwino ngati tigogomezera zinthu zolimbikitsa. Chotero, pokonzekera nkhani za muulaliki wathu ndiponso popenda chofalitsa chimene tikagaŵire, tiyenera kugogomezera mbali zogwira mtima za uthengawo. Mwa kuwauza za chiyembekezo chathu cha m’Baibulo mwa chidaliro komanso ndi mtima wonse, tingayembekezere zotsatira zolimbikitsa.—Miy. 25:11.
3 Ngakhale kuti timamva chisoni pamene anthu afotokoza mmene mikhalidwe ya dziko yoipitsitsayi yawakhudzira, tiyenera kuwasonyeza chothetsera chenicheni cha mavuto a anthu, Ufumu wa Mulungu. Ngakhale pokambirana za “tsiku lakubwezera” la Yehova lomwe likudzalo, tikufuna kusonyeza mmene ameneŵa alilidi “mawu abwino kwa ofatsa.” (Yes. 61:1, 2) Tingawatsimikizire omvetsera athu kuti chilichonse chimene Yehova amachita pamapeto pake chimadzetsa chimwemwe chachikulu ndi zotsatira zabwino kwambiri.
4 Lalikirani Choonadi mwa Chimwemwe Chenicheni: Pamene anthu aona nkhope zathu zachimwemwe ndi kulankhula kwathu motsimikiza, amakhala chire kwambiri kumvetsera. Ngati tisonyeza chidaliro, omvetsera athu adzaona kuti ‘timakondwera m’chiyembekezo.’ (Aroma 12:12) Chotero, akhoza kukhala osavuta kwambiri kumvetsera uthenga wabwino. Ndithudi, tili ndi chifukwa chabwino chosonyezera maganizo abwino ndi achimwemwe nthaŵi zonse m’mbali iliyonse ya utumiki wathu.
5 Monga atumiki a uthenga wabwino, timachita zambiri zoposa kungodziŵitsa. Ulaliki wathu umapereka chiyembekezo chodalirika cha moyo wabwino pakalipano komanso m’tsogolo. (1 Tim. 4:8) Pofikira munthu aliyense, malingaliro athu abwino adzaonekera m’zimene tidzanena ndipo adzathandiza anthu kulandira uthenga wabwino. Tiyeni tilimbikitse oongoka mtima kulandira uthenga wabwino wosangalatsa umene timalalikira mwa kusamalira zimene timanena ndi mmene tikuzinenera!